14 Akatero, aziikaponso ziwiya zonse zimene amachitira utumiki paguwapo nthawi zonse. Aziikapo zoikamo phulusa la zingwe za nyale, mafoloko aakulu, mafosholo, mbale zolowa, ndi ziwiya zonse za paguwa lansembe.+ Ndiyeno aziziphimba ndi zikopa za akatumbu, n’kubwezeretsa mitengo yake yonyamulira.+