Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lolemba, September 15

Abale, pa nkhani ya kumva zowawa ndi kuleza mtima, tengerani chitsanzo cha aneneri amene analankhula m’dzina la Yehova.​—Yak. 5:10.

M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anali oleza mtima. Bwanji osakonza zoti mufufuze zitsanzozi pamene mukuphunzira Baibulo panokha? Mwachitsanzo, ngakhale kuti Davide anadzozedwa ali mwana kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli, anafunika kudikira kwa zaka zambiri asanapatsidwe ufumuwo. Simiyoni ndi Anna ankatumikira Yehova mokhulupirika pamene ankayembekezera kubwera kwa Mesiya. (Luka 2:25, 36-38) Mukamaphunzira nkhanizi muzifufuza mayankho a mafunso awa: Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinathandiza munthuyu kuti akhale woleza mtima? Kodi kukhala woleza mtima kunamuthandiza bwanji? Kodi ndingamutsanzire bwanji? Mungapindulenso ngati mutaphunzira za anthu omwe sanasonyeze kuleza mtima. (1 Sam. 13:8-14) Mungadzifunse kuti: ‘Kodi mwina n’chiyani chinachititsa kuti asakhale woleza mtima? Nanga zotsatirapo zake zinali zotani?’ w23.08 25 ¶15

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachiwiri, September 16

Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera amene Mulungu anamutumiza.​—Yoh. 6:69.

Mtumwi Petulo anali wokhulupirika ndipo sanalole kuti chilichonse chimulepheretse kutsatira Yesu. Iye anasonyeza kukhulupirika kwake pa nthawi ina pamene Yesu analankhula zinthu zimene ophunzira ake sanazimvetse. (Yoh. 6:68) Anthu ambiri anasiya kutsatira Yesu popanda kudikira kuti awafotokozere zimene ankatanthauza. Koma Petulo ankadziwa kuti Yesu yekha, ndi yemwe ali ndi “mawu othandiza munthu kuti adzapeze moyo wosatha.” Yesu ankadziwa kuti Petulo ndi atumwi ena amusiya yekha. Komabe sankakayikira kuti Petulo adzabwerera n’kukhalabe wokhulupirika. (Luka 22:31, 32) Yesu ankadziwa kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Maliko 14:38). Choncho ngakhale kuti Petulo anamukana kuti sakumudziwa, iye sanasiye kukonda mtumwi wakeyu. Ataukitsidwa, Yesu anakumana ndi Petulo ndipo zikuoneka kuti Petuloyo anali yekha. (Maliko 16:7; Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Zimenezi ziyenera kuti zinalimbikitsa mtumwiyu, yemwe ankadzimvera chisoni kwambiri. w23.09 22 ¶9-10

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachitatu, September 17

Osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo ndipo machimo awo akhululukidwa.​—Aroma 4:7.

Mulungu amakhululuka kapena kuphimba machimo a anthu omwe amamukhulupirira. Iye amawakhululukira kotheratu moti sawerengeranso machimo awo. (Sal. 32:1, 2) Amawaona kuti ndi opanda cholakwa komanso olungama chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ngakhale kuti Abulahamu, Davide ndi atumiki ena okhulupirika ankaonedwa kuti ndi olungama, iwo anali adakali ochimwa. Koma chifukwa cha chikhulupiriro chawo, Mulungu ankawaona kuti ndi opanda cholakwa poyerekezera ndi anthu omwe sankamutumikira. (Aef. 2:12) Mtumwi Paulo anafotokoza bwino m’kalata yake zoti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri kuti munthu akhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Ndi mmenenso zinalili ndi Abulahamu ndi Davide. Choncho ifenso chikhulupiriro chingatithandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. w23.12 3 ¶6-7

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena