16 pamenepo ine ndidzakuchitani zotsatirazi: pokulangani ndidzakugwetserani zoopsa za chifuwa chachikulu+ ndi kuphwanya kwa thupi koopsa, kumene kudzachititsa maso anu khungu+ ndi kukufooketsani.+ Simudzapindula ndi mbewu zimene mwafesa, chifukwa adani anu adzadya zokolola zanuzo.+