9 Iwo adzabwera akulira.+
Ndidzawatsogolera akadzandipempha kuti ndiwakomere mtima.
Ndidzawatsogolera kumitsinje ya madzi,+
Ndipo ndidzawayendetsa mʼnjira yabwino imene sadzapunthwa.
Chifukwa ine ndine Bambo ake a Isiraeli ndipo Efuraimu ndi mwana wanga woyamba kubadwa.”+