Pamene Anatitengera ku Ukapolo ku Siberia!
YOSIMBIDWA NDI VASILY KALIN
Mutaona munthu akuŵerenga Baibulo ali phee koma mfuti zikulilima, kodi simungafune kudziŵa kuti n’chiyani cham’khazika mtima m’malo choncho? Bambo wanga anaona zoterozo zaka 56 zapitazo.
MUNALI mu July 1942 Nkhondo Yadziko II itafika pachimake. Pamene asilikali a Germany anali kudutsa m’mudzi umene munkakhala bambo wanga, umene umatchedwa Vilshanitsa, ku Ukraine, bambo wanga anakhotera ku khomo la mkulu wina wachikulire. Mfuti zinali kulilima konsekonse, komabe munthuyo anali atangokhala pambali pamoto namaotcha chimanga uku akuŵerenga Baibulo.
Ineyo ndinabadwa patapita zaka zisanu, pafupi ndi mzinda wa Ivano-Frankivs’k, ku Ukraine, dziko lomwe linali mbali ya Soviet Union. Kenaka bambo wanga anandiuza mmene anakumanirana ndi munthu ameneyo, wa Mboni za Yehova ndiponso za kuopsa kwa zaka za nkhondo, kuti sadzaiŵala. Anthu anali atatopa ndi kusokonezeka nazo maganizo, ndipo ambiri anali kudzifunsa kuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani anthu akuzunza kwambiri anzawo chonchi? Anthu osalakwa ambirimbiri akuferanji chonchi? Kodi Mulungu akuloleranji zimenezi? N’chifukwa chiyani izi zili chonchi, izo zili motero, zija zili mwakutimwakuti?’
Bambo anakambirana ndi munthu wachikulireyo mofunadi kumvetsetsa kwa nthaŵi yaitali mafunso ngati amenewo. Munthuyo anali kutsegula Baibulo lake lemba ndi lemba, namasonyeza bambo mayankho a mafunso amene sanali kuwamvetsetsa kwa nthaŵi yaitali. Munthuyo anafotokoza kuti cholinga cha Mulungu ndi choti nthaŵi yake ikadzakwana, adzathetse nkhondo zonse ndiponso kuti dzikoli lidzakhala paradaiso wokongola.—Salmo 46:9; Yesaya 2:4; Chivumbulutso 21:3, 4.
Bambo anathamangira kunyumba n’kungofikira kuti: “Kodi mungakhulupirire? Ndangokambirana kamodzi basi ndi Mboni za Yehova ndipo maso anga atseguka! Ndachipeza choonadi!” Bambo ananena kuti ngakhale ankapita ku Tchalitchi cha Katolika nthaŵi zonse, ansembe ankalephera kuwayankha mafunso awo. Choncho Bambo anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo mayi wanga nawo anayambanso. Anayambanso kuphunzitsa ana awo atatu—mlongo wanga, yemwe anali ndi zaka ziŵiri chabe, ndi akulu anga, wina wazaka 7 ndi wina wazaka 11. Posakhalitsa, bomba linawononga kwambiri nyumba yawo, n’kungosiya chipinda chimodzi chokha chokhalamo.
Mayi anachokera m’banja lalikulu la akazi asanu ndi mmodzi, ndi mwamuna mmodzi. Bambo awo anali m’modzi wa anthu olemera m’dera lawo, ndipo ankadziona kuti iwo anali munthu wofunika kumamumvera komanso kumamulemekeza. Choncho, poyamba achibale ankadana nazo zoti anthu a m’banja lathu ayambe chikhulupiriro chatsopano. Komabe, patapita nthaŵi, ambiri amene anali kutitsutsa anasiya kuchita zinthu zotsutsidwa ndi Malemba, monga kugwiritsira ntchito mafano, n’kuyamba kugwirizana ndi makolo anga pakulambira koona.
Ansembe ankasonkhezera anthu mosabisa kuti azidana ndi a Mboni. Ndiyeno anthu oyandikana nawo anali kumangowaswera mawindo awo namawaopseza. Makolo anga sanasamale zimenezo, anapitirizabe kuphunzira Baibulo. Choncho, pamene ine ndinabadwa mu 1947, n’kuti a m’banja lathu akulambira Yehova mumzimu ndi m’choonadi.—Yohane 4:24.
Kutitengera ku Ukapolo
Zimene zinachitika m’mamaŵa kwambiri pa April 8, 1951, ndikuzikumbukirabe, ngakhale kuti nthaŵi imeneyo n’kuti ndili ndi zaka zinayi zokha. Asilikali okhala ndi agalu analoŵa m’nyumba mwathu. Ndiye anatisonyeza chikalata chotilamula kuchoka m’dzikomo. Kenaka anayamba kufufuzafufuza m’nyumba. Asilikali okhala ndi mfuti zachiwaya ndi agalu anangoti chilili pakhomo pathu, kwinaku ena ovala zausilikali atakhala pathebulo pathu, kutidikira kuti tikonzeke msangamsanga tinyamuke asanathe maola aŵiri amene anatipatsa. Sindinali kumvetsa kuti chikuchitika ndi chiyani, ndipo ndinayamba kulira.
Makolo anga analamulidwa kusayina dzina lawo pa chikalata china kunena kuti iwowo sanalinso a Mboni za Yehova ndi kutinso sadzagwirizana nawonso. Akadavomera kusayina dzina lawo, akanaloledwa kukhalabe m’nyumba mwawo, kukhalabe m’dziko lawo. Koma bambo ananena molimba mtima kuti: “Ndikudziŵa kuti kulikonse kumene mungakatisiye, Mulungu wathu, Yehova akakhalabe nafe komweko.”
Msilikaliyo anadandaula kuti: “Ganizirani banja lanu, ana anunso. Chifukwa si kuti tikukupititsani kumalo a chisangalalo ayi. Tikukupititsani kutali kumpoto, kozizira chizizirire ndipo zimbalangondo m’misewu zimangoti yakaliyakali.”
Panthaŵiyo liwu lakuti “Siberia” linali loopsa ndi losadziŵika bwino kwa aliyense. Komabe, poti tinkakhulupirira Yehova ndi kum’konda kwambiri, sitinachite nazo mantha zosadziŵikazo. Analonga katundu wathu m’ngolo, ndiyeno anamka nafe kumzinda n’kukakweza katunduyo m’sitima, limodzi ndi mabanja ena okwana 20 kapena 30. Ndiyeno tinauyamba ulendo wathu womka kunkhalango, kapena kuchipululu cha Siberia.
Pamasiteshoni onse amene tinali kuimapo m’njira, tinali kukumana ndi sitima zina zonyamula anthu othamangitsidwa kwawo, ndipo tinali kuonanso zikwangwani zokolekedwa pamabogi a sitima, zakuti: “Muno mwakwera Mboni za Yehova.” Umenewo unalinso umboni wina wapadera, chifukwa anthu ambiri anadziŵa kuti a Mboni ambirimbiri ndi mabanja awo akuwapitikitsira kumpoto ndi kum’maŵa.
Kugwidwa kwa Mboni za Yehova ndi kuthamangitsidwa m’dziko lawo mu April 1951 ndi nkhani yolembedwa m’mabuku ambiri. Wolemba mbiri wina wotchedwa Walter Kolarz, analemba m’buku lake lakuti Religion in the Soviet Union, kuti: “Kumeneku sikunali kutha kwa ‘Mboni’ ku Russia, koma chabe chiyambi china cha ntchito yawo yotembenuza anthu. Ndipo ankayesa ngakhale kufalitsa chikhulupiriro chawo paliponse pamene anaima panjira pom’ka kudziko lothaŵirako. Pamene Boma la Soviet linali kuwapitikitsa m’dziko, silinali kudziŵa kuti linali kungowathandiza kufalitsa chikhulupiriro chawo. Pamene ‘Mbonizo’ anazitenga ndi kuzipititsa kutali ndi kwawo, anakazitula kumene kunali anthu ambiri, ngakhale kuti linali dziko loipa kumene zinkagwira ntchito yaukapolo m’misasa.”
Ifeyo tinali ndi mwayi, chifukwa anatilola kutenga chakudya—ufa, chimanga, ndi nyemba. Agogo anga mpaka anawalola kupha nkhumba, moti tinali ndi ndiwo ife ndi Mboni zina. M’njira monse nyimbo zinali wawawa, kuimba ndi mtima wonse m’sitima. Yehova anatipatsa nyonga yakupirira.—Miyambo 18:10.
Tinayenda ulendo pafupifupi milungu itatu tisanatulukebe m’Russia ndipo mpaka tinafika ku Siberia, kumene kuli kutali, kwa zii komanso kozizira. Anatitula pasiteshoni ya Toreya m’dera la Chunsk ku Irkutsk. Kuchokera pamenepo, anamka nafe kunkhalango, pakamudzi kena. M’zikalata zathu munalembedwa kuti pamudzi pamenepa padzakhala pathu “mpaka kalekale.” Katundu wa mabanja 15 anakwana m’ngolo, ndipo tirakita inakoka ngoloyo m’matope. Mabanja 20 anaikidwa m’nyumba zimene zinali za asilikali, nyumba zazitali zopanda zipinda. Boma linawauziratu chire anthu a m’mudzimo kuti a Mboni za Yehova ndi anthu oipa. Choncho, kungoyambira pachiyambi, anthu anali kuchita nafe mantha ndipo sanayese kutizoloŵera.
Ntchito ku Ukapolo
Mboni za Yehova zinkagwira ntchito yodula mitengo, koma m’mikhalidwe yoipa kwambiri. Ntchito zonse zinkagwiridwa ndi manja—kudula mitengo, kuilonga m’ngolo zokokedwa ndi akavalo, ndiyeno n’kukaikweza m’sitima. Zinthu zinavuta kwambiri pamene kunabwera khamu latizilombo touluka, mizaza yoluma, imene inali yosaingitsika. Bambo wanga zinawasautsa kwambiri. Thupi lawo linangotupiratu, ndipo anapemphera kwambiri kwa Yehova kuti awathandize kupirira. Koma ngakhale zinthu zinali zovuta choncho, Mboni za Yehova zinakhulupirikabe, osagwedezeka.
Posakhalitsa anakatisiya kumzinda wa Irkutsk, kumeneko tinkakhala m’nyumba imene kale inali ndende ndipo tinkagwira ntchito pakampani ina yake yopanga njerwa. Njerwazo tinali kuziphula ndi manja muuvuni wotentha, ndipo ankawonjezera chiŵerengero cha njerwa zimene aliyense anayenera kunyamula, moti ngakhale ana anayamba kuthandiza makolo awo kuti akwanitse chiŵerengero cha njerwazo. Tinakumbukira za ntchito imene Aisrayeli akale ankagwiritsidwa monga akapolo ku Igupto.—Eksodo 5:9-16.
Kenaka zinaoneka kuti a Mboni ndi anthu ogwira ntchito zedi ndipo oona mtima, osati “adani a anthu.” Zinaonekanso kuti panalibe wa Mboni amene ananyoza boma, ndiponso a Mboni sankatsutsa zimene owayang’anira ankafuna. Anthu ambiri anayamba kukopeka ndi chikhulupiriro chawo.
Moyo Wathu Wauzimu
Ngakhale kuti katundu wa Mboni anafufuzidwa mobwerezabwereza—asanathamangitsidwe m’dziko, adakali m’njira, ndiponso kumene anawathamangitsirako—ambiri anatha kubisa magazini a Nsanja ya Olonda ngakhale mabaibulo amene. Kenaka, anatha kulembanso nkhani zake mwina pamanja kapenanso mwa njira zina. Ankakhala pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse m’nyumba zakale za asilikali. Ankati woyang’anira asilikali akabwera n’kutipeza tikuimba nyimbo pagulu, ankatiletsa. Ndiye tinkalekadi. Koma akapita kunyumba ina, tinkayambiranso kuimba. Sitikanaleka iyayi.
Ngakhale ntchito yathu yolalikira siinaime iyayi. A Mboni ankalankhula ndi wina aliyense kwina kulikonse. Nthaŵi zonse akulu anga ndi makolo anga anali kundiuza njira zimene anali kuuzira ena choonadi cha Baibulo. Njira zimenezo zinathandiza kuti pang’onopang’ono anthu oona mtima ayambe kumva choonadi. Choncho, kuchiyambi kwa ma 1950, anthu a ku Irkutsk anayamba kudziŵa za Ufumu wa Yehova.
Poyamba a Mboni anali kuonedwa ngati adani pankhani zandale, koma akuluakulu anaona kuti gulu lathuli n’lachipembedzo basi. Komabe, olamulira anayesayesabe kuletsa ntchito yathu. Choncho kuti asatitulukire, tinayamba kuphunzira Baibulo tikasonkhana m’timagulu ta mabanja aŵiri kapena atatu basi. Tsiku lina m’mamaŵa, mu February 1952 anabwera kudzafufuza m’nyumba. Kenaka, Mboni khumi zinamangidwa, ndipo enafe anapita nafe kumalo osiyanasiyana. Banja lathu anapita nalo kumudzi wotchedwa Iskra, mudzi wokhala ndi anthu pafupifupi 100, ndipo kuchoka pamenepo kukafika kumzinda wa Irkutsk, pali makilomita 30.
Kupirirabe Pamene Mikhalidwe Inkasintha
Akuluakulu a m’mudzimo anatilandira mwa ulemu umene sitinauyembekezere. Anthu ake anali odzichepetsa ndi aubwenzi—angapo anabwera kudzatithandiza. Banja lathu ndilo linali lachitatu kupatsidwa kachipinda kamodzi kukula kwake kunali pafupifupi mamita 17. Tinali kuunikira ndi nyali ya parafini.
Tsiku lotsatira kunali chisankho. Makolo anga ananena kuti anali atasankha kale Ufumu wa Mulungu, ndipo zimenezo zinangowadabwitsa anthu. Choncho ena a m’banja lathu okula msinkhu anakhala tsiku lonse atamangidwa. Kenaka, anthu angapo anayamba kuwafunsafunsa za chikhulupiriro chawo, ndiye panapezeka mpata woti a m’banja lathu awauze za Ufumu wa Mulungu kuti ndi wokhawo umene anthu ayenera kuuyembekezera.
Pazaka zonse zinayi zimene tinakhala m’mudzi wa Iskra, panalibe Mboni zina chapafupi zimene tikanatha kusonkhana nazo. Kuti tichoke m’mudzimo, tinkafunikira kuyamba tapempha chilolezo chapadera kwa mkulu wa asilikali, koma kaŵirikaŵiri sankatiloleza, chifukwa cholinga chenicheni chimene anatithamangitsira kwathu chinali choti atilekanitse ndi anthu ena. Komabe, nthaŵi zonse a Mboniwo anali kuonana ndi anzawo kuti agaŵane chakudya chauzimu chilichonse chimene wina anapeza.
Stalin atamwalira mu 1953, a Mboni onse amene anamangidwa anawachepetsera zaka zawo m’ndende kuchoka pa zaka 25 kufika pa 10. Kwa amene anali ku Siberia, sankafunikiranso chikalata chapadera chowaloleza kuyendayenda. Komabe, olamulira anayambanso kufufuza m’nyumba za anthu ndi kumanga a Mboni onse amene anawapeza ali ndi mabaibulo kapena mabuku onena za Baibulo. Anapanganso misasa ina yoti muzikhala a Mboni, ndipo abale 400 ndi alongo 200 anawaika m’misasa imeneyo m’dera la Irkutsk.
Mboni za Yehova padziko lonse zinamva mbiri yakuti tikuzunzidwa ku Soviet Union. Choncho, pakati pa August mu 1956 ndi February mu 1957, pamisonkhano yachigawo 199 yochitika padziko lonse panaŵerengedwa chikalata choimira pempho la tonsefe. Anthu 462,936 omwe analipo anavomereza kuti mawu analembedwa m’chikalatacho akaperekedwe kwa yemwe anali mtsogoleri wa dziko la Soviet, Nikolay A. Bulganin. Zina mwa zinthu zimene tinapempha pachikalatacho, zinali zakuti timasulidwe ndi kutinso “tiziloledwa kulandira magazini a Nsanja ya Olonda m’chinenero cha ku Russia, cha ku Ukraine ndi m’zinenero zina zofunika, ndi kumalandiranso mabuku ena onena za Baibulo amene a Mboni za Yehova ankagwiritsira ntchito padziko lonse.”
Panthaŵiyi, n’kuti banja lathu atapita nalo kumudzi wina wakutali, mudzi wa Khudyakovo, pafupifupi makilomita 20 kuchokera ku Irkutsk. Tinakhala kumeneko zaka zisanu ndi ziŵiri. Mu 1960 mkulu wanga Fyodor anapita ku Irkutsk, ndipo chaka chotsatira mkulu wangayo anakwatira, ndipo mlongo wanga anapita kwina. Ndiye mu 1962, Fyodor anamangidwa n’kuikidwa m’ndende chifukwa cholalikira.
Kukula Kwanga Kwauzimu
Kuyenda pansi kapena panjinga, kuchokera m’mudzi wathu wa Khudyakovo, unali ulendo wamakilomita pafupifupi 20, kukafika kumene tinkasonkhana ndi ena kuti tiphunzire Baibulo. Choncho tinayesa kusamukira kufupi ndi Irkutsk kuti tikayandikane ndi a Mboni anzathu. Komabe, anyakwawa a m’mudzi umene tinkakhalamowo sizinawasangalatse zoti tikufuna kusamuka, ndiye anayesetsa kuchita izi ndi izi kuti atiletse. Komabe, kenaka anayamba kutiyanja, ndiyeno anatilola kusamukira kumudzi wa Pivovarikha, makilomita pafupifupi 10 kuchokera ku Irkutsk. Kumeneko anakhazikitsako mpingo wa Mboni za Yehova, ndipo ndinayamba moyo watsopano. Ku Pivovarikha kunali magulu olinganizidwa a Phunziro la Buku la Mpingo ndi abale omwe ankayang’anira zinthu zauzimu. Ndinasangalala bwanji!
Pomafika nthaŵi imeneyo ndinali nditayamba kukonda choonadi cha Baibulo kwambiri, ndipo ndinkafuna kubatizidwa. Mu August 1965 chikhumbo changa chinakwanira pamene ndinabatizidwa mu Mtsinje wa Olkhe, limodzi ndi Mboni zina zatsopano zimene zinabatizidwanso panthaŵiyo. Munthu wongoonera patali akanaganiza kuti tikungocheza kapena kusambira mumtsinje. Posakhalitsa ndinapatsidwa udindo wakukhala woyang’anira Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Ndiyeno mu November 1965, tinali okondwanso pamene tinaona Fyodor atamasulidwa kundende.
Mmene Ntchito Inapitira Patsogolo
Mu 1965 tonse othamangitsidwa kwathu tinasonkhana, ndiye analengeza kuti tinali aufulu kusamukira kwina kulikonse kumene tidakafuna, kuchoka pamudzi wathu umene ukanasanduka “mudzi wathu mpaka kalekale.” Tangoganizirani mmene tinasangalalira! Ena anasamukira kumbali zina zadzikolo, koma ena anasankha kungokhala pomwepo pamene Yehova anatidalitsira ntchito yathu ndi kutithandiza kukula mwauzimu. Ambiri mwa amenewo analera ana awo, adzukulu, ndi adzukulutuvi ku Siberia komweko, moti anazoloŵerako, samaonanso kuti kukuoopsa ngakhale pang’ono.
Mu 1967, ndinadziŵana ndi Maria, mtsikana amene makolo akenso anawathamangitsira ku Siberia kuchokera ku Ukraine. Pamene tinali ana, tinkakhala m’mudzi umodzi wa Vilshanitsa, ku Ukraine. Tinakwatirana mu 1968, ndipo tinadalitsidwa ndi mwana wamwamuna, Yaroslav, kenakanso mwana wamkazi, Oksana.
Tinapitirizabe kulimbikitsana mwauzimu titasonkhana pamaliro kapena paphwando laukwati. Pazochitika zimenezi m’pamenenso tinkafotokozera achibale ndi mabwenzi osakhala Mboni kuwauza choonadi cha Baibulo. Nthaŵi zambiri apolisi ankakhalapo pazochitika zimenezi, ndipo tinkalalikira momasuka kuti Baibulo limatipatsa chiyembekezo chakudzaona akufa akuukitsidwa; ikakhala nkhani ya ukwati, tinali kuwauza kuti Yehova ndiye anauyambitsa, ndi kulalikiranso za madalitso a m’tsogolo m’dziko lake latsopano.
Tsiku lina, nditangotsiriza kumene kukamba nkhani pamaliro, panafika galimoto, kenaka zitseko zake zinatseguka, ndiye mmodzi wa anthu amene analimo anatuluka n’kundilamula kuti ndiloŵe m’galimotoyo. Mtima wanga unali m’malo. Ndikadaopa chiyani ngati kuti tinali achifwamba? Tinali anthu okhulupirira Mulungu basi. Komabe, m’thumba mwanga munali malipoti a utumiki a anthu a mumpingo wathu. Ndikanamangidwa chifukwa cha zimenezo. Ndiye ndinapempha kuti asananditenge, ndim’patse kaye mkazi wanga ndalama. Ndiye onsewo akuyang’ana, ndinam’patsa mkazi wanga bwinobwino kachikwama kanga kam’manja limodzi ndi malipoti ampingowo.
Kuyambira mu 1974, ine ndi Maria tinayamba kukonza mabuku ophunzitsa za Baibulo m’nyumba mwathu. Poti tinali ndi mwana, kamnyamata, tinkachita zimenezo usiku kwambiri kuti iye asadziŵe. Komabe, iye ankafuna kudziŵa chinthu chilichonse, ndiye ankanamizira kugona ndipo ankatisuzumira kuti aone zimene tinali kuchita. Tsiku lina anati: “Ndikudziŵa amene amapanga magazini a Mulungu.” Tinachita mantha pang’ono, koma nthaŵi zonse tinkapempha Yehova kuti ateteze banja lathu pantchito yofunikayi.
Potsiriza, olamulira anafeŵa mitima, osadanso Mboni za Yehova, ndiye tinakonza msonkhano waukulu umene tinachitira muholo yamaseŵero ya Mir, mumzinda wa Usol’ye-Sibirskoye. Tinawalonjeza oyang’anira mzinda kuti pamisonkhano yathu timangophunzirapo Baibulo basi ndi kuyanjana ndi Akristu anzathu. Anthu oposa 700 anasonkhana mu January 1990, kudzaza holo yonseyo ndipo ambiri anaona zimenezo.
Msonkhanowo utatha, mtolankhani wina anafunsa kuti: “Kodi ana anuŵa munawaphunzitsa liti?” Iyeyo, limodzi ndi alendo ena anadabwa chifukwa choti iwo anali kumvetsera mwachidwi kwa maola anayi pamsonkhanowo. Posakhalitsa, m’nyuzipepala munatuluka nkhani yabwino kwambiri yokhudza Mboni za Yehova. Inati: “Munthu angaphunzirepo kanthu [kwa Mboni za Yehova].”
Kukondwera ndi Kupita Patsogolo kwa Ntchito
Mu 1991 tinali ndi misonkhano yachigawo isanu ndi iŵiri ku Soviet Union, imene panasonkhana anthu 74,252. Pamene mayiko omwe kale anali mbali ya Soviet Union anapeza ufulu, ndinapatsidwa ntchito ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova kuti ndipite ku Moscow. Nditafika kumeneko anandifunsa ngati ndingakonde kuwonjezera utumiki wanga pantchito ya Ufumu. Pamenepo n’kuti Yaroslav atakwatira ndipo ali ndi mwana wake, koma Oksana anali adakali mtsikana. Choncho mu 1993, ine ndi Maria tinayamba utumiki wanthaŵi zonse ku Moscow. Chaka chomwecho ndinaikidwa kukhala tcheyamani wa Malo Oyendetsa Ntchito a Magulu Achipembedzo a Mboni za Yehova ku Russia.
Tsopano ine ndi Maria tikukhala pa ofesi yanthambi yomwe ili kunja kwa St. Petersburg. Timagwiranso ntchito pomwepo. Ndikuona kuti kugwira ntchito ndi abale okhulupirika yosamalira olengeza Ufumu amene akuwonjezeka msanga ku Russia, ndi mwayi waukulu kwambiri. Lero kuli Mboni zoposa 260,000 m’mayiko omwe kale anali mbali ya Soviet Union, ku Russia kokha kuli zoposa 100,000!
Nthaŵi zambiri ine ndi Maria timakumbukira achibale ndi mabwenzi athu amene timakonda omwe akukhulupirikabe pa utumiki wawo wa Ufumu ku Siberia, dziko limene linangokhala ngati kumudzi kwathu kokondeka. Lero kumachitika misonkhano yaikulu kumeneko, ndipo Mboni 2,000 ku Irkutsk n’zokangalika. Indedi, ulosi wa Yesaya 60:22 wakuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu,” ukukwaniritsidwanso kumbali imeneyo yadziko.
[Chithunzi patsamba 20]
Mu 1959 ku Irkutsk, ndili ndi bambo wanga, banja lathu ndi anthu enanso, ku ukapolo
[Chithunzi patsamba 23]
Ana pamene anali pa ukapolo ku Iskra
[Chithunzi patsamba 25]
Chaka chimene tinakwatirana
[Chithunzi patsamba 25]
Lero, ndili ndi Maria