Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Loweruka, September 20

Muzikondana.​—Yoh. 13:34.

Sitingamvere lamulo la Yesu lakuti tizikondana ngati timakonda ena mumpingo n’kumalephera kukonda ena. N’zoona kuti tingamagwirizane kwambiri ndi ena kuposa ena, ngati mmenenso Yesu ankachitira. (Yoh. 13:23; 20:2) Koma mtumwi Petulo akutikumbutsa kuti tiyenera kuyesetsa kuti ‘tizikonda abale’ onse ngati anthu a m’banja lathu. (1 Pet. 2:17) Petulo anatilimbikitsa kuti ‘tizikondana kwambiri kuchokera mumtima.’ (1 Pet. 1:22) Apa mawu akuti ‘kukondana kwambiri’ akutanthauza kukonda winawake ngakhale pamene zili zovuta kutero. Mwachitsanzo, bwanji ngati m’bale watikhumudwitsa m’njira inayake? Mwachibadwa timafuna kumubwezera osati kumusonyeza chikondi. Komatu Petulo anaphunzira kwa Yesu kuti kubwezera sikusangalatsa Mulungu. (Yoh. 18:10, 11) Iye analemba kuti: “Munthu akakuchitirani choipa musamabwezere ndi choipa, akakuchitirani chipongwe musamabwezere ndi chipongwe. M’malomwake muziwachitira zabwino.” (1 Pet. 3:9) Muzilola kuti kukonda kwambiri ena, kuzikulimbikitsani kuti muzikomera mtima komanso kuganizira ena. w23.09 28-29 ¶9-11

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lamlungu, September 21

Nawonso akazi akhale . . . ochita zinthu mosapitirira malire, okhulupirika pa zinthu zonse.—1 Tim. 3:11.

Timadabwa kuona mmene mwana amakulira mofulumira kwambiri n’kukhala munthu wamkulu. Zimaoneka kuti kukula kumeneku kumangochitika pakokha. Koma kukula mwauzimu sikumachitika pakokha. (1 Akor. 13:11; Aheb. 6:1) Kuti munthu akule mwauzimu amafunika kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Timafunikanso mzimu woyera kuti utithandize kukhala ndi makhalidwe abwino, kukhala ndi luso lochitira zinthu bwino komanso kukonzekera maudindo athu am’tsogolo. (Miy. 1:5) Polenga anthu, Yehova anawalenga mwamuna ndi mkazi. (Gen. 1:27) Mwamuna ndi mkazi amaoneka mosiyana komanso amakhala osiyana m’njira zina. Mwachitsanzo, Yehova analenga amuna ndi akazi kuti azikwaniritsa maudindo osiyana. Choncho iwo amafunika kukhala ndi makhalidwe komanso maluso amene angawathandize kukwaniritsa bwino maudindo awowo.—Gen. 2:18. w23.12 18 ¶1-2

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lolemba, September 22

Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza mʼdzina la Atate, [ndi] la Mwana.​—Mat. 28:19.

Kodi Yesu amafuna kuti enanso azigwiritsa ntchito dzina lenileni la Atate wake? Inde. Atsogoleri ena achipembedzo pa nthawiyo, ankakhulupirira kuti dzina la Mulungu ndi lopatulika kwambiri ndipo si ulemu kumalitchula. Koma Yesu sanalole kuti miyambo yosagwirizana ndi Malembayi imulepheretse kulemekeza dzina la Atate wake. Taganizirani zimene zinachitika atachiritsa munthu wina wogwidwa ndi ziwanda, m’dera la Agerasa. Anthu akumeneko anachita mantha ndipo anapempha Yesu kuti achoke m’deralo, ndipo anachokadi. (Maliko 5:16, 17) Komabe, Yesu ankafuna kuti anthu akumeneko adziwe dzina la Yehova. Choncho analamula munthu amene anamuchiritsayo kuti aziuza anthu, osati zimene Yesu anamuchitira, koma zimene Yehova anamuchitira. (Maliko 5:19) Masiku anonso, iye amafuna kuti tizidziwitsa anthu padziko lonse dzina la Atate wake. (Mat. 24:14; 28:20) Tikamachita zimenezi, timasangalatsa Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu. w24.02 10 ¶10

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena