AUGUST 25-31
MIYAMBO 28
Nyimbo Na. 150 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kusiyana Pakati pa Munthu Woipa ndi Munthu Wolungama
(10 min.)
Munthu woipa amakhala wamantha, pomwe wolungama amakhala wolimba mtima (Miy 28:1; w93 5/15 26 ¶2)
Munthu woipa saona zinthu moyenera, pomwe wolungama amasankha zinthu mwanzeru (Miy 28:5; it-2 1139 ¶3)
Munthu wolungama amene ndi wosauka amakhala wamtengo wapatali kuposa munthu woipa yemwe ndi wolemera (Miy 28:6; it-1 1211 ¶4)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 28:14—Kodi pavesili pali chenjezo lotani? (w01 12/1 11 ¶3)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 28:1-17 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani kuti nkhondo komanso zachiwawa zidzatha. (lmd phunziro 5 mfundo 5)
5. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani kuti nkhondo komanso zachiwawa zidzatha. (lmd phunziro 5 mfundo 4)
6. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Kambiranani kuti nkhondo komanso zachiwawa zidzatha. (lmd phunziro 1 mfundo 4)
7. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Kambiranani kuti nkhondo komanso zachiwawa zidzatha. (lmd phunziro 2 mfundo 4)
Nyimbo Na. 112
8. Kodi Mumadana ndi Zachiwawa?
(6 min.) Nkhani yokambirana.
Satana Mdyerekezi yemwe Yesu anamutchula kuti “wopha anthu,” ndi amene anayambitsa zachiwawa. (Yoh 8:44) Angelo ena atakhala ku mbali ya Satana popandukira Mulungu, chiwawa chinawonjezereka kwambiri padziko lapansi moti linaipa kwambiri pamaso pa Mulungu. (Ge 6:11) Pamene tikuyandikira mapeto a dziko lachiwawa la Satanali, anthu ambiri ndi oopsa komanso osadziletsa.—2Ti 3:1, 3.
Werengani Salimo 11:5. Kenako funsani mafunso awa:
Kodi Yehova amaona bwanji anthu amene amakonda zachiwawa, nanga n’chifukwa chiyani?
Kodi masewera komanso zosangalatsa zina zimasonyeza bwanji kuti anthu m’dzikoli amakonda kwambiri zachiwawa?
Werengani Miyambo 22:24, 25. Kenako funsani mafunso awa:
Kodi zosangalatsa zimene timasankha komanso anthu amene timachita nawo zinthu zingakhudze bwanji mmene timaonera zachiwawa?
Kodi zosangalatsa zimene timasankha zingasonyeze bwanji kuti timakonda zachiwawa?
9. Ntchito Yapadera Yolalikira mu September
(9 min.)
Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Limbikitsani omvera kuti adzagwire nawo ntchitoyi mwakhama ndipo fotokozani zimene mpingo wanu wakonza.
Onerani VIDIYO yakuti Kudzakhala Mtendere (Nyimbo ya Msonkhano ya 2022)
10. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 12-13
Mawu Omaliza (3 min.) | ndi Pemphero
Nkhani Yophunzira 25: August 25-31, 2025
8 Zimene Tikuphunzira pa Ulosi wa Yakobo Atatsala Pang’ono Kumwalira—Gawo 2