Lamlungu, October 26
Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.—Yak. 4:6.
Baibulo limatchula zitsanzo zambiri za akazi amene ankakonda Yehova komanso kumutumikira. Iwo anali “ochita zinthu mosapitirira malire” ndiponso “okhulupirika pa zinthu zonse.” (1 Tim. 3:11) Kuwonjezera pamenepo, Akhristu achitsikana angapeze mumpingo wawo alongo olimba mwauzimu amene angamawatsanzire. Ngati ndinu mlongo wachitsikana, mungachite bwino kupeza alongo a Chikhristu olimba mwauzimu amene mungamawatsanzire. Muziona makhalidwe awo abwino. Khalidwe lofunika kwambiri kuti Mkhristu akule mwauzimu ndi kudzichepetsa. Mkazi wodzichepetsa amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso anthu ena. Mwachitsanzo, mkazi amene amakonda Yehova amakhala wodzichepetsa n’kumatsatira malangizo amene Yehova anapereka okhudza mutu wa banja ndi mutu wa mpingo.—1 Akor. 11:3. w23.12 18-19 ¶3-5
Lolemba, October 27
Amuna azikonda akazi awo ngati mmene amakondera matupi awo.—Aef. 5:28.
Yehova amafuna kuti mwamuna azikonda mkazi wake ndipo azimupezera zofunika pa moyo, azikhala mnzake wapamtima komanso azimuthandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehovayo. Kuganiza bwino, kulemekeza akazi komanso kukhala odalirika, kungakuthandizeni kuti mukhale mwamuna wabwino. Mukadzakwatira, mukhoza kudzakhala ndi ana. Ndiye kodi mungaphunzire chiyani kwa Yehova pa nkhani yokhala bambo wabwino? (Aef. 6:4) Yehova ankauza Mwana wake Yesu kuti amamukonda ndiponso kuti amamusangalatsa kwambiri. (Mat. 3:17) Nanunso mukadzakhala ndi ana, muzidzawauza pafupipafupi kuti mumawakonda. Nthawi zonse muzidzawayamikira akachita zabwino. Abambo amene amatsanzira Yehova, amathandiza ana awo kuti akule mwauzimu. Mungakonzekere udindo umenewu posamalira mwachikondi anthu a m’banja lanu ndiponso a mumpingo. Komanso pouza anthu ena kuti mumawakonda ndiponso kuwayamikira.—Yoh. 15:9. w23.12 28-29 ¶17-18
Lachiwiri, October 28
[Yehova] adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.—Yes. 33:6.
Ngakhale kuti ndife atumiki okhulupirika a Yehova, mofanana ndi anthu onse, timakumana ndi mavuto komanso matenda. Nthawi zinanso timatsutsidwa kapena kuzunzidwa ndi anthu odana ndi anthu a Mulungu. Yehova samatiteteza kuti tisakumane ndi mavuto, koma amatilonjeza kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10) Iye akatithandiza timapitirizabe kukhala osangalala, timasankha zinthu mwanzeru komanso timakhalabe okhulupirika kwa iye ngakhale pamene zili zovuta kutero. Yehova amatilonjeza kuti atipatsa “mtendere [wake]” wotchulidwa m’Baibulo. (Afil. 4:6, 7) Munthu akakhala ndi mtendere umenewu, mtima ndi maganizo ake zimakhala m’malo chifukwa choti ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mtenderewu ndi woti “anthu sangathe kuumvetsa” ndipo ndi wodabwitsa kuposa mmene tingaganizire. Kodi inunso mtima wanu unayamba wakhalapo m’malo mutapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima? Munamva choncho chifukwa cha “mtendere wa Mulungu.” w24.01 20 ¶2; 21 ¶4