9 Isimaeli anaponya mitembo yonse ya amuna amene anawapha mʼchitsime chachikulu kwambiri. Mfumu Asa ndi imene inakumba chitsime chimenechi pamene Basa mfumu ya Isiraeli+ inamuopseza. Chitsime chimenechi ndi chimene Isimaeli mwana wa Netaniya anaponyamo mitembo ya anthu amene anawapha.