Mawu a M'munsi
a Nkosangalatsa kudziŵa kuti mtumwi Paulo wophunzira kwambiriyo anasankha kudzichirikiza mu utumiki mwa kupanga mahema, umisiri umene mwinamwake anauphunzira kwa atate wake. Kupanga mahema sikunali ntchito yosavuta. Nsalu ya ubweya wa mbuzi imene inagwiritsiridwa ntchito, yotchedwa cilicium, inali yokhuthala ndi ya nyankhalala, yovuta kudula ndi kusoka.—Machitidwe 18:1-3; 22:3; Afilipi 3:7, 8.