16 Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera. Chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu, Yerusalemu komanso anthu anu, tikunyozedwa ndi anthu onse otizungulira.+