31 Tinalumbira kuti anthu amʼdzikolo akabwera kudzagulitsa katundu ndi mbewu zamtundu uliwonse pa tsiku la Sabata,+ sitidzawagula chilichonse pa Sabata kapena pa tsiku lililonse lopatulika.+ Tinalumbiranso kuti sitizilima minda yathu mʼchaka cha 7+ ndipo tizikhululuka ngongole zonse.+