2 mʼchaka choyamba cha ulamuliro wake, ineyo Danieli ndinazindikira chiwerengero cha zaka zimene zinatchulidwa mʼmawu amene Yehova anauza mneneri Yeremiya, kuti Yerusalemu adzakhala bwinja+ kwa zaka 70.+ Ndinazindikira zimenezi nditawerenga mʼmabuku.