21 Pakuti pali munthu amene ntchito yake yovuta waigwira mwanzeru, mozindikira ndiponso waigwira bwino.+ Koma zonse zimene anapeza zidzaperekedwa kwa munthu amene sanagwire mwakhama ntchito ngati imeneyo.+ Zimenezinso n’zachabechabe ndipo n’zomvetsa chisoni kwambiri.+