Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
Chilengezo
Chinenero chatsopano chomwe chilipo: Betsileo
  • Lero

Loweruka, October 25

Safani anayamba kuwerengera mfumu bukulo.​—2 Mbiri 34:18.

Atakula, Mfumu Yosiya anayamba kukonzanso kachisi. Pogwira ntchitoyi “anapeza buku la Chilamulo cha Yehova loperekedwa ndi dzanja la Mose.” Mfumuyi itamva zimene zinawerengedwa, nthawi yomweyo inasintha kuti itsatire malangizo a m’bukuli. (2 Mbiri 34:14, 19-21) Kodi mumafuna kuti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse? Ngati mukuyesa kale kuchita zimenezi kodi zinthu zikukuyenderani bwanji? Kodi mumasunga mavesi ena ake omwe mukuona kuti angakuthandizeni? Yosiya ali ndi zaka pafupifupi 39, analakwitsa zinthu ndipo zinachititsa kuti aphedwe. Iye anadzidalira m’malo mopempha malangizo kwa Yehova. (2 Mbiri 35:20-25) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kaya ndife wamkulu kapena wamng’ono kapenanso takhala tikuphunzira Baibulo kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenera kupitiriza kufunafuna Yehova. Zimenezi zikuphatikizapo kupempha Yehova nthawi zonse kuti atipatse malangizo, kuphunzira Mawu ake komanso kumvera malangizo a Akhristu olimba mwauzimu. Tikamachita zimenezi tidzapewa kulakwitsa kwambiri zinthu ndipo tidzakhala osangalala.—Yak. 1:25. w23.09 12 ¶15-16

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lamlungu, October 26

Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.—Yak. 4:6.

Baibulo limatchula zitsanzo zambiri za akazi amene ankakonda Yehova komanso kumutumikira. Iwo anali “ochita zinthu mosapitirira malire” ndiponso “okhulupirika pa zinthu zonse.” (1 Tim. 3:11) Kuwonjezera pamenepo, Akhristu achitsikana angapeze mumpingo wawo alongo olimba mwauzimu amene angamawatsanzire. Ngati ndinu mlongo wachitsikana, mungachite bwino kupeza alongo a Chikhristu olimba mwauzimu amene mungamawatsanzire. Muziona makhalidwe awo abwino. Khalidwe lofunika kwambiri kuti Mkhristu akule mwauzimu ndi kudzichepetsa. Mkazi wodzichepetsa amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso anthu ena. Mwachitsanzo, mkazi amene amakonda Yehova amakhala wodzichepetsa n’kumatsatira malangizo amene Yehova anapereka okhudza mutu wa banja ndi mutu wa mpingo.—1 Akor. 11:3. w23.12 18-19 ¶3-5

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lolemba, October 27

Amuna azikonda akazi awo ngati mmene amakondera matupi awo.—Aef. 5:28.

Yehova amafuna kuti mwamuna azikonda mkazi wake ndipo azimupezera zofunika pa moyo, azikhala mnzake wapamtima komanso azimuthandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehovayo. Kuganiza bwino, kulemekeza akazi komanso kukhala odalirika, kungakuthandizeni kuti mukhale mwamuna wabwino. Mukadzakwatira, mukhoza kudzakhala ndi ana. Ndiye kodi mungaphunzire chiyani kwa Yehova pa nkhani yokhala bambo wabwino? (Aef. 6:4) Yehova ankauza Mwana wake Yesu kuti amamukonda ndiponso kuti amamusangalatsa kwambiri. (Mat. 3:17) Nanunso mukadzakhala ndi ana, muzidzawauza pafupipafupi kuti mumawakonda. Nthawi zonse muzidzawayamikira akachita zabwino. Abambo amene amatsanzira Yehova, amathandiza ana awo kuti akule mwauzimu. Mungakonzekere udindo umenewu posamalira mwachikondi anthu a m’banja lanu ndiponso a mumpingo. Komanso pouza anthu ena kuti mumawakonda ndiponso kuwayamikira.—Yoh. 15:9. w23.12 28-29 ¶17-18

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena