58 Mwachitsanzo, ukamapita ndi munthu amene akukuimba mlandu kwa wolamulira, muli mʼnjira udziyesetsa kuchitapo kanthu kuti uthetse mlanduwo. Uzichita zimenezi kuti asakutengere kwa woweruza, woweruzayo nʼkukupereka kwa msilikali wapakhoti, msilikaliyo nʼkukuponya mʼndende.+