Maliko
12 Kenako, anayamba kulankhula nawo m’mafanizo kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ ndi kumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa, ndi kumanga nsanja.+ Atatero anausiya m’manja mwa alimi+ n’kupita kudziko lina.+ 2 Tsopano nyengo ya zipatso itakwana, iye anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akam’patseko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo.+ 3 Koma iwo anam’gwira, n’kumumenya ndi kum’bweza chimanjamanja.+ 4 Iye anatumizanso kapolo wina kwa iwo koma ameneyu anamutema m’mutu ndi kumuchitira zachipongwe.+ 5 Anatumizanso wina, koma ameneyo anamupha. Ndiyeno anatumizanso akapolo ena ambiri. Ena mwa iwo anawamenya ndipo ena anawapha. 6 Tsopano anatsala ndi mmodzi yekha, mwana wake wokondedwa.+ Anatumizanso mwanayo kwa iwo ngati wotsirizira, n’kunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’+ 7 Koma alimiwo anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’+ 8 Choncho anamugwira n’kumupha,+ ndipo anamuponya kunja kwa munda wa mpesawo.+ 9 Kodi mwinimunda wa mpesawo adzachita chiyani? Adzabwera ndi kupha alimiwo, ndipo munda wa mpesawo+ adzaupereka kwa ena.+ 10 Kodi simunawerengepo lemba limene limati, ‘Mwala+ umene omanga nyumba anaukana, umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri’?+ 11 Kodi simunawerenge kuti ‘Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’?”+
12 Atamva zimenezo anayamba kufunafuna njira yomugwirira, koma anaopa khamu la anthu, pakuti iwo anazindikira kuti iye ananena fanizolo akuganiza za iwowo. Choncho anangomusiya n’kuchokapo.+
13 Pambuyo pake anam’tumizira ena mwa Afarisi ndi a chipani cha Herode,+ kuti akam’kole m’mawu ake.+ 14 Atafika, iwo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo simusamala kuti uyu ndani, chifukwa simuyang’ana maonekedwe a munthu, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi:+ Kodi n’kololeka kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi tizipereka kapena tisamapereke?”+ Pozindikira chinyengo chawo, Yesu anawafunsa kuti: “Bwanji mukundiyesa? Bweretsani khobidi la dinari kuno ndilione.”+ 16 Iwo anam’patsadi. Ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi chifaniziro ichi ndi mawu akewa n’zandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.”+ 17 Pamenepo Yesu anati: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu.”+ Ndipo iwo anadabwa naye kwambiri.+
18 Kenako Asaduki amene amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa iye ndipo anam’funsa kuti:+ 19 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti ngati munthu wamwalira ndi kusiya mkazi koma osasiya mwana, m’bale wake+ atenge mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana mwa mkaziyo.+ 20 Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma pomwalira, sanasiye mwana aliyense.+ 21 Wachiwiri anatenga mkaziyo, koma nayenso anamwalira osasiya mwana. Zimenezi zinachitikanso chimodzimodzi kwa wachitatu. 22 Ndipo onse 7 aja sanasiye mwana. Pamapeto pake mkazi nayenso anamwalira.+ 23 Kodi pouka kwa akufa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anam’kwatira.”+ 24 Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu?+ 25 Akadzauka kwa akufa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba.+ 26 Koma zakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge m’buku la Mose, m’nkhani ya chitsamba chaminga, mmene Mulungu anamuuzira kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?+ 27 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.”+
28 Tsopano mmodzi wa alembi amene anafika ndi kuwamva akutsutsana, anadziwa kuti anawayankha bwino, ndipo anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo loyamba ndi liti pa malamulo onse?”+ 29 Yesu anayankha kuti: “Loyamba n’lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova* Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.+ 30 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.’+ 31 Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Kulibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.” 32 Mlembiyo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi, ndipo palibenso wina, koma Iye yekha.’+ 33 Kunena za kukonda Mulungu ndi mtima wonse, maganizo onse, mphamvu zonse, komanso kukonda mnzako mmene umadzikondera wekha, n’zofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.”+ 34 Pamenepo Yesu, pozindikira kuti wayankha mwanzeru, anauza mlembiyo kuti: “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo panalibe amene analimba mtima kumufunsanso.+
35 Koma pamene Yesu anali kuphunzitsa m’kachisi, anayankha zonse mwa kufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani alembi amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 36 Mwa mzimu woyera,+ Davideyo ananena kuti, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’+ 37 Davideyo anamutcha kuti ‘Ambuye,’ nanga zikutheka bwanji kuti alinso mwana wake?”+
Ndipo khamu lalikulu linali kumumvetsera mosangalala.+ 38 Pophunzitsapo Yesu ananenanso kuti: “Chenjerani ndi alembi+ amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ndi kupatsidwa moni m’misika. 39 Komanso amakonda kukhala m’mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo.+ 40 Iwo ndi amene amadyerera nyumba+ za akazi amasiye, ndipo mwachiphamaso amapereka mapemphero ataliatali. Anthu amenewa adzalandira chiweruzo champhamvu.”+
41 Ndiyeno anakhala pansi moyang’anana ndi moponyamo zopereka+ ndipo anali kuona mmene khamu la anthu linali kuponyera ndalama moponya zoperekamo. Anthu ambiri olemera anali kuponyamo makobidi ambiri.+ 42 Kenako panafika mkazi wamasiye wosauka ndipo anaponyamo timakobidi tiwiri tating’ono.+ 43 Choncho Yesu anaitana ophunzira ake ndi kuwauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa onse amene aponya ndalama moponya zoperekamo.+ 44 Zili choncho chifukwa onsewo aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zochirikizira moyo wake.”+