“Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
1-4. (a) Kodi ndim’mbali ziti za chithunzithunzi chathu chapachikuto zimene mukanakonda kusangalalamo? (b) Kodi nchiyembekezo chaulemelero chotani chimene chikusonyezedwa pamenepa kwa inu? (c) Kodi ndimalemba ena otani a Baibulo amene amachirikiza chiyembekezo chotero?
TAWONANI anthu achimwemwe pachikuto cha kabukhu kano. Kodi mungakonde kukhala mmodzi wa iwo? ‘Eya, inde,’ inu mukutero. Pakuti pano pali mtendere ndi chimvano zokhumbidwa ndi anthu onse. Anthu amafuko onse—akuda, oyera achikasu—akusanganikirana monga banja limodzi. Ha nchisangalalo chotani nanga! Ha nchigwirizano chotani nanga! Mwachiwonekere anthu amenewa saali odera nkhawa ndi kulakatika kwa nyukleya kapena chiwopsezo cha uchigawenga. Ndege zankhondo za jeti sizimaipitsa miyamba yamtendere pamwamba pa paki yokongola imeneyi. Kulibe asilikali, kulibe akasinja, kulibe mfuti. Sikufunika ngakhale ndodo ya wapolisi yosungitsira mtendere. Nkhondo ndi upandu kulibiretu. Ndipo palibe kuperewera kwa nyumba, pakuti aliyense ali ndi nyumba yokongola imene akuitcha kukhala yake.
2 Tangoyang’anitsitsani anawo! Kusewera kwawo nkokondweretsa kukuwona. Ha ndinyama zotani nanga zosewera nazo! Mulibe mipiringidzo yachitsulo imene ikufunika m’paki imeneyi, pakuti nyama zonse ziri pamtendere ina ndi inzake. Ngakhale mkango ndi mwana wa nkhosa zakhala mabwenzi. Tawonani mbalame zamawonekedwe okongola izo zimene zikuuluka chakuno ndi chauko, ndipo imvani nyimbo zawo zokongola zomvekera limodzi ndi kuseka zikudzadza m’mlengalenga. Kodi palibe zikwere? Ayi, chifukwa chakuti zonse nzaufulu ndi zachisangalalo chopanda malire muulamuliro uwu. Tangomvani kununkhira kwa maluwawo, imvani kuchita waa kwa mtsinjeko, imvani kuthumilira kwabwino kwadzuŵa. O, kukoma kwa zipatso ziri mumtangawo, pakuti ndizo zabwino kopambana zimene dziko lapansi lingatulutse, zabwino koposa, mofanana ndi chinthu chirichonse chimene chingawonedwe ndi kusangalala nacho m’munda wonga paki waulemelero umenewu.
3 ‘Koma taimani,’ wina angatero, ‘kodi anthu okalamba ali kuti? Kodi nawonso, sayenera kusangalala limodzi ndi chimangidwe chachimwemwe chimenechi?’ Kwenikweni, anthu okalamba ali momwemo, koma iwo abwerera ku unyamata. M’paki imeneyi palibe amene akufa ndi ukalamba. Achichepere tsopano akukula kukhala anthu achikulire koma osakalamba. Kaya akhale wazaka 20 kapena 200 zakubadwa, aliyense wa anthu mamiliyoni ambiri okhala ndi moyo m’paki iyi amasangalala ndi changu cha kukhala ndi moyo waunyamata, thanzi langwiro. Mukuti, mamiliyoni? Inde, mamiliyoni, chifukwa chakuti paki imeneyi ikufutukulidwira m’dziko lirilonse. Lidzazadzidwa ndi zamoyo, mtendere, ndi kukongola kufikira kumalekezero enieni a dziko lathu lapansili, kuchokera ku Fuji kufikira ku Andes, kuchokera ku Hong Kong kufikira ku Mediterranean. Pakuti dziko lonse lapansi likusandutsidwa Paradaiso wobwezeretsedwa padziko lonse lapansi.
4 Kodi imu munati, ‘Nzosakhulupiririka,’ Komabe choyamba talingalirani maumboni otsimikizirika. Kuli kothekera kwa inu ndi banja lanu kupulumuka kutha kwa dongosolo lovutitsidwa liripoli lazinthu ndi kulowa m’Paradaiso wosonyedzedwa pa chikuto chatu.a
Bukhu Limene Limalongosola Paradaiso
5. (a) Kodi ndi bukhu liti limene limalongosola zinthu zimenezi? (b) Kodi bukhuli liri lapadera m’njira zotani?
5 Zinthu zaulemerero zonsezi, ndi kutsimikizirika kwake, zalongosoledwa m’bukhu, bukhu labwino koposa onse amene analembedwapo. Limatchedwa Baibulo. Ndibukhu lakale kwambiri, mbali zake zinalembedwa zaka zokwanira 3 500 zapitazo. Panthawi imodzimodziyo, ndilo bukhu lamakono koposa m’kupereka uphungu wabwino, ndi wogwira ntchito m’moyo watsiku ndi tsiku wamakono. Maulosi ake amadzutsa chiyembekezo chowala kaamba ka mtsogolo. Ndilo bukhu logulitsidwa koposa onse m’mbiri, makope oposa 2 000 000 000 a Baibulo lathunthu kapena zigawo zake zazikulu afalitsidwa m’zinenero zokwanira 1 810.
6. Kodi nchiyani chimene chimalekanitsa Baibulo ndi mabukhu ena olingaliridwa kukhala opatulika?
6 Palibe bukhu lina lopatulika limene linakhalapo ndi kugawiridwa kofalikira kotero ndipo unyinji wa ena suuli wakale mofanana nalo. Korani Yachisilamu njazaka zosakwanira 1 400. Buddha ndi Confucius anakhala ndi moyo pafupifupi zaka 2 500 zapitazo, ndipo mabukhu awo akuyambira panthawi imeneyo. Malemba a Shinto analembedwa mumpangidwe wawo wamakono zosapitilira zaka 1 200 zapitazo. Bukhu la Mormon liri ndi zaka 160 zokha. Palibe lirilonse la mabukhu opatulika amenewa limene lingakhoze kulongosola molondola mbiri ya anthu kubwerera m’mbuyo ku zaka 6 000, monga momwe limachitira Baibulo. Chifukwa chake kuti tizindikire chipembedzo choyambirira, tiyenera kupita ku Baibulo. Ndilo bukhu lokha limene uthenga wake uli wa anthu onse.
7. Kodi nchiyani chimene anthu ophunzira anena ponena za Baibulo?
7 Nzeru ndi kukongola kwa uthenga Wabaibulo zatamandidwa ndi amuna anzeru ochokera kumitundu yonse ndi ochokera kuziyambi zonse za moyo. Wasayansi wina wotchuka amenenso anatulukira mphamvu yokoka, Bwana Isaac Newton, anati: “Palibe sayansi imene imachitiridwa umboni bwino kwambiri kuposa Baibulo.” Patrick Henry, mtsogoleri wa chipanduko cha Amereka wotchuka kaamba ka mawu ake akuti “Ndipatseni ufulu, kapena mundipatse imfa,” analengezanso kuti: “Baibulo liposa mabukhu ena onse amene analembedwapo.” Ngakhale wanthanthi wamkulu Wachihindu Mohandas K. Gandhi panthawi ina anauza bwanamkubwa Wachibritishi ku Indiya kuti: “Pamene dziko lanu ndi langa adzagwirizana pamodzi pa ziphunzitso zonenedwa ndi Kristu muulaliki wa Paphiri uwu, tidzakhala titathetsa mavuto, osati kokha amaiko athu komanso a dziko lonse.” Gandhi anali kulankhula za Mateyu mutu 5 kufikira 7 m’Baibulo. Dziwerengereni mitu imeneyi ndi kuwona ngati simukuchita chidwi ndi uthenga wake wamphamvu.
Baibulo—Bukhu la Kummaŵa
8, 9. (a) Kodi chifukwa ninji kuli kulakwa kunena kuti Baibulo liri bukhu la Kumadzulo? (b) Kodi ndimotani mmene Baibulo linalembedwera, ndipo mkati mwanyengo yanthawi yotani? (c) Kodi nchifukwa ninji Baibulo lingatchedwe laibulale? (d) Kodi ndi anthu angati amene anagwiritsiridwa ntchito kulemba Baibulo? (e) Kodi ndi umboni wotani umene ena a anthu amenewa amapereka ponena za magwero a Baibulo?
8 Mosiyana ndi chikhulupiriro chofala, Baibulo siliri chipatso cha kutsungula kwa Kumadzulo, ndiponso iro silimatamanda kutsungula kumeneko. Pafupifupi Baibulo lonse linalembedwera kumaiko a Kummaŵa. Amuna onse amene analilemba anali a Kummaŵa. Zaka chikwi chimodzi Buddha asanakhaleko, mu 1513 B.C.E., Mose, amene anakhala ku Middle East, anauziridwa ndi Mulungu kulemba bukhu loyamba Labaibulo, lotchedwa Genesis. Kuchokera pachiyambi chimenechi, Baibulo limalondola mutu wankhani umodzi wogwirizana kufikira kubukhu lake lomalizira la Chivumbulutso. Baibulo linamalizidwa mu 98 C.E., pafupifupi zaka 600 pambuyo pa Buddha. Kodi munali kudziwa kuti Baibulo nlopangidwa ndi mabukhu osiyanasiyana okwanira 66? Inde, Baibulo liri laibulale mwa iro lokha!
9 Motero, nyengo yoposa zaka 1 600 kuchokera m’nthawi ya Mose kumkabe mtsogolo, amuna okwanira 40 anakhala ndi phande m’kulemba cholembedwa chogwirizana Chabaibulo. Iwo akuchitira umboni kuti zolembedwa zawo zinauziridwa ndi mphamvu yapamwamba kwambiri kuposa munthu wokhoza kufa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulugu, ndipo lipindulitsa pa chiphuzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.”b (2 Timoteo 3:16) Ndipo mtumwi Petro analongosola kuti: ‘Palibe ulosi wa Lemba umene umachokera ku kutanthauzira kwamtseri kulikonse. Pakuti nthawi iriyonse ulosi sunadze mwa chifuniro cha munthu, koma anthu analankhula kuchokera kwa Mulungu pamene anasonkhezeredwa ndi mzimu woyera.’—2 Petro 1:20, 21; 2 Samueli 23:2; Luka 1:70.
10. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo lafikira mpaka tsiku lathu? (b) Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti tikali chikhalirebe ndimalemba pamanja oyambilira ouziridwa a Baibulo?
10 Chapaderanso kopambana, ndicho mmene Baibulo lakhalirapo mpaka lerolino. Kwa zaka zikwi zambiri, kufikira pa kutulukiridwa kwa kusindikiza pafupifupi zaka 500 zapitazo, makope Abaibulo anafunikira kulembedwa ndi manja. Palibe bukhu lina lirilonse la m’nthawi zikale limene linajambulidwa mwakhama kwambiri chotero ndi mobwerezabwereza. Iro linajambulidwa mobwerezabwereza, koma nthawi zonse mwachisamaliro chachikulu. Alembi anapanga zolakwa zazing’ono zowerengeka chabe ndipo kuyerekezeredwa kwa zimenezi kwatsimikizira malembo apamanja oyambirira kukhala ouziridwa ndi Mulungu. Katswiri wotchuka wa malembo apamanja Abaibulo, Bwana Frederick Kenyon, amati: “Maziko omalizira a chikaikiro chirichonse chakuti Malemba afika kwa ife ndendende monga momwe analembedwera tsopano achotsedwa.” Lerolino, pakali chikhalirebe makope pafupifupi 16 000 olembedwa pamanja a Baibulo kapena mbali zake, ena anakhalako ngakhale kuchokera m’zaka za zana lachiwiri Kristu asanadze. Komanso matembenuzidwe olondola apangidwa kuchokera kuzinenero Zachihebri, Zachiaramaiki, ndi Zachigiriki m’zimene Baibulo linalembedwa poyambirira ndiyeno kufalikira mu pafupifupi zinenero zonse za padziko lapansi.
11. Kodi nzotulukapo zamakono zotani zimene ziri zogwirizana ndi cholembedwa cha Baibulo?
11 Ena ayesa kutsutsa Baibulo mwa kunena kuti siliri lolondola. Komabe, m’zaka zaposachedwapa akatswiri ofukula mabwinja akumba mabwinja a mizinda yakalekale m’maiko Abaibulo ndipo apeza zilemba zozokotedwa ndi malo otchulidwa ngakhale m’zinenero zakalekale Zabaibulo kuti analikodi. Iwo afukula umboni wochuluka kwambiri wosonya ku chigumula cha dziko lonse, chimene Baibulo limanena kuti chinachitika zaka zoposa 4 000 zapita, m’tsiku la Nowa. Pamfundoyo, Prince Mikasa, katswiri wofukula mabwinja wotchuka kwambiri, analongosola kuti: “Kodi Chigumula chinalikodi? . . . Chenicheni chakuti chigumula chinalikodi chatsimikiziridwa mokhutiritsa maganizo.”c
Mulungu wa Baibulo
12. (a) Kodi nchiyani chimene oseka monyoza amanena ponena za Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji Baibulo limasonya kwa Mulungu monga Atate? (c) Kodi nchiyani chimene Baibulo limasonyeza kukhala dzina la Mulungu?
12 Monga momwedi anthu ena asekera monyozera za Baibulo, ena aseka monyoza ponena za kukhalako kwa Mulungu Wamphamvuyonse. (2 Petro 3:3-7) Iwo anati, ‘Kodi ndimotani mmene ndingakhulupirire Mulungu, popeza kuti sinditha kumuwona? Kodi pali umboni wakuti Mlengi wosawoneka, wapamwamba kuposa munthu, alikodi? Kodi Mulungu samakhala m’chinthu chirichonse?’ Ena amati,, ‘Kulibe Mulungu kapena Buddha.’ Komabe, Baibulo limasonyeza kuti monga momwedi tonsefe tinalandilira moyo kupyolera mwa atate wa dziko lapansi, chotero makolo athu oyambirira analandira moyo kuchokera kwa Atate wakumwamba, kapena Mlengi, amene dzina lakelake ndilo Yehova.—Salmo 83:18; 100:3; Yesaya 12:2; 26:4.
13. Kodi ndim’njira ziwiri zotani m’zimene Yehova wadzivumbulira iye mwini kwa anthu?
13 Yehova wadzivumbula yekha kwa anthu m’njira ziwiri zapadera. Njira yaikulu ndiyo kupyolera mwa Baibulo, limenele limadziwikitsa chowonadi chake ndi zifuno zake zosatha. (Yohane 17:17; 1 Petro 1:24, 25) Njira ina ndiyo kupyolera mwa chilengedwe chake. Mwa kuwona zinthu zodabwitsa zowazungulira, anthu ambiri afikira pozindikira kuti Mlengi ndi Mulungu ayenera kukhalapo amene umunthu wake waukulu wasonyezedwa m’ntchito zake.—Chivumbulutso 15:3, 4.
14. Kodi Baibulo limatiuza chiyani ponena za Yehova?
14 Yehova Mulungu ndiye Woyambitsa Baibulo. Iye ndiye Mzimu Waukulu, wokhalako ku umuyaya wonse. (Yohane 4:24; Salmo 90:1, 2) Dzina lake lakuti “Yehova” limasonya ku chifuno chake kulinga ku zolengedwa zake. Chiri chifuno chake kulemekeza dzina lalikulu limeneli mwa kuwononga oipa ndi kuwombola awo amene amamkonda kotero kuti akhale ndi moyo padziko lapansi laparadaiso. (Eksodo 6:2-8; Yesaya 35:1, 2) Pokhala Mulungu Wamphamvuyonse, iye ali ndi mphamvu ya kuchita ichi. Monga Mlengi wa chilengedwe chonse iye ali pamwambamwamba pa milungu wamba ya amitundu ndi mafano.—Yesaya 42:5, 8; Salmo 115:1, 4-8.
15. Kodi kufufuzidwa kwa chilengedwe kochitidwa ndi anthu aluntha kwatsogolera ku zotulukapo zotani?
15 Mkati mwa zaka za mazana aposachedwapa, amuna asayansi awonongera nthawi yaikulu kupenda ntchito za chilengedwe. Kodi iwo anenanji? Mmodzi wa akalambulabwalo m’ntchito zamagetsi, wokhulupirira zinthu zakuthupi wodziwika kwambiri Wachibritishi Lord Kelvin, analengeza kuti: “Ndikhulupirira kuti pamene sayansi iphunziridwa mosamalitsa ndipamenenso ikutichotsa kuchinthu chirichonse choyerekezeredwa ndi kusakhulupirira mwa Mulungu.” Wasayansi wobadwira ku Ulaya Albert Einstein, ngakhale kuti amalingaliridwa kukhala wosakhulupirira mwa Mulungu, anavomereza kuti: “Kuli kokwanira kwa ine . . .kusinkhasinkha mpangidwe wodabwitsa wa chilengedwe, chimene tingathe kulingalira mwachizimezime, ndi kuyesayesa modzichepetsa kuzindikiradi mbali yochepetsetsa koposa ya chisonyezero cha luntha m’chilengedwe.” Wasayansi wa ku Amerika ndi wopambana mphotho ya Nobel Arthur Holly Compton anati: “Chilengedwe chadongosolo chovumbulutsidwa mosalekeza chimachitira umboni chowonadi cha mawu amtengo wapatali kwambiri kuposa onse amene ananenedwapo akuti—‘Pachiyambi Mulungu.’” Iye anali kugwira mawu oyambirira Abaibulo.
16. Kodi ndimotani mmene chilengedwe chonse chimalemekezera nzeru ndi mphamvu zolenga za Mulungu?
16 Olamulira a mitundu yamphamvu angadzitamandire kaamba ka luntha lawo ndi zipambano zasayansi m’kugonjetsa kutali mumlengalenga. Koma ha masetilaiti awo a mumlengalenga ngosanunkha kanthu chotani nanga pamene ayerekezeredwa ndi mwezi umene umazungulira dzuŵa! Ha nzochepetsetsa chotani nanga zipambano za anthu okhoza kufa amenewa poyerekezeredwa ndi chilengedwe cha Yehova cha makamu a nyenyezi ambiri a madzuŵa ofanana ndi lathu, ndi kuwaika kwake pamodzi ndi kuwakhazikitsa mumlengalenga kwanthawi yosayezeka! (Salmo 19:1, 2; Yobu 26:7, 14) Mposadabwitsa kuti Yehova amawona anthu mofananadi ndi ziwala, ndipo amitundu amphamvu ‘kukhala chabe.’—Yesaya 40:13-18, 22.
17. Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kukhulupirira Mlengi?
17 Kodi inu mumakhala m’nyumba? Mwinamwake simunamange nyumbayo inumwini, ndipo mwinamwake simumadziwa amene anatero. Komabe, chenicheni chakuti simumadziwa woimanga sichikanakulepheretsani kuvomereza chowonadi chakuti munthu wina waluntha anaimanga. Kulingalira kuti nyumbayo inadzimanga yokha kukanawonekera kukhala kupusa kwambiri! Popeza kuti chilengedwe chachikulu ndi zonse ziri mmenemo, chinafunikiritsa luntha lalikulu kwambiri lopanda polekezera kuti chipangidwe, kodi sikuli kwanzeru kutsimikiza kuti payenera kukhala Mlengi Waluntha? Ndithudi, nchitsiru chokha chimene chikanena mumtima mwake kuti, “Kulibe Yehova.”—Salmo 14:1; Ahebri 3:4.
18. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Mulungu ndimunthu, ndipo ngwoyenelera kutamandidwa?
18 Zozizwitsa zaulemerero zimene zatizungulira—maluwa, mbalame, nyama cholengedwa chozizwitsa chotchedwa munthu, zozizwitsa za moyo ndi kubadwa—zonsezi zimachitira umboni Mmisiri Waluntha wosawoneka amene anazipanga. (Aroma 1:20) Pamene pali luntha, pali maganizo, pamene pali maganizo, pali munthu. Nzeru yaikulu ndiyo ya Munthu Wamkulukulu, Mlengi wa zinthu zonse zamoyo, Chitsime chenicheni cha moyo. (Salmo 36:9) Mlengi alidi woyenerera chitamando chonse ndi ulemu.—Salmo 104:24; Chivumbulutso 4:11.
19. (a) Kodi nchifukwa ninji palibe mtundu lerolino umene ungadzinenere kukhala ndichipambano choperekedwa ndi Mulungu m’nkhondo? (b) Kodi nchifukwa ninji Mulungu alibe mbali m’nkhondo za amitundu?
19 Pali ena emene chikhulupirliro chawo mwa Mulungu chinagwedezedwa ndi zokumana nazo zovutitsa maganizo za Nkhondo Yadziko II. Panthawiyo dziko lirilonse linaitanira pa “Mulungu” wake, kaya wa zipembedzo za Chikatolika kapena Chiprotestante kapena zipembedzo za Kummawa. Kodi kunganenedwe kuti “Mulungu” anapereka chilakiko kwa ina ya mitundu imeneyi nalola ina kugonjetsedwa? Baibulo limasonyeza kuti palibe uliwonse wa mitundu imeneyi umene unaitanira pa Mulungu wowona. Yehova Mulungu, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, sali ndi thayo la chisokonezo ndi nkhondo pakati pa Amitundu. (1 Akorinto 14:33)Maganizo ake ali pamwamba kwambiri pa amitundu andale zadziko ndi okonda kuchita nkhondo a dziko lino. (Yesaya 55:8, 9) mofananamo, chipembedzo chowona ndi kulambiridwa kwa Yehova kulibe mbali m’nkhondo za amitundu. Yehova ngwapamwamba kwambiri koposa milungu yautundu. Iye ngwapadera m’kukhala Mulungu wa amuna ndi akazi okonda mtendere m’mitundu yonse. Monga momwe Baibulo limanenera kuti: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Anthu okonda chilungamo m’mitundu yonse tsopano akuphunzira Baibulo ndipo akuvomereza kulambiridwa kwa ‘Mulungu wowona wopereka mtendere,’ Mlengi wa anthu onse.—Aroma 16:20; Machitidwe 17:24-27.
20. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza Dziko Lachikristu kukhala lachikunja ndi lokana Mulungu?
20 Anthu ena amosonya kukugawanika ndi chinyengo m’zipembedzo za Dziko Lachikristu, zimene zimadzinenera kukhala zikutsatira Baibulo. Iwo amanenanso kuti, ‘Kodi ndingakhulupilire motani Mulungu wa Baibulo, pamene mitundu imene iri ndi Baibulo iri pakuti pa younjika mokangalika zida zankhondo zanyukliya?’ Chenicheni nchakuti, pamene kuli kwakuti nthawi zonse Baibulo nlowona, mitundu ya Dziko Lachikristu yafikira kukhala yotalikirana ndi Chikristu cha Baibulo monga momwe kumpoto kuliri kotalikirana ndi kummwera. Iwo ngonyenga mwa kudzinenera kukhala ogwiritsira ntchito Chikristu. Iwo ali ndi Baibulo, koma samamvera ziphunzitso zake. Prezidenti wa Amereka amene analamula kuponyeredwa bomba loyamba pa Hiroshima panthawi ina anadzuma kuti: “Ha, kaamba ka Yesaya kapena St. Paul (Paulo woyera)!”—kutsogoza anthu kudziko la mavuto lino. Iye akanavomerezana ndi Yesaya Wabaibulo, sakanaponya konse bomba la atomu, chifukwa chakuti Yesaya anavomereza ‘kusula malupanga kukhala zolimira ndi mikondo kukhala anagwape.’ Ndiponso, anali Paulo Wabaibulo amene analengeza kuti: “Sitichita nkhondo monga mwathupi, pakuti zida zankhondo yathu siziri zathupi.” (Yesaya 2:4; 2 Akorinto 10:3, 4) Komabe, mmalo mwa kutsatira uphungu wanzeru Wabaibulo, mitundu ya Dziko Lachikristu yafikira kukhala yophatikizidwa mumpikisano wa kudzipha wa zida zankhondo. Kudzinenera kulikonse kwakuti ali Akristu omvera Baibulo nkwabodza. Iwo ayenera kuyang’anizana ndi chiweruzo cha Mulungu kaamba ka kulephera kuchita chifuniro chake.—Mateyu 7:18-23; Zefaniya 1:17, 18.
Chilengedwe cha Yehova ndi Zozizwitsa
21. Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kusakaikira zozizwitsa za Mulungu?
21 Yehova amalenga, ndipo amachita zozizwitsa. Kodi munayamba mwadabwapo za kusanduliza madzi kukhala mwazi, kulekanitsidwa kwa Nyanja Yofiira, kubadwa kwa Yesu mwa namwali, ndi zozizwitsa zina zolembedwa m’Baibulo? Popeza kuti munthu ngwochepekedwa m’mphamvu ya kulingalira, mwinamwake iye sadamvetsetse mmene zina za zozizwitsa zimenezi zinachitikira, mofanana ndi mmene sangamvetsetsere mokwanira chozizwitsa cha kutuluka ndi kulowa kwa dzuwa tsiku lirilonse. Kulengedwa kwa munthu chinali chozizwitsa. Munthu wamakono sanawone chozizwitsa chimenecho, koma amadziwa kuti icho chinachitika, pakutingwamoyo lerolino kuchitsimikizira. Ndithudi, moyo wonse ndi chilengedwe chonse zimapanga chozizwitsa chimodzi chosatha. Motero kodi tiyenera kukaikira pamene Mawu a Mulungu, Baibulo, limanena kuti analenga zozizwitsa zapadera kaamba ka nthawi zapadera, ngakhale kuti palibe kufunikira kwa zozizwitsa zimodzimodzizo lerolino?
22. Longosolani cholengedwa choyamba cha Mulungu.
22 Cholengedwa chirichonse cha Yehova nchozizwitsa ndi chodabwitsa! Komabe, cholengedwa chake choyambilira chenicheni chinali chozizwitsa koposa zonse. Chinali cholengedwa cha Mwana wake wauzimu, ‘wobadwa wake woyamba.’ (Akolose 1:15) Mwana wakumwamba ameneyu anatchedwa “Mawu.” Zaka zosawerengeka pambuyo pa kulengedwa kwake, anadza padziko lino lapansi nadzatchedwa “munthu, Kristu Yesu.” (1 Timoteo 2:5) Pamenepo kunanenedwa za iye kuti: “Ndipo Mawu anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinawona ulemelero wake, ulemelero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.”—Yohane 1:14.
23. (a) Kodi ndimotani mmene unansi wa pakati pa Mulungu ndi Mwana wake ungalongosoledwere? (b) Kupyolera mwa Mwana wake, kodi Yehova analenga chiyani?
23 Unansi wa Yehova ndi Mwana wake ungayerekezeredwe ndi wa manijala yemwenso ali mwini kampani ndi mwana wake wamwamuna m’wekishopo, mmene mwana wamwamunayo amathandiza kupanga zinthu zolinganizidwa ndi atate wake. Kupyolera mwa Mwana wake wobadwa yekha ndi wantchito mnzake, Yehova analenga zolengedwa zina zauzimu, ana a Mulungu. Pambuyo pake, zimenezi zinasangalala kuwona Mwana wa Yehova, Mmisiri wake, akutulutsa miyamba yeniyeni ndi dziko lapansi limene tikukhalamo. Kodi mukukaikira kuti zinthu zimenezi zinalengedwa? Zaka zikwi zambiri pambuyo pake, Yehova anafunsa mwamuna wina wokhulupirika kuti: “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira. Muja nyenyezi zammaŵa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?”—Yobu 38:4, 7; Yohane 1:3.
24. (a) Kodi ndicholengedwa chapadziko lapansi chotani chimene chiri chapadera, ndipo m’mbali zotani? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kupanda nzeru kunena kuti munthu anasinthira kuchokera ku zinyama?
24 M’kupita kwanthawi, Yehova analenga zinthu zamoyo, zakuthupi padziko lino lapansi, zomera, mitengo, maluŵa, nsomba, mbalame, ndi zinyama. (Genesis 1:11-13, 20-25) Ndiyeno Mulungu anati kwa Mmisiri wakeyo: “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu . . . Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye, adawalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” (Genesis 1:26, 27) Pokhala atalengedwa m’chifanizo ndi m’chifanefane cha Mulungu, limodzi ndi mikhalidwe yaikulu ya Mulungu ya chikondi, nzeru, chilungamo, ndi mphamvu, mwamuna woyambilira anali wapamwamba koposa zinyama. Munthu ali m’kagulu kapadera kusiyana ndi zinyama m’chakuti iye ali wokhoza kulingalira, iye angakhoze kulinganiza mtsogolo, ndipo ali ndi luso la kulambira Mulungu. Nyama ziribe nzeru zolingalira nazo, koma zimadalira pa chibadwa. Ha nkupusa kotani nanga kunena kuti kulibe Mlengi koma kuti cholengedwa chaumunthu chopatsidwa nzeru kwakukulukulucho, chinasinthika kuchokera ku nyama zopanda nzeru zotsika!—Salmo 92:6, 7; 139:14.
25, 26. (a) Kodi nchiyembekezo chabwino kwambiri chotani chimene chinaikidwa pamaso pa munthu? (b) Kodi nchifukwa ninji sipakanakhala vuto la kukhala ndi anthu ochulukitsitsa padziko lapansi?
25 Mulungu anaika munthu “m’munda wa Edene, cha kummaŵa.” Unali munda wachisangalalo, wofanana ndi munda umene uli pachikuto chathuwo, ngakhale kuti panthawiyo panali anthu awiri okha, Adamu ndi mkazi wake. Paradaiso woyambilira ameneyu sakupezekanso, pokhala atawonongedwa m’Chigumula cha tsiku la Nowa. Koma malo ake oyerekezeredwa m’Middle East ngodziwika, chifukwa chakuti mitsinje ina yotchulidwa m’Baibulo kukhala ikuyenda kudzeramo iripo kufikira lerolino. (Genesis 2:7-14)Munthu anali ndi mwayi wapadera wa kugwiritsira ntchito munda uwu monga malo apakati oyambirapo kufutukula ndi kulima dziko lonse lapansi, kulipanga kukhala paradaiso wa padziko lonse.—Yesaya 45:12, 18.
26 Popeza kuti awiri onsewo Mulungu ndi Mwana wake ngogwira ntchito, choteronso Mulungu anapatsa munthu ntchito yoichita pano padziko lapansi. (Yohane 5:17) Kwa Adamu ndi Hava, mwamuna ndi mkazi woyamba, iye anati: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa padziko lapansi.” (Genesis 1:28) Kodi ichi chinatanthauza kuti munthu akachuluka, kudzadza dziko lapansi, ndiyeno kupitirizabe kuchuluka kufikira dziko lapansi litadzala mpaka kusefukira? Ayi. Pamene munthu wina akuuzani kudzaza kapu ndi tii, inu simumapitirizabe kuthira kufikira tiiyo atasefukira m’kapu kutaikira pagome lonse. Mumadzaza kapuyo ndiyeno mumaleka. Mwanjira yofananayo, lamulo la Yehova kwa munthu lakuti, ”Mudzaze dziko lapansi,” linasonyeza chifuno chake cha kudzaza moyenelera dziko lapansi, ndiyeno kubalana kwa anthu pano padziko lapansi kukanaleka. Ichi sichikanakhala vuto konse m’chitaganya cha anthu angwiro. Ndimo m’dziko la anthu opanda ungwiro lalerolino mmene kuchulukitsitsa kwa anthu kuli vuto.
Zinthu Zoipa—Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Amazilola?
27. Kodi ndimafunso otani amene tsopano afunikira yankho?
27 Ngati chifuno cha Mulungu ndicho kupanga dziko lapansi laparadaiso, kodi ndimotani kuti dziko lapansi lerolino liri lodzala motero ndi kuipa, kuvutika, ndi chisoni? Ngati Mulungu ali Wamphamvuyonse, kodi nchifukwa ninji waloleza mikhalidwe imeneyi kwanthawi yaitali kwambiri? Kodi pali chiyembekezo cha kutha kwa mavuto athu onse? Kodi Baibulo limanenanji?
28. Kodi ndimotani mmene chipanduko chinalowerera m’munda wa Paradaiso?
28 Baibulo limasonyeza kuti mavuto a anthu anayamba pamene mmodzi wa ana a Mulungu anapandukira ufumu wa Yehova, kapena ulamuliro. (Aroma 1:20; Salmo 103:22, mawu amtsinde a NW Ref. Bi.) Mosakaikira mngelo ameneyu anali pakati pa awo amene anasangalala atawona kulengedwa kwa munthu. Komano msiliro ndi kunyada zinakula mumtima mwake, ndipo anakopedwa ndi chilakolako cha kuchititsa Adamu ndi Hava kumlambira mmalo mwa Mlengi wawo, Yehova. Polankhula kupyolera mwa njoka, monga momwedi katswiri wolankhula atatseka pakamwa amalankhulira kupyolera mwa chinthu chosalankhula, mngelo ameneyu ananyenga Hava kusamvera Mulungu Wamphamvuyonse. Pamenepo mwamuna wake Adamu anamtsatira m’kusamvera kwake.—Genesis 2:15-17; 3:1-6; Yakobo 1:14, 15.
29. (a) Kodi ndinkhani zotani zimene zinabuka zofunikira chosankha? (c) Kodi ndimotani mmene inu mungakhalire ndi phande m’kupereka yankho ku kutonza kwa Satana?
29 Mngelo wopanduka ameneyu anafikira podziwika monga “Njoka yoyambilira.” (Chivumbulutso 12:9; 2 Akorinto 11:3) Iye amatchedwanso Satana, kutanthauza “wotsutsa,” ndi Mdyerekezi, kutanthauza “Woneneza.” Iye anakaikira kuyenera ndi kulungama kwa ulamuliro wa Yehova padziko lapansi, ndipo anatokosa Mulungu kuti tsopano iye, Satanayo, akanafufunula anthu onse kukulambira kowona. Mulungu walola Satana zaka zokwanira 6,000 kuyesa kutsimikizira chitokoso chake, kotero kuti nkhani yonena za ufumu wa Yehova ithetsedwe kwamuyaya wonse. Ulamuliro wa munthu wosadalira pa Mulungu walephera momvetsa chisoni. Koma amuna ndi akazi achikhulupiliro, pakati pa amene Yesu anali chitsanzo chapadera, asunga umphumphu kwa Mulungu pansi pa ziyeso zankhalwe koposa, kulemekeza Yehova ndi kutsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza. (Luka 4:1-13; Yobu 1:7-12; 2:1-6; 27:5) Nanunso, mungakhale wosunga umphumphu. (Miyambo 27:11) Koma Satana sindiye mdani yekha amene amatizunza. Kodi pali mdani wina uti?
Mdaniyo—Imfa
30. Kodi nchiyani chimene Malemba amanena ponena za chilango chimene chikatulukapo kwa munthu chifukwa cha kusamvera?
30 Mulungu anali atalongosola chilango cha kusamvera—imfa. Popereka chilango kwa mkazi woyambayo, Yehova anati: “Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” Kwa mwamunayo Adamu iye anati: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka; chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:16-19) Awiri okwatirani osamverawo anathamangitsidwa m’Paradaiso wachimwemwe kumka m’dziko lapansi losalimidwa. M’kupita kwanthawi iwo anafa—Genesis 5:5.
31. Kodi tchimo nchiyani, ndipo kodi chotulukapo chake chakhala chiyani kwa anthu?
31 Kunali kokha pambuyo pa kuphonya kwawo chizindikiro cha ungwiro kuti Adamu ndi Hava anayamba kubala ana. Anthu onse lerolino ali mbadwa zawo m’kupanda ungwiro, ndipo chotero onse amafa. Wolemba Baibulo wina akulongosola mfundoyi m’mawu awa: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi mwa imfa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” Kodi nchiyani chimene chiri “uchimo” umenewu? Ndiwo kuperewera pa chizindikiro cha ungwiro kapena kukwanira. Yehova Mulungu samavomereza chinthu chirichonse kapena kuchisungabe chiri moyo chimene chiri chopanda ungwiro. Popeza kuti anthu onse alandira cholowa cha uchimo ndi kupanda ungwiro kuchokera kwa mwamuna woyamba Adamu, imfa yakhala ‘ikulamulira monga mfumu’ pa iwo. (Aroma 5:12, 14) Munthu wochimwa amafa, mofanana ndi mmene zinyama zimafera.—Mlaliki 3:19-21.
32. Kodi Baibulo limalongosola motani imfa imene tailandira mwacholowa?
32 Kodi nchiyani chimene chiri “imfa” imeneyi? Imfa ndiyo kusiyana ndi moyo. Mulungu anaika pamaso pa munthuyo chiyembekezo cha moyo wopanda mapeto padziko lapansi ngati anamvera. Komabe, iye sanamvere, ndipo chilangocho chinali imfa, kusazindikira, kusakhalako. Mulungu sananene kanthu ponena za kusamutsira moyo wa munthu kuchigawo chamizimu kapena ku “helo” wamoto ngati iye sanamvera ndiyeno kufa. Iye anachenjeza munthuyo kuti: “Udzafa ndithu.” Anali Mdyerekezi wakupha munthuyo amene adanama mwa kunena kuti: “Kufa simudzafai.” (Genesis 2:17; 3:4; Yohane 8:44) Chimene anthu onse alandira monga cholowa kuchokera kwa Adamu ndicho imfa ya kukhala ngati fumbi.—Mlaliki 9:5, 10; Salmo 115:17; 146:4.
33. (a) Kodi ndimtsogolo maulemerero motani mmene mukuyembekezera anthu ndi dziko lapansi iri? (b) Kodi ndizinthu zitatu zofunika zotani zimene Yehova amachita kupyolera mwa Mwana wake?
33 Pamenepo, kodi palibe mtsogolo kaamba ka munthu amene wafa? Pali mtsogolo modabwitsa! Baibulo limasonyeza kuti chifuno cha Mulungu cha paradaiso wa padziko lapansi kaamba ka anthu onse, kuphatikizapo awo amene tsopano ali akufa, sichidzalephera konse. Yehova amati: “Kumwamba ndimpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndichoikapo mapazi anga.” (Yesaya 66:1; 60:13) Chifukwa cha chikondi chake chachikulu, Yehova anatumiza Mwana wake, Mawuyo, kudziko lino lapansi, kuti dziko la mtundu wa anthu lipeze moyo kupyolera mwa iye. (Yohane 3:16; 1 Yohane 4:9) Pali zinthu zitatu zofunika zimene tsopano tiyenera kuzilongosola ndi zimene Yehova amachita kupyolera mwa Mwana wake, ndiko kuti, (1) Kupereka chimasuko kuchokera kumphamvu ya imfa; (2) Kubwezeretsadi akufa ku moyo; ndi (3) .kukhazikitsa boma langwiro pa mtundu wonse wa anthu.
Chimasuko ku Imfa
34, 35. (a) Kodi munthu akawomboledwa ku imfa kokha motani? (b) Kodi dipo nchiyani
34 Kuyambira nthawi zakale, aneneri a Mulungu asonyeza chidaliro chawo, osati m’kusakhoza kufa kwa munthu, koma m’chiyembekezo chakuti Mulungu ‘akawawombola’ kuchokera kuimfa. (Hoseya 13:14) Koma kodi ndimotani mmene munthu akamasuliridwa kunsinga za imfa? Chilungamo changwiro cha Yehova chinafunikiritsa ‘moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino.’ (Deuteronomo 19:21) Chotero, popeza kuti Adamu anadzetsa imfa ya cholowa pa anthu onse mwa kusamvera Mulungu mwadala ndipo motero kutaikiridwa ndi moyo wangwiro waumunthu, munthu wina wangwiro anafunikira kulowa mmalo Adamu m’kulipira moyo wake wangwiro, kuwombola chimene Adamu anataya.
35 Lamulo lamakhalidwe abwino la chilungamo la kulipira ‘chofanana kaamba ka chofanana’ lakhala lolandiridwa m’mbiri yonse. Mawu ogwiritsiridwa nchito mofala ndiwo “mtengo wolipilira dipo.” Kodi dipo nchiyani? Ndilo “mtengo wolipilidwa kulipilira munthu kapena chinthu kwa munthu amene wasunga munthuyo kapena chinthucho muukapolo. Chotero akaidi ankhondo kapena akapolo amanenedwa kukhala owomboledwa pamene amasulidwa mosinthanitsa ndi mphotho yamtengo wapatali. . . . chirichonse chimene chimalowetsedwa mmalo kapena kusinthanitsidwa ndi munthuyo ndicho dipo lake.”d Kuyambira pa uchimo wa Adamu, anthu onse akhala ofanana ndi akaidi ankhondo kapena akapolo, omangika ndi kupanda ungwiro ndi imfa. Kuti awawonjole, dipo linafunikira kuperekedwa. Kupewa mkangano uliwonse tsopano kapena mtsogolo ponena za kulinganira kwa mtengo wadipo, kukakhala kofunika kupereka nsembe moyo waumunthu wangwiro umodzi, ndiko kuti, wofanana ndendende ndi Adamu.
36. Kodi ndimotani mmene Yehova anaperekera moyo waumunthu wangwiro monga dipo?
36 Komabe, kodi moyo waumunthu wangwiro woterowo ukanapezeka kuti? Anthu onse, monga mbadwa za Adamu wopanda ungwiro, abadwa ali opanda ungwiro. ‘Kuwombola mbale sangamuwombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.’ (Salmo 49:7) Kukwaniritsa chofunikacho, Yehova, mosonkhezeredwa ndi kukonda kwake kwakuya mtundu wa anthu, kwenikweni anapereka mwana wake “wobadwa yekha” wamtengo wapataliyo kukhala nsembe yofunika. Iye anasamutsira moyo wangwiro wa Mwana wake wauzimu, Mawu, m’mimba ya namwali Wachiyunda, Mariya. Namwaliyo anakhala ndi pakati, ndipo m’nyengo yokwanira anabala mwana wamwamuna, amene anadzatchedwa “Yesu.” (Mateyu 1:18-25) Mwachiwonekere Mlengi wa moyo akanakhoza kuchita chozizwitsa chotero.
37. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera chikondi kwa anthu onse okhumba moyo?
37 Yesu anakula kukhala mwamuna wachikulira, anadzipereka kwa Yehova, ndipo anabatizidwa. Pamenepo Mulungu anamlamulira kuchita chifuniro Chake. (Mateyu 3:13, 16, 17) Popeza kuti moyo wa padziko lapansi wa Yesu unachokera kumwamba ndipo anali wangwiro, akanakhoza kupereka nsembe moyo waumunthu wangwiro umenewu, akumaugwiritsira ntchito kumasulira anthu kuimfa. (Aroma 6:23; 5:18, 19) Monga momwe iyemwini ananenera kuti: “Ndadza ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.” “Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” (Yohane 10:10; 15:13) Pamene Satana anachititsa Yesu kuphedwera pamtengo wozunzirapo, Yesu anagonjera ku imfa yankhalwe iyi, akumadziwa kuti anthu osonyeza chikhulupiliro akapeza moyo kupyolera mwa kakonzedwe ka dipo kameneka.—Mateyu 20:28; 1 Timoteo 2:5, 6.
Kubwezeretsedwera ku Moyo
38. Kodi ndimotani mmene Mwana wa Mulungu anabwezeretsedwera ku moyo, ndipo kodi nchiyani chimene chatsimikizira ichi?
38 Ngakhale kunali kwakuti adani ake anamupha, Mwana wa Mulungu sanataye konse kuyenera kwake kwa moyo wangwiro waumunthu, pakuti iye anasunga umphumphu wake kwa Mulungu. Komabe, pokhala wakufa m’manda, kodi ndimotani mmene Yesu akadagwiritsirira ntchito chinthu chamtengo wake chimenechi, kuyenera kwa moyo waumunthu, ku ubwino wa mtundu wa anthu? Ndipanopa pamene Yehova anachita chozizwitsa china, choyamba cha mtundu uwu. Patsiku lachitatu la kukhala kwa Yesu m’manda, Yehova anamuukitsa kuchokera ku imfa monga cholengedwa chauzimu, chosakhoza kufa. (Aroma 6:9; 1 Petro 3:18) Kuti akhazikitse chikhulupiliro m’chiukiriro, Yesu anadziveka matupi aumunthu ndi kuwonekera kwa ophunzira ake pa zochitika zosiyanasiyana, panthawi imodzi kwa 500 a iwo ndi kuposerapo. Palibe aliyense wa amenewa, kapena mtumwi Paulo amene pambuyo pake anachititsidwa khungu mwa kawonekedwe ka Yesu wolemekezedwayo, amene anali ndi chifukwa chirichonse chokaikirira chozizwitsa cha chiukiriro chake.—1 Akorinto 15:3-8; Machitidwe 9:1-9.
39. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu amagwiritsirira ntchito mtengo wa nsembe yake, ndipo choyamba kwa ayani? (b) Kodi ndizachozizwitsa chachikulu chotani chimene Yesu analankhula?
39 Patapita masiku 40 Yesu woukitsidwayo anakwera kumwamba pamaso penipeni pa Mulungu m’miyamba, kumeneko kukapereka mtengo wa nsembe yake yangwiro yaumunthu monga chomasulira anthu onse. “Koma iye, mmene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala padzanja lamanja la Mulungu chikhalira; kuyambira pomwepo alindilira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando kumapazi ake.” (Ahebri 10:12, 13) Oyambilira kumasulidwa kupyolera mwa dipo limeneli ndiwo “kagulu ka nkhosa” ka Akristu okhulupirika “amene ali kwa Kristu.” (Luka 12:32; 1 Akorinto 15:22, 23) Amenewa ali “ogulidwa kuchokera pakati pa anthu,” ndipo chotero pa chiukiriro iwo amafikira kukhala ogwirizana naye auzimu a Kristu m’miyamba. (Chivumbulutso 14:1-5) Komabe, bwanji za unyinji wa anthu amene tsopano amagona muimfa m’manda mwawo? Pamene anali padziko lino lapansi, Yesu ananena kuti Atate wake anali atampatsa ulamuliro wakuweruza ndi kupereka moyo. Iye anawonjezera kuti: “Musazizwe ndi ichi, pakuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, . . . kukuuka.” (Yohane 5:26-29) Iye adzabwezeretsa amenewa ku moyo m’Paradaiso padziko lapansi.
40, 41. (a) Longosolani chimene kwenikweni chimatanthauzidwa mwa mawu akutiwo “chiukiriro.” (b) Kodi nchifukwa ninji tingakhale ndi chikhulupiriro mu lonjezo la Mulungu la chiukiriro?
40 Tamvetserani mawu a Yesu akutiwo, “Musazizwe ndi ichi.” Ngakhale ziri choncho, kodi ndimotani mmene munthu wofa kalekale angamasulidwire kuimfa ndi kubwezeretsedwera ku moyo? Kodi thupi lake silinabwerere kufumbi? Ziwalo zina zimene zinapanga thupilo zingakhaledi zitalowa m’zamoyo zina, monga ngati zomera ndi zinyama. Komabe, chiukiriro sichimatanthauza kubwezeretsa ziwalo zimodzimodzizo kachiwirinso. Chimatanthauza kuti Mulungu amalenganso munthu yemweyo, wokhala ndi umunthu umodzimodziwo. Iye amalenga thupi latsopano kuchokera kuzipangizo za padziko lapansi, ndipo m’thupilo amaikamo mikhalidwe imodzimodziyo, mikhalidwe yosiyanitsa imodzimodziyo, chikumbukiro chimodzimodzicho, chitsanzo cha moyo chimodzimodzicho chimene munthuyo anali atapanga kufikira podzafika nthawi ya imfa yake.
41 Mwinimwake munakhalapo ndi chokumana nacho chakuti nyumba yanu imene munakonda kwambiri inatenthedwa. Komabe, inu mukanachititsa mosavuta kumangidwanso kwa nyumba imodzimodziyo, chifukwa chakuti chitsanzo cha mikhalidwe yake yokondweretsa nchowonekera bwino kwambiri m’chikumbukiro chanu. Pamenepa, ndithudi, Mulungu amene ali Muyambi wa chikumbukiro angathe kulenganso anthu amene wawasunga m’chikumbukiro chake chifukwa chakuti anawakonda. (Yesaya 64:8) Chimenechi ndicho chifukwa chake Baibulo limagwiritsira ntchito mawu akuti ‘manda a chikumbukiro.’ Pamene ifikira kukhala nthawi yoikika ya Mulungu yakubwezeretsa akufa ku moyo kachiwirinso, iye adzachita chozizwitsa chimenecho, monga momwedi anachitira chozizwitsa polenga munthu woyamba, koma pali panthawi ino yokha pamene adzachichita nthawi zambiri mobwerezabwereza.—Genesis 2:7; Machitidwe 24:15.
42. Kodi nchifukwa ninji moyo wosatha padziko lapansi uli wothekera ndi wotsimikizirika?
42 Mulungu adzabweretsa mtundu wa anthu ku moyo, limodzi ndi chiyembekezo cha kusafanso konse padziko lapansi. Koma kodi moyo wosatha padziko lapansi ngwothekera motani? Uwo ngwotheka ndipo ngwotsimikizirika chifukwa chakuti chiri chifuniro ndi chifuno cha Mulungu. (Yohane 6:37-40; Mateyu 6:10) Chifukwa chokha chimene munthu amafera padziko lapansi lerolino nchakuti iye analandira cholowa cha imfa kuchokera kwa Adamu. Komabe, pamene tilingalira za kusatha kwa zinthu zodabwitsa zosiyanasiyana padziko lapansi zimene munthu analinganizidwira kusangalala nazo, nyengo yaifupi ya moyo wa zosakwanira zaka zana limodzi njaifupi mopambanitsa! Popereka dziko lapansili kwa ana a anthu, Mulungu analinganiza kuti munthu ayenera kukhalabe ndi moyo kuti asangalale ndi zokongola za chilengedwe chake, osati kwa zaka zana limodzi lokha, kapena ngakhale zaka chikwi, koma kosatha!—Salmo 115:16; 133:3.
Bukhu Langwiro Lamtendere
43. (a) Kodi nkufunikira kotani kwa boma langwiro kumene kulipo? (b) Kodi nchiyani chimene Yehova walinganiza m’chimenechi?
43 Chifukwa chakuti makolo athu oyamba anakana lamulo la Mulungu, boma la anthu linakhala pansi pa uyang’aniro wa Satana. Moyenelera Baibulo limatcha Satana “mulungu wa dongosolo lino lazinthu.” (2 Akorinto 4:4, NW) Nkhondo, nkhanza, chivundi ndi kusakhazikika kwa maboma a anthu zimatsimikizira kuti iye ali. Chigwirizano cha Amitundu ndi Mitundu Yogwirizana zalephera kubweretsa mtendere kuchokera m’chisokonezo. Anthu akufuula kuti apeze boma lamtendere. Kodi sikuli kwanzeru kuti Mlengi, amene akulinganiza kubwezeretsa Paradaiso kudziko lapansili, akaperekanso boma langwiro kaamba ka Paradaiso ameneyu? Ndicho chimenedi Yehova walinganiza kuchita. Mfumu Yomuimira m’boma limeneli ndiyo ‘Kalonga wake Wamtendere,’ Kristu Yesu, ndipo “kuchuluka kwa kulamulira kwaukalonga ndi mtendere sikudzakhala ndi mapeto.”—Yesaya 9:6, 7, NW.
44. (a) Kodi boma limeneli lidzakhala kuti? (b) Kodi lidzapangidwa ndi yani?
44 Baibulo limasonyeza kuti boma langwiro lidzakhala kumwamba. Kuchokera pamalo apamwamba amenewa, Mfumu Yesu Kristu adzalamulira mogwira mtima dziko lonse lapansi m’chilungamo. Ndiponso, iye adzakhala ndi olamulira anzake m’boma losawoneka limenelo, lakumwamba. Amenewa asankhidwa pakati pa anthu okhulupirika, otsatira a Yesu amene anamamatirana naye m’mayesero ndi amene iye ananena nawo kuti: “Ndichita pangano ndi inu, monga momwe Atate wanga wachita pangano ndi ine, la Ufumu.” (Luka 22:28, 29) Ndiowerengeka chabe ochokera mwa anthu amene atengeredwa kumwamba kukalamulira ndi Kristu Yesu. Kuli kofanana ndi amitundu lerolino, kumene owerengeka chabe amasankhidwa kulamulira m’nyumba ya aphungu kapena nyumba ya malamulo. Baibulo limasonyeza kuti Yesu adzakhala kokha ndi olamulira anzake 144 000. Motero Ufumu wa Mulungu, kapena boma lakumwamba, lapangidwa ndi Kristu Yesu ndi anthu okwanira 144 000 otengedwa kuchokera padziko lapansi kumka kumwamba. (Chivumbulutso 14:1-4; 5:9, 10) Ndipo bwanji zadziko lapansi? Salmo 45:16 limanena kuti Mfumuyo idzaika ‘akalonga m’dziko lonse lapansi.’ ‘Akalonga,’ aumunthu kapena oyang’anira aboma, adzaikidwa kuchokera kumwamba chifukwa cha kudzipereka kwawo kwakuya kumalamulo amakhalidwe abwino achilungamo.—Yerekezerani Yesaya 32:1.
45, 46. (a) Kodi nchiyani chimene chinali mutu wankhani waukulu wa kulalikira kwa Yesu padziko lapansi? (b) Kodi nchifukwa ninji boma langwiro silinakhazikitsidwe mwamsanga? (c) Kodi ndimotaini mmene chaka cha 1914 C.E. chinaliri chapadera mu ulosi ndi m’zochitika zadziko?
45 Kodi ndiliti ndipo ndimotani mmene boma langwiro lidzakhazikitsidwira? Pamene Yesu anali padziko lapansi ufumu umenewo unali mutu waukulu wa kulalikira kwake. (Mateyu 4:17; Luka 8:1) Komabe, iye sanakhazikitse ufumuwo panthawiyo, ngakhale pachiukiriro chake. (Machitidwe 1:6-8) Ngakhale pamene anakwera kumwamba, iye anafunikirabe kuyembekezera nthawi yoikidwiratu ya Yehova. (Salmo 110:1, 2; Ahebri 1:13) Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti nthawi yoikidwiratu imeneyo inafika mu 1914 C.E. Komabe, wina adzafunsa kuti, ‘Mmalo mwa boma langwiro, kodi 1914 sinali chizindikiro cha kuyambika kwa masoka ochuluka adziko?’ Mfundo ndiimeneyo kumene! Pali kugwirizana kwakukulu pakati pa kudza kwa Ufumu wa Mulungu ndi zochitika zamasoka za zaka zaposachedapa, monga momwe tidzawonera tsopano.
46 Kwa zaka zokwanira 35 chaka cha 1914 chisanafike, The Watchtower (tsopano magazine achipembedzo ofalitsidwa mofalikira koposa onse padziko lapansi) anasonyeza 1914 kukhala chaka chapadera mu ulosi wa Baibulo. Umodzi wa amenewa unali wa Yesu mwiniyo, wonenedwa zaka 1 900 zapita, wonena za “chizindikiro” chimene chikawoneka m’nthawi ya mapeto a dongosolo la zinthu ndiumene akatsimikizira kuti iye anali pafupi mosawoneka m’mphamvu yaufumu. Poyankha funso la ophunzira ake lonena za “chizindikiro,” chimenechi iye anati: “Mtundu umodzi anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi mmalo akuti akuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.” (Mateyu 24:3, 7, 8) M’kukwaniritsidwa kochititsa chidwi, yoyamba yankhondo zadziko inayambidwa mu 1914, imene inadzetsa chiwonongeko chowirikiza nthawi zisanu ndi ziwiri kuposa nkhondo zonse 900 za m’zaka zam’mbuyomo 2 500! Zowawa zoyamba zapitirizabe kuyambira pamenepo. Kodi inu mwakumana ndi chiwonongeko chankhondo, kuperewera kwa zakudya, kapena chirichonse cha zivomezi zazikulu zimene zakantha dziko lapansi kuyambira 1914? Ngati ziri choncho, inu mwakhala mboni yowona ndi maso ya “chizindikiro” cha “nthawi za mapeto” za dongosolo lino la zinthu.—Danieli 12:4.
47. Kodi ndimotani mmene zochitika zokwaniritsa “chizindikiro” zawonjezerekera m’zaka zaposachedwapa?
47 “Zowawa zoyamba” zawonjezereka kupyolera mwa Nkhondo Yadziko II, imene inali yowononga kuwirikiza nthawi zinayi kuposa Nkhondo Yadziko I, ndi kupitirizabe kufikira m’nyengo ya nyukleya, kukwaniritsa ulosi wina wa Yesu wakuti: “Pa dziko lapansi kuvutika maganizo kwa mitundu, yosadziwa njira yotulukira . . . , pamene anthu akukomoka ndi mantha ndi chiyembekezo cha zinthu za kudza pa dziko lapansi lokhalidwa ndi anthu.” (Luka 21:25, 26, NW) Kuwonjezereka kwa upandu ndi kuipa, kusamvera ndi kupulupudza pakati pa ana kuphatikizapo kukula kwa kupanda umulungu ndi chisembwere—zochitika zowopsa zimenezi zinanenedweratunso monga chizindikiro cha “masiku otsiriza” a dongosolo loipa la zinthu lino.—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:12.
48. Kodi ndani amene ali ndi thayo la masoka adziko lapansi, ndipo kodi nchifukwa ninji awonjezereka chiyambire 1914?
48 Komabe, ngati boma lakumwamba linakhazikitsidwa mu 1914, kodi nchifukwa ninji pa dziko lapansi pali masautso onsewa? Ndiye Satana Mdyerekezi amene ali ndi thayo. Pamene Kristu analandira mphanvu ya ufumu, chochita chake choyamba chinali kuchita nkhondo ndi Satana m’miyamba yosawoneka. Chotulukapo chake chinali chakuti Satana “amene ali kusocheza dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu,” anaponyedwa limodzi ndi angelo ake chifupi ndi dziko lapansi. Pozindikira kuti chiwonongeko chake chayandikira, iye akusonkhezera vuto lalikulu padziko lapansi. Ndiro ‘tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa chakuti Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu podziwa kuti kamtsalira kanthawi.’—Chivumbulutso 12:7-9, 12.
49. (a) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira awo amene “akuwononga dziko”? (b) Kodi ndimotani mmene Yehova adzaperekera “chiweruzo” chake pa amitundu?
49 Kodi padzakhala mapeto a masoka amenewa? Inde!—pamene boma lakumwamba lenilenilo, Ufumu wa Mulungu Wamphanvuyonse, lichitapo kanthu “kuwononga iwo akuwononga dziko.” (Chivumbulutso 11:18; Danieli 2:44) Mulungu sadzalola konse maulamuliro andale zadziko, Akristu onyenga, kapena munthu wina aliyense kuwononga ntchito ya manja ake, dziko lapansi, ndi zipangizo zawo za nyukleya. Mmalo mwake, iye akulengeza kuti: “Ndatsimikiza mtima ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndiko mkwiyo wanga wonse waukali.” (Zefaniya 3:8) Yehova, kudzera mwa Kristu wake, adzagwiritsira ntchito mphamvu zazikulu zimene amalamulira nazo chilengedwe chonse kudzetsa chiwonongeko champhamvu kwa onse amene amatsatira Satana padziko lapansi. Izi zidzakhala pa mlingo wadziko lonse, mofanana ndi ukulu wa Chigumula cha tsiku la Nowa.—Yeremiya 25:31-34; 2 Petro 3:5-7, 10.
50. (a) Kodi “Armagedo” nchiyani? (b) Kodi ndani okha amene adzapulumuka Armagedo?
50 M’Baibulo chiwonongeko chamitundu yoipa chimenechi chimatchedwa nkhondo ya Mulungu ya Armagedo. (Chivumbulutso 16:14-16) Ndiwo anthu ofatsa okha, ofunafuna Yehova ndi chilungamo, amene angapulumuke Armagedo kulowa m’Dongosolo Latsopano lamtendere. (Zefaniya 2:3; Yesaya 26:20, 21) Ponena za amenewa Baibulo limati: “Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:11) Pamenepo ntchito yaikulu yakubwezeretsa Paradaiso pa dziko lapansi idzayamba!
Maphunziro Akulowera Paradaiso
51. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti inu muchitepo kanthu tsopano lino?
51 Kodi mukanakonda kukhala ndi moyo m’Paradaiso? Ngati yankho lanu liri ‘Inde,’ mudzasangalala kudziwa kuti pamene Yesu analankhula za dongosolo lamavuto lamakonoli ndi za “chizindikiro” cha chiwonongeko chake choyandikira, iye anawonjezera kuti, “mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.” Anthu ena, a mbadwo umene unawona “zowawa zoyamba” mu 1914 adzakhala ndi moyo kuwona Paradaiso akubwezeretsedwa padziko lapansi. (Mateyu 24:3-8, 34) Komabe, chiri chowonadi chomvetsa chisoni chakuti unyinji wa anthu lerolino uli panjira yotakata imene imatsogolera kuchiwonongeko. (Mateyu 7:13, 14) Pali nthawi yochepa imene yawatsalira kuti asinthe. Mungakhale woyamikira chotani nanga kuti Yehova wapereka chenjezo m’nthawi yake! Chifukwa chakuti Yehova amafuna kuti inu mukhale ndi moyo, adzakuthandizani kuti mutenge njira yolungama.—2 Petro 3:9; Ezekieli 18:23.
52. Kodi nchiyani chimene mufumikira kuti mupange chosankha chanzeru ponena za chipembedzo?
52 Chofunika chanu chofulumira tsopano ndicho chidziwitso cholongosoka. (1 Timoteo 2:4; Yohane 17:3) Kodi mungachipeze kuti chimenechi? Kodi chingapezedwe m’chipembedzo china chiri chonse? Anthu ena amanena kuti zipembedzo zonse ziri ndi cholinga chofanana, monga momwedi njira zonse zopita kuphiri zimatsogolelera pamutu paphiriro. Ha ngolakwa chotani nanga! Kuti apeze njira yoyenera, okwera mapiri amagwiritsira ntchito mapu, ndipo amalemba ganyu owaperekeza. Mofananamo, pali chipembedzo chimodzi chokha cha chowonadi chimene chidzatsogolera ku moyo wosatha, ndipo kuti muchipeze chitsogozo chiri chofunika.—Machitidwe 8:26-31.
53. (a) Kuti mupeze moyo wasatha, kodi inu muyenera kupitirizabe kuchita chiyani? (b) Kodi ndimayeso otani ochokera kwa Satana amene mungafunikire kugonjetsa?
53 Kabukhu kano kakufalitsidwa ndi Mboni za Yehova kukuthandizani. Iko kakuthandizani kale kuzindikira chowonadi cha Baibulo chamaziko, kodi sichoncho? Mosakaikira inu mwadzitsimikizira kuti mfundo iri yonse yachokera m’Mawu ouziridwa a Mulungu. Tsopano, kuti mupite patsogolo kulinga ku chonulirapo chanu, muyenera kupitirizabe kphunzira. Monga momwe maphunziro adziko oyenerera aliri ofunika kuyeneretsa munthu kuti apeze malo m’chitaganya cha tsiku ndi tsiku chotero maphunziro oyenerera a Baibulo ngofunika kukonzekeretsa munthuyo kulowa m’chitaganya chimene chidzapulumuka kukhala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi. (2 Timoteo 3:16, 17) Satana angayese kukudodometsani mwakuchititsa atsamwali apafupi kukutsutsani kapena mwakukuyesani kulowa m’njira yadyera yokondetsa zinthu zakuthupi kapena chisembwere. Musagonjere kwa Satana. Chisungiko chanu ndi mtsogolo monse mwa inu mwini ndi banja lanu zimadalira pa kupitirizabe kuphunzira kwanu Baibulo.—Mateyu 10:36; 1 Yohane 2:15-17.
54. Kodi ndikakonzedwe kowonjezereka kotani kamaphunziro kamene Yehova wapanga kwanuko?
54 Kuwonjezera pa kupitirizabe phunziro lanu la Baibulo tsopano, pali njira ina ya kuphunzira. Anthu m’dera la kwanuko amene ali okondwera ndi kuphunzira Baibulo amafika pamisonkhano mokhazikika pa nyumba Yaufumu kwanu konko. Ofikapo onse amalandira malangizo ochokera m’Baibulo ndipo amayesayesa mowona mtima kukhala anthu abwino kwambiri. Iwo amalandira alendo mwachisangalalo mwakumati, ‘Idzani anthu inu, ndipo tiyeni tipite ku phiri la Yehova [malo ake olambirira] . . . ndipo iye adzatilangiza njira zake, ndipo ife tidzayenda m’mabande ake.’ (Yesaya 2:3, NW) Zifukwa zabwino zofikira pamisonkhano Yabaibulo zalongosoledwa pa Ahebri 10:24, 25, pamene pamati: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muwona tsiku lirikuyandika.”
55. (a) Kodi gulu la Yehova limasiyana motani ndi ena? (b) Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zagwirizanira koposa anthu ena onse?
55 Pamene mugwirizana ndi gulu la Yehova, mudzapeza mkhalidwewo kukhala wosiyana kwambiri ndi uja wa mu akachisi ndi matchalitchi. Mulibe mbale zazopereka, mulibe miseche kapena kukangana, ndipo mulibe kusankhana chifukwa cha chiyambi cha banja kapena kaimidwe m’zandalama. Mkhalidwe wapadera koposa pakati pa Mboni za Yehova ndiwo chikondi. Choyamba, izo zimakonda Yehova, ndipo chachiwiri, zimakonda anthu ena. Izi ndizo zizindikiro za Akristu owona. (Mateyu 22:37-39; Yohane 13:35) Muyenera kufika pamisonkhano yawo ndi kudzitsimikizirira nokha. Mosakaikira mudzachita chidwi ndi kugwirizana kwawo. Pali Mboni zoposa mamiliyoni atatu padziko lonse lapansi m’maiko oposa 200. Komabe, Mbonizo padziko lonse lapansi zimatsatira maprogramu amodzimodzi pa misonkhano yawo. Ndipo chifukwa cha kufalitsidwa kwa panthawi imodzimodzi m’zinenero zambiri, unyinji wa Mboni za Yehova umaphunzira nkhani Zamalemba zimodzimodzi pamisonkhano yawo padziko lonse mkati mwa maora osiyana pang’ono. Chigwirizano cha gulu la Yehova ndicho chozizwitsa chamakono m’dziko logawanika lino.
56. (a) Kodi ndimapindu otani amene mungalandire kuchokera m’kugwirizana ndi gulu la Yehova? (b) Pamene mavuto abuka, kodi muyenera kuchita chiyani? (c) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti inu mupatulire moyo wanu kwa Yehova?
56 Pamene musonkhana mokhazikika ndi anthu a Yehova, mudzafunikira kudziveka “umunthu watsopano” ndi kukulitsa zipatso zamzimu—“chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikulupiriro, chifatso, chiletso.” (Akolose 3:10, 12-14; Agalatiya 5:22, 23) Zimenezi zidzakupatsani chikhutiro chachikulu. Mungakhale ndi mavuto oti mugonjetse nthawi ndi nthawi chifukwa chakuti mukukhala ndi moyo m’dziko lovunda ndiponso chifukwa cha kupanda ungwiro kwa inu mwini. Koma Yehova adzakuthandizani. Mawu ake amatsimikizira awo amene amayesayesa mowona mtima kumkondweretsa kuti: “Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Mudzasonkhezeredwa ndi chikondi cha Yehova, kotero kuti mudzafuna kumtumikira. Mboni za Yehova zidzakhala zachimwemwe kukusonyezani mmene mungaperekere moyo wanu kwa Mulungu wachikondi ameneyu ndi kukhala mmodzi wa mboni zake zamwaŵizo. (Salmo 104:33; Luka 9:23) Inde, uli mwaŵi. Tangolingalirani! Monga wolambira wa Yehova, mungathe kukalimira chonulirapo cha moyo wasatha m’paradaiso pano padziko lapansi.—Zefaniya 2:3; Yesaya 25:6, 8.
57. (a) M’Dongosolo Latsopano, kodi ndiunansi wapafupi wotani umene udzakhalapo pakati pa Mulungu ndi anthu? (b) Kodi ndi ena a madalitso otani amene mungadzasangalale nawo panthawiyo?
57 Pamenepo, pitirizanitu kuphunzira ndi kukula msinkhu m’chikondi ndi kuyamikira Yehova Mulungu, Mwana wake, ndi boma lakumwamba lachilungamo. Polongosola boma la Mulungu ndi madalitso amene lidzawatsanulira pa anthu, ulosi wa Baibulo umati: “Tawonani! Chihema cha Mulungu chiri mwa anthu, ndipo iye adzakhala pamodzi ndi iwo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Ndipo Mulungu mwiniyo adzakhala limodzi nawo.” “Mulungu mwiniyo” amene ali wokwezeka pamwambamwamba pa ulamuliro wadyera wa anthu, ndi wovulaza wamakonowu, adzakhala pafupi kwambiri monga Atate wachifundo kwa awo onse amene amamkonda ndi kumlambira m’Dongosolo Latsopano. Ndithudi, padzakhala chipembedzo chimodzi chokha, kulambiridwa kowona kwa Yehova Mulungu, ndipo olambira ake adzakhala ndi unansi wapafupi wa ana kwa Atate. Ha Adzadzisonyeza kukhala Atate wachikondi chotani nanga! “Ndipo adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo sikudzakhalanso imfa, ngakhale kulira maliro ngakhale kufuula ngakhale zopweteka sizidzakhalakonso. Zinthu zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
58. Kodi nchifukwa ninji mungakhale wotsimikizira kuti Yehova ‘adzapanga zinthu zonse kukhala zatsopano’?
58 Motero chozizwitsa chachikulu cha kukhazikitsa dziko lapansi la paradaiso pansi pa boma lakumwamba langwiro chidzakhala chitakwaniritsidwa. Chiri chotsimikizirika mofanana ndi chenicheni chakuti maŵa dzuŵa lidzatuluka ndi kulowa. Pakuti malonjezo a Yehova Mulungu, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, ali “okhulupirika ndi owona” nthawi zonse. Ali Iyeyo amene amalengeza kuchokera ku mpando wake wachifumu kumwamba kuti: “Tawonani! Ndikupanga zinthu zonse zatsopano.”—Chivumbulutso 21:5, NW.
M’kupenda Kabukhu Kano, Kodi mukanayankha motani mafunso otsatirawa?
Kodi Baibulo liri lapadera m’njira zotani?
Kodi mwaphunziranji ponena za Mulungu?
Kodi Kristu Yesu ndani?
Kodi Satana Mdyerekezi ndani?
Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola kuipa?
Kodi nchifukwa ninji munthu amafa?
Kodi mkhalidwe wa akufa ndi wotani?
Kodi dipo nchiyani?
Kodi chiukiriro chimachitikira kuti ndipo motani?
Kodi Ufumu nchiyani, ndipo kodi udzachita chiyani?
Kodi nchiyani chimene chiri “chizindikiro” cha “mapeto a dongosolo la zinthu”?
Kodi ndimotani mmene mungakonzekerere moyo wosatha m’Paradaiso?
[Mawu a M’munsi]
a Malemba a Baibulo ochirikiza ndime zapamwambapazo: (1) Machitidwe 17:26; Salmo 46:9; Mika 4:3, 4; Yesaya 65:21-23; (2) Yesaya 65:25; 11:6-9; 55:12, 13; Salmo 67:6, 7; (3) Yobu 33:25; Yesaya 35:5, 6; 33:24; Salmo 104:24; (4) Yesaya 55:11.
b Kusiyapo ngati kwasonyezedwa mwanjira ina, mawu ogwidwa Amalemba m’kabukhu kano ngochokera mu Revised Union Nyanja Version ndi New World Translation of the Holy Scriptures, kope lotulusidwa 1984 akumakhala chidule chake.
c Monarchs and Tombs and Peoples—The Dawn of the Orient, tsamba 25.
d Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, lolembedwa ndi J. McClintock and J. Strong, Voliamu 8, tsamba 908.
[Zithunzi patsamba 13]
Monga cholengedwa, munthu ali wapamwamba kwambiri koposa nyama
[Chithunzi patsamba 18]
Yesu anali wolingana ndi munthu wangwiro Adamu