Chidziŵitso Chimene Yehova Wapereka
“Ponena za awo okhala ndi chidziŵitso pakati pa anthu, iwo adzapereka kumvetsera kwa ambiri.”—Danieli 11:33, “NW.”
1, 2. (a) Ngakhale kuti Aisrayeli anakumana ndi kukoma mtima kwa Mulungu, nchifukwa ninji iwo anachita mopanduka? (b) Nchiyani chomwe chikakhala chopindulitsa kwa ife kuchichita? (Yeremiya 51:10)
ANTHU a Israyeli wakale anadziwa kuti Yehova anali Mulungu yekha wowona. Iwo anawuzidwa za zochita zake ndi makolo awo, ndipo anali atakumana mwaumwini ndi kukoma mtima kwake. Koma koposa pa chochitika chimodzi, iwo anachita ndi kusoweka kwa chidziŵitso kokulira. Iwo “anachita mopikisana” kulinga kwa Yehova ndi oimira ake. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “sanakumbukire” zomwe iye anachita kaamba ka iwo. (Salmo 106:7, 13) Sichinali chifukwa chakuti iwo sanadziŵe zinthu zimenezi; iwo analephera kusinkhasinkha pa izo moyamikira. Monga chotulukapo, iwo anatsimikizira kukhala “olakalaka zoipa.”—1 Akorinto 10:6.
2 M’tsiku lathu, njira yaikulu mu imene Yehova wakhazikira mboni zake kukhala zosiyana monga anthu apadera mwa chidziŵitso chimene iye wapereka kupyolera mu gulu lake lowoneka ndi maso. Kuyamikira kwathu kwenikweni kaamba ka njira mu imene Yehova akutsogozera anthu ake kungalimbitsidwe mwa kubwerera mu zina za zitsanzo za chidziŵitso choterocho. Chimodzi cha ichi chimaphatikiza magwero enieni a chikhulupiriro chathu—chizindikiritso cha Mulungu iyemwini.
Kodi Mulungu Ali Utatu?
3. Nchiyani chomwe chinatheketsa atumiki a Yehova, mkati mwa zaka mazana angapo zapita, kuzindikira chowonadi ponena za kuzindikiritsidwa kwa Mulungu? (1 Akorinto 8:5, 6)
3 Chikristu cha Dziko chasungirira zolimba kuti awo omwe samavomereza chikhulupiriro mu Utatu ali opanduka. Koma m’malo moyambukiridwa ndi anthu, atumiki a Yehova azindikira kuti, osati mwambo ndi ziphunzitso za anthu osawuziridwa, koma Malemba Oyera ndi amene amapereka miyezo ya kuzindikira chimene chiri chowonadi. Kumangirira pa maziko amenewa, kumbuyoko mu 1882 ophunzira a Baibulo odzipereka amenewa analongosola momvekera bwino mu Nsanja ya Olonda kuti: “Aŵerengi athu ali odziŵa kuti pamene kuli kwakuti timakhulupirira mwa Yehova Mulungu ndi Yesu, ndi Mzimu woyera, timatsutsa monga chopanda malemba kotheratu, chiphunzitso chakuti iyi iri Milungu itatu mwa munthu mmodzi, kapena monga mmene ena amachiikira icho, Mulungu mmodzi mwa anthu atatu.”—Yohane 5:19; 14:28; 20:17.
4. (a) Kupyola pa zowonedweratu, nchiyani chimene anthu a Yehova azindikira ponena za maziko kaamba ka chiphunzitso cha Utatu ndi chotulukapo cha chiphunzitsocho? (b) Nchifukwa ninji Yehova anapatsa atumiki ake chidziŵitso choterocho?
4 Okonda chowonadi cha Baibulo amenewa anali atapyola kuposa pa zowonedweratu ndipo anali atawona maziko a chikhulupiriro cha Utatu m’zipembedzo zosakhala za Chikristu. Mwa phunziro losamalitsa la Malemba, iwo anali atazindikiranso kuti pamene malemba ena a Baibulo amawoneka kuchirikiza malingaliro a Utatu, ichi chinali chifukwa cha malingaliro opotozedwa a atembenuzi, osati chifukwa cha chimene chinali mu mamanusikripiti a chinenero choyambirira. Iwo amazindikira kuti chiphunzitso chimenechi, chodzinenera kulemekeza Yesu, m’chenicheni chinatsutsa chiphunzitso chake ndipo chinanyoza Yehova. Chotero, kope la Nsanja ya Olonda lomwe lalozeredwako pamwambapo linanena kuti: “Chikutifulumiza ife monga ofunafuna chowonadi, kuchita mowona mtima ndi ife eni ndi Mawu a Atate wathu, omwe ali okhoza kutipangitsa ife kukhala anzeru mowonadi. Chotero, kunyalanyaza miyambo ndi ziphunzitso za anthu osawuziridwa ndi dongosolo loipa, tiyeni timamatire ku mtundu wa mawu abwino olandiridwa kuchokera kwa Ambuye wathu ndi Atumwi.” Chifukwa chakuti iwo anakondadi chowonadi ndi kupereka chisamaliro osati kokha ku ndime za Baibulo zokondedwa zoŵerengeka koma ku Mawu onse a Mulungu, Yehova anawapatsa iwo chidziŵitso chimene mosakaikira chimawalekanita iwo ku Chikristu cha Dziko.—2 Timoteo 3:16, 17; onani New World Translation Reference Bible, tsamba 1580, mbale 6B.
Malo Olondola a Dzina la Mulungu
5. Nchiyani chomwe chakhala kumbuyo kwa chikhoterero kulinga ku kusiya dzina laumwini la Mulungu m’matembenuzidwe a Baibulo? (Chibvumbulutso 22:18, 19)
5 Lingalirani chitsanzo chachiŵiri: Pamene matembenuzidwe a Baibulo m’ziŵerengero zowonjezereka anaphimba kapena kusiya kotheratu dzina laumwini la Mulungu, Watch Tower Society inaika chigogomezero chokulira nthaŵi zonse pa kufunika kwa dzinalo. Chikristu cha Dziko chinatsutsa kuti kuchotsedwa kwa dzina lakuti Yehova kukapatsa Uthenga Wabwinowo kusangalatsa kowonjezereka kwa chilengedwe cha ponse ponse, koma atumiki odzozedwa a Yehova anazindikira yemwe anali kumbuyo kwa machenjera a kuchotsa m’Malemba Opatulika dzina lofunika koposa onse. (Yerekezani ndi Yeremiya 23:27.) Anthu a Mulungu anazindikira kuti ichi chinasonkhezeredwa ndi Mdyerekezi kuti achotse m’chikumbukiro cha munthu dzina la Mulungu wowona.
6. Mosiyana ndi njira ya Chikristu cha Dziko, nchiyani chimene atumiki owona a Mulungu achita kukulitsa dzina lake? (Machitidwe 15:14)
6 Mosiyana ndi njira yotsatiridwa ndi Chikristu cha Dziko, kuchokera m’chaka chake choyamba chenichenichi cha kufalitsidwa (1879), Nsanja ya Olonda inapereka kutchuka ku dzina laumulungu, YEHOVA. Mu 1926 magazini imeneyi inawonetsa nkhani yakuti “Kodi Ndani Adzalemekeza Yehova?” (Salmo 135:21) Mu 1931 ophunzira Baibulo ogwirizana ndi Watch Tower Society anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova. (Yesaya 43:10-12) Iwo anadzayamikiranso mokwanira kufunika kokulira kwa kupatulika kwa dzina la Yehova. (Yesaya 12:4, 5) Mu 1944 anayamba kufalitsa American Standard Version ya Baibulo, yomwe imaphatikiza dzina lakuti Yehova nthaŵi zoposa 6,800. M’chigwirizano ndi kufalitsidwa kwa Baibulolo, ngakhale kuli tero, chapadera koposa chakhala kutulutsidwa, chiyambire 1950, kwa New World Translation. Iyo imapatsa dzina laumulungu malo ake oyenera ponse paŵiri m’Malemba Achikristu Achihebri ndi Achigriki.
7. Ndimotani mmene chigogomezero choikidwa pa dzina la Mulungu ndi zonse zomwe zagwirizanitsidwa ndi ilo chayambukirira mopindulitsa anthu ambiri?
7 Chigogomezero chomwe mwakutero chaikidwa pa dzina laumwini la Mulungu chakhala chokondweretsa ku mamiliyoni okonda chilunjiko kuzungulira dziko lonse. Chawathandiza iwo kuyamikira Mulungu wowona monga Munthu. Ndipo pamene iwo adziŵa njira zake, akhala okhoza kudzisunga iwo eni mochenjera, kapena ndi chidziŵitso.—Mika 4:2, 5.
Kodi Moyo wa Munthu Uli Wosafa?
8. Kumayambiriro m’mbiri yawo yamakono, nchiyani chimene Mboni za Yehova zaphunzira ponena za moyo ndi mkhalidwe wa akufa?
8 Tsopano, chitsanzo chachitatu: Pa nthaŵi yoyambirira mu mbiri yamakono ya atumiki a Yehova, chikondi kaamba ka Mawu a Mulungu chinatsegula maso awo ku zowonadi zina zofunika. Loposa zana limodzi lapitalo, “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” anamvetsetsa molondola kuti moyo suli mzimu wina wa luntha ndi wokhoza kuchokamo womwe umakhala mkati mwa anthu koma kuti ali munthu iyemwini. (Mateyu 24:45-47, NW) Mu 1880 Nsanja ya Olonda inasanthula mawu a chinenero choyambirira otembenuzidwa motsatira kamvekedwe ka liwu la Shelo ndi Hade m’Baibulo ndipo inatsiriza kuti awa amaimira manda. Iyo inalozanso kuti anthu oponyedwa ku Gehena anawonongedwa, osati kuzunzidwa.—Onaninso New World Translation Reference Bible, masamba 1573-5.
9. Mu 1894, nchiyani chimene Nsanja ya Olonda inanena ponena za chiyambi cha chiphunzitso chakuti moyo wa munthu uli wosafa mwachibadwa?
9 Mu 1894 Nsanja ya Olonda inadzutsa funso lakuti, “Ndi liti chotero pamene kunadza lingaliro lofala lakuti anthu onse ali ndi moyo wosafa, mwachibadwa, mwachilengedwe?” Ndi chidziŵitso, iyo inayankha kuti: “Titafufuza masamba a mbiri yakale, timapeza kuti, ngakhale kuti chiphunzitso cha kusafa kwa munthu sichinaphunzitsidwe ndi mboni zowuziridwa za Mulungu, icho chiri magwero enieni a zipembedzo zonse zonyenga. . . . Sichiri chowona, chotero, kuti Socrates ndi Plato anali oyambirira kuphunzitsa chiphunzitsocho: icho chinali ndi mphunzitsi woyambirira kuposa aliyense wa iwo, ndipo komabe wodziŵa kwambiri. Iwo, ngakhale kuli tero, anakometsera chiphunzitsocho . . . ndi kupanga nthanthi kuchokera ku icho, ndipo mwakutero kuchipangitsa icho kukhala chokoka kwenikweni ndi cholandirika ku gulu la miyambo ya m’tsiku lawo ndi pambuyo pake. Zolembedwa zoyambirira za chiphunzitso chonyenga chimenechi zikupezeka m’mbiri yakale kwenikweni yodziŵika kwa munthu—Baibulo. Mphunzitsi wonyengayo anali Satana.”a
10. Ndi zotulukapo zoipa zotani zomwe zadza ku bodza la chipembedzo lonena za moyo ndi mkhalidwe wa akufa, koma kodi nchiyani chomwe chinachitidwa kuthandiza anthu owona mtima?
10 Mwa kuwanditsa chinyengo chakuti anthu onse ali ndi moyo wosafa ndi kuti oipa adzazunzidwa kosatha mu moto wa helo, Satana waimira molakwika ndi kuchitira mwano dzina la Mulungu. Mkonzi woyambirira wa Nsanja ya Olonda, C. T. Russell, anazindikira chimenecho. Iye anawona anthu a luntha akukana lingaliro la kuzunzidwa kosatha koma, mwachisoni, anakananso Baibulo chifukwa chakuti analingalira kuti linali magwero a chiphunzitso chosalongosoka chimenecho. Ndi cholinga chofuna kuchotsa utsi wa Mbadwo Wakuda m’malingaliro a anthu olingalira bwino, monga mmene iye anachiikira icho, Mbale Russell anapereka nkhani yapoyera yochititsa nthumanzi yakuti “Ku Helo ndi Kubwereranso! Ndani Ali Kumeneko.”
11. (a) Pamene kukhulupirira mizimu kunkawonekera, ndi chenjezo lotani lomwe linaperekedwa ndi gulu la ‘kapolo wokhulupirika’? (b) Ndani omwe apindula ndi chenjezo limeneli, ndipo motani?
11 Imeneyo inali nyengo imene kukhulupirira mizimu kunkawonekera. Koma ndi chidziŵitso chimene Yehova Mulungu anachipanga kukhala chothekera kupyolera m’Mawu ake, gulu la ‘kapolo wokhulupirika’ linazindikira kuti mizimu imene anthu ankalankhulana nayo inali ziwanda. Kutsutsana kwamphamvu kwa m’Malemba kunaperekedwa m’nkhani zapoyera ndi mu mkhalidwe wolembedwa kutsegula maso a anthu owona mtima ku ngozi yophatikizidwa m’machitachita a mzimu. (Deuteronomo 18:10-12; Yesaya 8:19) Monga chotulukapo cha chidziŵitso chimenechi chimene Yehova wapereka kwa atumiki ake, zikwi zambiri za anthu kuzungulira dziko lonse amasulidwa kuchoka ku kuwopa akufa, machitachita a kukhulupirira mizimu, ndi kuchoka ku miyambo yopotozedwa yogwirizanitsidwa ndi kukhulupirira mizimu.
Mkhalidwe Wachikristu m’Dziko Lovuta
12, 13. (a) Longosolani Danieli 11:32, 33. (b) Nchiyani chimene chiri zowonadi zenizeni zina za Baibulo zomwe zimapereka maziko kaamba ka kumvetsetsa koperekedwa ndi “awo okhala ndi chidziŵitso?”
12 Mneneri Danieli anasonyeza kuti atumiki a Mulungu akasonyeza chidziŵitso m’chigwirizano ndi nkhani inanso yachinayi, nkhani yofunika kwenikweni—uchete. Pambuyo pa kulongosola mwatsatanetsatane kulimbana pakati pa zigawo zotchuka za ndale zadziko, Danieli 11:32, 33 ikunena kuti: “Akuchitira choipa chipanganocho iye adzawaipsya, ndi kuwasyasyalika.” Uko ndiko kuti, mfumu yankhalwe ya kumpoto ikutsogoza mu mpatuko awo omwe amadzinenera kukhala Akristu koma omwe amakonda dziko, ofuna chivomerezo chake, ndipo chotero kuchita ndi chinyengo chipangano cha Yehova kaamba ka Ufumu mu umene Yesu Kristu adzalamulira dziko lonse lapansi. “Koma,” Danieli akupitiriza tero, “anthu akudziŵa Mulungu wawo, adzalimbika mtima nadzachita mwamphamvu. [Ndipo ponena za awo okhala ndi chidziŵitso pakati pa anthu, adzapereka kumvetsetsa kwa ambiri, NW].”
13 Chidziŵitso chofunikira kuti tichite mwanzeru ndi mikhalidwe yovuta yomwe kaŵirikaŵiri imatizungulira chazikidwa pa kuyamikira zowonadi zenizeni za Baibulo. Ndi chitsogozo cha Yehova, gulu la ‘kapolo wokhulupirika’ lazindikira zowonadi zimenezi. Chimodzi cha izo chiri chenicheni chakuti, monga mmene Yesu anasonyezera, wolamulira wosawoneka wa dziko iri ali Satana Mdyerekezi. (Luka 4:5-8; Yohane 12:31) M’chigwirizano ndi chowonadi chimenechi, 1 Yohane 5:19 imawonjezera kuti osati kokha gawo limodzi kapena lina koma “dziko lonse [mtundu wonse wa anthu kunja kwa mpingo wowona Wachikristu] ligona mwa woipayo.” (Chibvumbulutso 12:9) Popeza kuti Yesu ananena kuti atsatiri ake sakakhala “mbali ya dziko,” ichi chimaitanira kaamba ka uchete Wachikristu ku mbali yawo.—Yohane 17:16, NW.
14. (a) Ndi ku nkhani za pa nthaŵi yake zotani kumene chisamaliro cha atumiki a Yehova chinalunjikitsidwa mu 1939 ndi 1941? (b) Ndimotani mmene chidziŵitso choterocho chathandizira Mboni za Yehova kuchita mwanzeru?
14 Chotero, chinali cha panthaŵi yake, kuti pamene mitambo ya Nkhondo ya Dziko ya II inadera mu Europe, nkhani ya uchete Wachikristu inawunikiridwa mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1939 (m’Chingelezi). Chogwirizana ndi nkhaniyi chinali chowonadi china chofunika—kufunika kwa nkhani ya ulamuliro wa chilengedwe cha ponseponse ndi thayo la Ufumu wa Umesiya m’kukhazikitsa nkhani imeneyo. Moyenerera, mu 1941 nkhani imeneyi inawunikiridwa m’nkhani ya pa msonkhano wa Mboni za Yehova mu St. Louis, Missouri, U.S.A., ndipo chaka chotsatira m’bukhu la The New World. Ndi chitetezero chotani nanga chimene chidziŵitso chaumulungu choterocho chinapereka kaamba ka atumiki a Yehova m’dziko lino logawanika ndi la nkhondo! Ngakhale kuti madongosolo a zipembedzo za Chikristu cha Dziko agawanika chifukwa chakuti adzilola iwo eni kudzilowetsa mu kukanthana kwa mitundu yonse ndi machitachita a chiweniweni ndi cholinga chogwetsa maboma, Mboni za Yehova m’maiko onse zapitirizabe mogwirizana kudzipereka iwo eni ku kulengeza Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chokha kaamba ka mtundu wa anthu. Iwo adzisunga kukhala otanganitsidwa m’ntchito yopulumutsa moyo imene Yesu Kristu ananeneratu pamene ananena kuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko onse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14, NW.
Kukwaniritsidwa kwa Maulosi a Baibulo
15. Nchifukwa ninji atumiki a Yehova akhalira ndi chidziŵitso?
15 Nchifukwa ninji atumiki a Yehova akhalira ndi chidziŵitso choterocho? Chifukwa chakuti ali ndi chidaliro chotheratu m’Mawu olembedwa a Mulungu, amamvera iwo, ndipo mzimu wa Yehova uli pa iwo. Ichi chawatheketsanso iwo kumvetsetsa maulosi ofunika kwenikweni a Baibulo, ndipo iyi iri nsonga yachisanu yomwe tidzalingalira.
16, 17. (a) Nchifukwa ninji masiku ogwiritsiridwa ntchito ndi Mboni za Yehova nthaŵi zina amasiyanira ndi aja operekedwa ndi mbiri yakale ya kudziko? (b) Ndimotani mmene Mboni za Yehova zapindulira kuchokera ku chidaliro chawo m’Baibulo ponena za kuika masiku a chaka cha 20 cha Aritasasta ndi nthaŵi ya kuwonongedwa kwa Yerusalemu kochitidwa ndi Ababulo?
16 Akatswiri a mbiri yakale a kudziko, kudalira pa kumasulira kwawo kwa chimene m’mbali ina chiri zidutswa za miyala yofukulidwa ndi akatswiri ofukula zofotseredwa, atsiriza kuti 464 B.C.E. chinali chaka choyamba cha kukhala mfumu kwa Aritasasta Longimanus ndi kuti 604 B.C.E. chinali chaka choyamba cha kukhala mfumu kwa Nebukadinezara II. Ngati chimenecho chinali chowona, chaka cha 20 cha Aritasasta chikayamba mu 445 B.C.E., ndipo tsiku la kupasulidwa kwa Yerusalemu ndi Ababulo (m’chaka cha 18 cha kulamulira kwa Nebukadinezara) chikakhala 587 B.C.E. Koma ngati wophunzira Baibulo agwiritsira ntchito masiku amenewo pa kuŵerengera kukwaniritsidwa kwa ulosi, iye adzangosokonezeka.
17 Mboni za Yehova zakhala zokondweretsedwa m’zopeza za akatswiri ofukula zofotseredwa popeza kuti izi zimaloza ku Baibulo. Ngakhale kuli tero, kumene kumasulira kwa zopeza zimenezi kwatsutsana ndi ndemanga zomvekera zopezeka m’Baibulo, timalandira ndi chidaliro chimene Malemba Oyera amanena, kaya pa nkhani zogwirizana ndi kuŵerengera masiku kapena nkhani zina zirizonse. Monga chotulukapo, atumiki a Yehova azindikira kwa nthaŵi yaitali kuti nyengo ya nthaŵi ya ulosi yomwe inayamba mu chaka cha 20 cha Aritasasta inayenera kuŵerengedwa kuchokera mu 455 B.C.E. ndipo mwakutero kuti Danieli 9:24-27 inaloza modalirika ku chaka cha 29 C.E. m’chirimwe kukhala nthaŵi kaamba ka kudzozedwa kwa Yesu monga Mesiya.b Kaamba ka chifukwa chimodzimodzicho, iwo azindikira kuti ulosi wa Danieli mutu 4 wonena za “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri” unayamba kuŵerengedwa mu 607-606 B.C.E. ndi kuti iwo unaloza ku 1914 C.E. m’chirimwe kukhala chaka pamene Kristu anaikidwa pa mapndo wa chifumu m’mwamba monga Mfumu yolamulira ndipo dziko iri linalowa m’nthaŵi yake ya mapeto.c Koma iwo sakanakhoza kuzindikira zokwaniritsidwa zosangalatsa zimenezi za ulosi ngati iwo sanakhazikike m’chidaliro chawo m’kuwuziridwa kwa Malemba Oyera. Chotero, chidziŵitso chimene iwo asonyeza chagwirizanitsidwa mwachindunji ndi chidaliro chawo pa Mawu a Mulungu.
18. Nchiyani chimene Yesaya 65:13, 14 imalonjeza ponena za mkhalidwe wauzimu wa atumiki okhulupirika a Yehova?
18 Kusiyanitsa mkhalidwe wauzimu wa atumiki ake okhulupirika ndi uja wa aliyense pa yekha ndi magulu omwe mofulumira aika pambali Malemba m’kuyanja chirichonse chimene chiri chofala panthaŵiyo, Yehova akunena kuti: “Tawonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; tawonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; tawonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi; tawonani, atumiki anga adzayimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu.”—Yesaya 65:13, 14.
19. (a) Poyambirira, nkupyolera m’njira yotani imene “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” amaperekera kulongosola kwa Malemba? (b) Ndi programu ya mtundu wotani yophunzira yomwe idzatitheketsa kupindula mokwanira kuchokera ku chakudya chauzimu?
19 Monga mmene kubwerera kwachidule m’mbiri yake imeneyi kwasonyezera, chiri kupyolera m’madanga a Nsanja ya Olonda kumene kulongosola kwa zowonadi za m’Malemba zofunika koposa kwaperekedwa kaamba ka ife ndi “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” wa Yehova. Nsanja ya Olonda iri chiwiya chachikulu chogwiritsidwa ntchito ndi gulu la “kapolo” kaamba ka kupereka chakudya chauzimu. Kodi mukupindula kuchokera ku icho mokwanira? Kodi mumaŵerenga kope lirilonse, ndipo kodi programu yanu ya kuphunzira imaphatikizapo kuyang’ana malemba omwe aikidwamo koma osagwidwa mawu? Kodi mumachipanganso kukhala chizoloŵezi kusinkhasinkha pa zimene mwaphunzira, kumangirira chiyamikiro kaamba ka icho, kulingalira mmene chingayambukire mkhalidwe wanu, zikhumbo zanu, zochita zanu za tsiku ndi tsiku, zonulirapo zanu m’moyo? Kuchita kwanu tero kungakhale chochititsa chachikulu m’kupanga kwanu zigamulo zozikidwa pa chidziŵitso chenicheni chimene Yehova yekha wapereka.
[Mawu a M’munsi]
a Satana anatsogoza Hava kukhulupirira kuti mwa kuthupi iye sakafa nkomwe. (Genesis 3:1-5) Chotero sichinali kufikira pambuyo pake pamene iye anayambitsa chiphunzitso chonyenga chakuti anthu ali ndi moyo wosafa womwe umapitirizabe kukhala ndi moyo pambuyo pa imfa ya thupi.—Onani Nsanja ya Olonda, September 15, 1957, tsamba 575 (Chingelezi).
b Insight on the Scriptures, Volyumu 2, masamba 614-16, 899-901.
c “Let Your Kingdom Come,” masamba 186-9.
Kodi Nchiyani Chomwe Mukukumbukira?
◻ Kodi Mulungu ali Utatu, ndipo nchifukwa ninji mukuyankha tero?
◻ Ndi kuti kumene dzina la Mulungu molondola liyenera kupezeka?
◻ Kodi moyo wa munthu uli wosafa?
◻ Ndi chidziŵitso chotani chimene Yehova wapereka ku mkhalidwe Wachikristu m’dziko lovutali?
◻ Mboni za Yehova zalandira chidziŵitso chotani ponena za kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo?
[Zithunzi patsamba 18]
Mwa kugwiritsira ntchito Nsanja ya Olanda, “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” umapereka chidziŵitso ponena za tanthauzo la malemba ndi kugwira ntchito kwawo m’tsiku lathu