Lamlungu, September 21
Nawonso akazi akhale . . . ochita zinthu mosapitirira malire, okhulupirika pa zinthu zonse.—1 Tim. 3:11.
Timadabwa kuona mmene mwana amakulira mofulumira kwambiri n’kukhala munthu wamkulu. Zimaoneka kuti kukula kumeneku kumangochitika pakokha. Koma kukula mwauzimu sikumachitika pakokha. (1 Akor. 13:11; Aheb. 6:1) Kuti munthu akule mwauzimu amafunika kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Timafunikanso mzimu woyera kuti utithandize kukhala ndi makhalidwe abwino, kukhala ndi luso lochitira zinthu bwino komanso kukonzekera maudindo athu am’tsogolo. (Miy. 1:5) Polenga anthu, Yehova anawalenga mwamuna ndi mkazi. (Gen. 1:27) Mwamuna ndi mkazi amaoneka mosiyana komanso amakhala osiyana m’njira zina. Mwachitsanzo, Yehova analenga amuna ndi akazi kuti azikwaniritsa maudindo osiyana. Choncho iwo amafunika kukhala ndi makhalidwe komanso maluso amene angawathandize kukwaniritsa bwino maudindo awowo.—Gen. 2:18. w23.12 18 ¶1-2
Lolemba, September 22
Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza mʼdzina la Atate, [ndi] la Mwana.—Mat. 28:19.
Kodi Yesu amafuna kuti enanso azigwiritsa ntchito dzina lenileni la Atate wake? Inde. Atsogoleri ena achipembedzo pa nthawiyo, ankakhulupirira kuti dzina la Mulungu ndi lopatulika kwambiri ndipo si ulemu kumalitchula. Koma Yesu sanalole kuti miyambo yosagwirizana ndi Malembayi imulepheretse kulemekeza dzina la Atate wake. Taganizirani zimene zinachitika atachiritsa munthu wina wogwidwa ndi ziwanda, m’dera la Agerasa. Anthu akumeneko anachita mantha ndipo anapempha Yesu kuti achoke m’deralo, ndipo anachokadi. (Maliko 5:16, 17) Komabe, Yesu ankafuna kuti anthu akumeneko adziwe dzina la Yehova. Choncho analamula munthu amene anamuchiritsayo kuti aziuza anthu, osati zimene Yesu anamuchitira, koma zimene Yehova anamuchitira. (Maliko 5:19) Masiku anonso, iye amafuna kuti tizidziwitsa anthu padziko lonse dzina la Atate wake. (Mat. 24:14; 28:20) Tikamachita zimenezi, timasangalatsa Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu. w24.02 10 ¶10
Lachiwiri, September 23
Walimbana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha dzina langa.—Chiv. 2:3.
Ndi mwayi waukulu kukhala m’gulu la Yehova masiku otsiriza ovutawa. Pamene zinthu zikuipiraipira m’dzikoli, Yehova watipatsa banja lauzimu logwirizana la abale ndi alongo. (Sal. 133:1) Amatithandizanso kuti tizikhala ndi mabanja olimba. (Aef. 5:33–6:1) Komanso amatipatsa nzeru kuti tizikhala ndi mtendere wa mumtima. Koma tiyenera kuchita khama kuti tipitirizebe kutumikira Yehova mokhulupirika. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa nthawi zina tikhoza kukhumudwa ndi zinthu zimene ena alakwitsa. Tikhozanso kumakhumudwa ngati timalakwitsa zinthu zinazake mobwerezabwereza. Tiyenera kupitiriza kutumikira Yehova ngakhale (1) Mkhristu mnzathu akatilakwira, (2) mwamuna kapena mkazi wathu akatikhumudwitsa, ndiponso (3) tikakhumudwa ndi zimene timalakwitsa. w24.03 14 ¶1-2