5 Komanso uzidzaopa chimene chili pamwamba ndipo m’njira mudzakhala zoopsa. Mtengo wa amondi udzachita maluwa,+ chiwala chizidzayenda mochita kudzikoka ndipo zakudya sizidzakoma, popeza munthu adzakhala akupita kunyumba yake yokhalitsa+ ndipo olira azidzazungulira mumsewu.+