5 Davide anayankha wansembeyo kuti: “Koma akazi sanatiyandikire monga mmene zinakhaliranso poyamba pamene ndinapita kukamenya nkhondo.+ Anyamatawo amakhala oyera ngakhale pamene tili pa ntchito wamba. Ndiye kuli bwanji lero pamene tili pa ntchito yapadera?”