Lachiwiri, September 16
Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera amene Mulungu anamutumiza.—Yoh. 6:69.
Mtumwi Petulo anali wokhulupirika ndipo sanalole kuti chilichonse chimulepheretse kutsatira Yesu. Iye anasonyeza kukhulupirika kwake pa nthawi ina pamene Yesu analankhula zinthu zimene ophunzira ake sanazimvetse. (Yoh. 6:68) Anthu ambiri anasiya kutsatira Yesu popanda kudikira kuti awafotokozere zimene ankatanthauza. Koma Petulo ankadziwa kuti Yesu yekha, ndi yemwe ali ndi “mawu othandiza munthu kuti adzapeze moyo wosatha.” Yesu ankadziwa kuti Petulo ndi atumwi ena amusiya yekha. Komabe sankakayikira kuti Petulo adzabwerera n’kukhalabe wokhulupirika. (Luka 22:31, 32) Yesu ankadziwa kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Maliko 14:38). Choncho ngakhale kuti Petulo anamukana kuti sakumudziwa, iye sanasiye kukonda mtumwi wakeyu. Ataukitsidwa, Yesu anakumana ndi Petulo ndipo zikuoneka kuti Petuloyo anali yekha. (Maliko 16:7; Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Zimenezi ziyenera kuti zinalimbikitsa mtumwiyu, yemwe ankadzimvera chisoni kwambiri. w23.09 22 ¶9-10
Lachitatu, September 17
Osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo ndipo machimo awo akhululukidwa.—Aroma 4:7.
Mulungu amakhululuka kapena kuphimba machimo a anthu omwe amamukhulupirira. Iye amawakhululukira kotheratu moti sawerengeranso machimo awo. (Sal. 32:1, 2) Amawaona kuti ndi opanda cholakwa komanso olungama chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ngakhale kuti Abulahamu, Davide ndi atumiki ena okhulupirika ankaonedwa kuti ndi olungama, iwo anali adakali ochimwa. Koma chifukwa cha chikhulupiriro chawo, Mulungu ankawaona kuti ndi opanda cholakwa poyerekezera ndi anthu omwe sankamutumikira. (Aef. 2:12) Mtumwi Paulo anafotokoza bwino m’kalata yake zoti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri kuti munthu akhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Ndi mmenenso zinalili ndi Abulahamu ndi Davide. Choncho ifenso chikhulupiriro chingatithandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. w23.12 3 ¶6-7
Lachinayi, September 18
Nthawi zonse tizitamanda Mulungu. . . . Kuchita zimenezi kuli ngati nsembe imene tikupereka kwa Mulungu ndipo timagwiritsa ntchito milomo yathu polengeza dzina lake.—Aheb. 13:15.
Masiku ano Akhristu onse ali ndi mwayi wopereka nsembe kwa Yehova pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndiponso zinthu zawo pomutumikira. Tingasonyeze kuti timayamikira mwayi wathu wolambira Yehova poyesetsa kuchita zonse zomwe tingathe pomutumikira. Mtumwi Paulo anatchula zinthu zosiyanasiyana zokhudza kulambira kwathu zimene sitiyenera kuzinyalanyaza. (Aheb. 10:22-25) Zinthu zake zikuphatikizapo kupemphera kwa Yehova, kulengeza poyera chiyembekezo chathu, kusonkhana pamodzi ngati mpingo ndiponso kulimbikitsana, ‘makamaka panopa pamene tikuona kuti tsiku la [Yehova] likuyandikira.’ Pofuna kutsindika, chakumapeto kwa buku la Chivumbulutso, mngelo wa Yehova ananena kawiri kuti: “Lambira Mulungu.” (Chiv. 19:10; 22:9) Tiyeni tizikumbukira nthawi zonse mfundo zozama za choonadi zokhudza kachisi wamkulu wauzimu ndipo tiziyamikira mwayi wolambira Mulungu wathu wamkulu, Yehova. w23.10 29 ¶17-18