12 Kenako, anayamba kulankhula nawo m’mafanizo kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ ndi kumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa, ndi kumanga nsanja.+ Atatero anausiya m’manja mwa alimi+ n’kupita kudziko lina.+