Mlaliki
12 Kumbukira Mlengi wako Wamkulu+ masiku a unyamata wako,+ asanafike masiku oipa+ komanso zisanafike zaka zimene udzati: “Moyo sukundisangalatsa.”+ 2 Uchite zimenezi kuwala kwa dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi kusanazime,+ ndiponso mitambo isanabwerere kuti igwetse mvula. 3 Pa nthawi imeneyo oyang’anira nyumba+ azidzanjenjemera, amuna amphamvu adzapindika,+ akazi opera ufa+ adzasiya kugwira ntchito chifukwa adzatsala ochepa, akazi oyang’ana pawindo+ azidzaona mdima, 4 zitseko zotulukira popita mumsewu zidzatsekedwa,+ phokoso la miyala yoperera ufa lidzayamba kumveka motsika,+ ndipo munthu azidzadzuka ndi kulira kwa mbalame, ndiponso ana onse aakazi azidzaimba nyimbo ndi mawu otsika.+ 5 Komanso uzidzaopa chimene chili pamwamba ndipo m’njira mudzakhala zoopsa. Mtengo wa amondi udzachita maluwa,+ chiwala chizidzayenda mochita kudzikoka ndipo zakudya sizidzakoma,* popeza munthu adzakhala akupita kunyumba yake yokhalitsa+ ndipo olira azidzazungulira mumsewu.+ 6 Umukumbukire, chingwe chasiliva chisanachotsedwe, mbale yagolide isanaphwanyidwe,+ mtsuko usanaphwanyike pakasupe, ndiponso wilo lotungira madzi pachitsime lisanathyoke. 7 Kenako fumbi lidzabwerera kunthaka+ kumene linali, ndipo mzimu*+ udzabwerera kwa Mulungu woona+ amene anaupereka.+
8 Wosonkhanitsa+ anati: “Zachabechabe! Zinthu zonse n’zachabechabe.”+
9 Kuwonjezera pa kukhala ndi nzeru,+ wosonkhanitsayo nthawi zonse anali kuphunzitsanso anthuwo kuti adziwe zinthu.+ Anali kusinkhasinkha ndi kufufuza zinthu mosamala,+ ndipo analemba miyambi yambiri m’ndondomeko yoyenera.+ 10 Wosonkhanitsayo anafufuza mawu okoma+ ndipo analemba mawu olondola a choonadi.+
11 Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga zobayira ng’ombe pozitsogolera,+ ndipo anthu amene amadzipereka kusonkhanitsa mawu anzeru, ali ngati misomali yokhomerera kwambiri.+ Mawuwo aperekedwa ndi m’busa mmodzi.+ 12 Mwana wanga, ponena za chilichonse chowonjezera pa izi, ndikukuchenjeza kuti: Kupanga mabuku ambiri sikudzatha ndipo kuwawerenga kwambiri kumangotopetsa munthu.+
13 Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita. 14 Pakuti Mulungu woona adzaweruza ntchito iliyonse ndiponso chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati zili zabwino kapena zoipa.+