18 Ndipo uuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse pokonzekera tsiku lamawa,+ pakuti mudya nyama. Paja mwakhala mukulirira Yehova,+ kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye? Ku Iguputo zinthu zinali kutiyendera bwino.”+ Nyamayo Yehova akupatsani ndithu, ndipo muidyadi.+