SEPTEMBER 1-7
MIYAMBO 29
Nyimbo Na. 28 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzikana Miyambo Kapena Zikhulupiriro Zomwe Sizisangalatsa Mulungu
(10 min.)
Mukamamvera Yehova, mumasangalaladi (Miy 29:18; wp16.6 6, bokosi)
Muzidalira nzeru za Mulungu kuti mudziwe ngati mwambo winawake umamusangalatsa kapena ayi (Miy 29:3a; w19.04 17 ¶13)
Musamalole kuti anthu ena akukakamizeni kuchita miyambo yomwe sisangalatsa Mulungu (Miy 29:25; w18.11 11 ¶12)
Kufufuza mfundo za m’Baibulo mosamala kwambiri komanso kukambirana ndi achibale omwe si a Mboni, kungakuthandizeni kupewa miyambo imene sisangalatsa Mulungu
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 29:5—Kodi kuyamikira mwachiphamaso n’kutani, nanga munthu amene amachita zimenezi amayalira bwanji ukonde mapazi ake? (it “Kuyamikira Mwachiphamaso” ¶1)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 29:1-18 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muitanireni kuti adzamvetsere nkhani yapadera. (lmd phunziro 2 mfundo 3)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda Na. 1 2025 kuti muyambe kukambirana ndi munthu. Sinthani nkhani yomwe mukukambirana kuti igwirizane ndi nkhani yomwe munthuyo ali nayo chidwi. (lmd phunziro 3 mfundo 3)
6. Ulendo Woyamba
(5 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Perekani magazini ya Nsanja ya Olonda Na. 1 2025 kwa munthu amene akudera nkhawa zokhudza nkhondo. (lmd phunziro 3 mfundo 4)
Nyimbo Na. 159
7. Zofunika Pampingo
(15 min.)
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mawu oyamba gawo 4 komanso mutu 14-15