18 kuti ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mumdima+ nʼkuwapititsa kowala+ ndiponso kuwachotsa mʼmanja mwa Satana+ nʼkuwapititsa kwa Mulungu. Ukachite zimenezi kuti machimo awo akhululukidwe+ nʼkulandira cholowa pamodzi ndi oyeretsedwa chifukwa chondikhulupirira.’