Mlaliki
2 Ine ndinadziuza mumtima mwanga+ kuti: “Ndiyesereko kusangalala.+ Komanso ndisangalale ndi zinthu zabwino.”+ Ndipo ndinaona kuti zimenezonso zinali zachabechabe. 2 Ndinauza kuseka kuti: “Ndiwe wamisala!”+ ndipo kusangalala+ ndinakuuza kuti: “Uli ndi phindu lanji?”
3 Ndinafufuza ndi mtima wanga wonse kuti ndidziwe uchitsiru posangalatsa thupi langa ndi vinyo,+ pamene ndinali kutsogolera mtima wanga ndi nzeru.+ Ndinachita zimenezi kuti ndione ubwino umene ana a anthu amapeza pa zimene amachita padziko lapansi pano masiku onse a moyo wawo.+ 4 Ndinachita zinthu zikuluzikulu.+ Ndinadzimangira nyumba zambirimbiri.+ Ndinalima minda ya mpesa yambirimbiri.+ 5 Ndinadzipangira minda yokongola ndi malo obzalamo maluwa ndi mitengo.+ Mmenemu ndinabzalamo mitengo ya zipatso zosiyanasiyana. 6 Ndinadzipangira madamu a madzi+ kuti ndizithirira mitengo imene inali kumera m’nkhalango yanga.+ 7 Ndinali ndi antchito aamuna ndi aakazi.+ Ndinalinso ndi antchito obadwira m’nyumba mwanga.+ Komanso, ndinali ndi ziweto zochuluka zedi, ng’ombe ndi nkhosa. Ziwetozo zinali zambiri kuposa za onse amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo.+ 8 Ndinapezanso siliva ndi golide wambiri,+ ndi chuma chimene chimakhala ndi mafumu ndiponso chimene chimapezeka m’zigawo za dziko.+ Ndinali ndi oimba aamuna ndi aakazi.+ Ndinalinso ndi akazi ambiri,+ omwe amasangalatsa mtima+ wa amuna. 9 Ndinali ndi zinthu zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo.+ Komanso ndinali kuchitabe zinthu mwanzeru.+
10 Chilichonse chimene maso anga anali kupempha sindinali kuwamana.+ Mtima wanga sindinaumane chosangalatsa cha mtundu uliwonse. Ndinasangalalanso ndi ntchito yonse imene ndinaigwira mwakhama.+ Imeneyi ndiyo inali mphoto yanga ya ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama.+ 11 Ineyo ndinaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira ndiponso ntchito yovuta imene ndinachita khama kuti ndiikwanitse.+ Nditatero, ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe ndipo kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ Padziko lapansi pano panalibe chaphindu chilichonse.+
12 Ineyo ndinaganizaganiza kuti nzeru n’chiyani,+ misala n’chiyani, ndipo uchitsiru n’chiyani.+ Kodi munthu wochokera kufumbi amene wabwera pambuyo pa mfumu angachite chiyani? Zimene angachite n’zimene anthu ena anachita kale. 13 Ndinaona kuti nzeru zili ndi phindu lalikulu kuposa uchitsiru+ monga mmene kuwala kulili ndi phindu lalikulu kuposa mdima.+
14 Aliyense wanzeru maso ake amaona bwino,+ koma wopusa amangoyendabe mu mdima waukulu.+ Ineyo ndazindikira kuti onsewa mapeto awo ndi amodzi.+ 15 Ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Mapeto ngati a munthu wopusa+ adzagweranso ineyo ndithu.”+ Choncho kodi ineyo ndinavutikiranji kukhala wanzeru kwambiri+ pa nthawi imene ija? Ndipo ndinanena mumtima mwanga kuti: “Izinso n’zachabechabe.” 16 Pakuti munthu wanzeru, mofanana ndi wopusa, sadzakumbukiridwa mpaka kalekale.+ M’masiku amene akubwerawa aliyense adzaiwalidwa. Ndipo kodi wanzeru adzafa motani? Adzafa mofanana ndi wopusa.+
17 Ine ndinadana ndi moyo+ chifukwa ndinaona kuti ntchito imene yachitidwa padziko lapansi pano ndi yosautsa mtima.+ Pakuti zonse zinali zachabechabe ndipo kuchita zimenezi kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ 18 Ineyo ndinadana ndi ntchito yonse yovuta imene ndinali kugwira padziko lapansi pano,+ imene ndidzasiyire munthu amene akubwera pambuyo panga.+ 19 Ndipo kodi ndani angadziwe kuti kaya adzakhala wanzeru kapena wopusa?+ Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinazipeza movutikira ndiponso zimene ndinazichita mwanzeru padziko lapansi pano.+ Zimenezinso n’zachabechabe. 20 Ineyo ndinayamba kutaya mtima+ poganizira ntchito yanga yonse yovuta imene ndinaigwira mwakhama padziko lapansi pano. 21 Pakuti pali munthu amene ntchito yake yovuta waigwira mwanzeru, mozindikira ndiponso waigwira bwino.+ Koma zonse zimene anapeza zidzaperekedwa kwa munthu amene sanagwire mwakhama ntchito ngati imeneyo.+ Zimenezinso n’zachabechabe ndipo n’zomvetsa chisoni kwambiri.+
22 Pakuti munthu amapeza chiyani pa ntchito yonse imene waigwira mwakhama, ndiponso imene wasautsika nayo mtima poigwira padziko lapansi pano?+ 23 Masiku ake onse, ntchito yakeyo imamubweretsera zowawa ndi zokhumudwitsa.+ Komanso usiku mtima wake sugona.+ Izinso n’zachabechabe.
24 Kwa munthu, palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.+ Ineyo ndaona kuti zimenezinso n’zochokera m’dzanja la Mulungu woona.+ 25 Pakuti ndani amadya+ bwino ndi kumwa zabwino kuposa ine?+
26 Munthu wabwino pamaso pa Mulungu,+ Mulunguyo amam’patsa nzeru, kudziwa zinthu, ndi kusangalala.+ Koma wochimwa amam’patsa ntchito yotuta ndi kusonkhanitsa zinthu kuti azipereke kwa munthu amene ali wabwino pamaso pa Mulungu woona.+ Zimenezinso n’zachabechabe ndipo kuli ngati kuthamangitsa mphepo.+