Chiphunzitso Chaumulungu Chilakika
“Maso anu adzakhala maso oona Mlangizi wanu Wamkulu. Ndipo makutu anuwo adzamva mawu kumbuyo kwanu akuti: ‘Njira ndiiyi. Yendani mmenemo, anthu inu.’”—YESAYA 30:20, 21, NW.
1. Kodi nchifukwa ninji malangizo a Yehova moyenerera angatchedwe chiphunzitso chaumulungu?
YEHOVA MULUNGU ndiye Magwero a chiphunzitso chabwino choposa chimene aliyense angachilandire. Ngati timvetsera pamene alankhula, makamaka kupyolera m’Mawu ake Opatulika, iye adzakhala Mlangizi wathu Wamkulu. (Yesaya 30:20) Malemba a Baibulo Achihebri amamutchanso “Waumulungu.” (Salmo 50:1, NW) Chifukwa chake, malangizo a Yehova ali chiphunzitso chaumulungu.
2. Kodi ndim’lingaliro lotani mmene kuliri kowona kuti Mulungu yekha ndiye wanzeru?
2 Dziko limanyadira sukulu zake zosiyanasiyana zochuluka, koma palibe ngakhale imodzi ya sukulu zakezo imene imaphunzitsa chiphunzitso chaumulungu. Eya, nzeru zonse zadziko zimene zasonkhanitsidwa m’mbiri yonse ya anthu sizili kanthu poziyerekezera ndi malangizo aumulungu ozikidwa panzeru ya Yehova yopanda polekezera. Lemba la Aroma 16:27 limanena kuti Mulungu yekhayo ndiye wanzeru, ndipo zimenezi nzowona m’lingaliro lakuti Yehova yekha ndiye ali ndi nzeru yachikwanekwane.
3. Kodi nchifukwa ninji Yesu Kristu ali mphunzitsi wamkulu woposa onse amene anakhalako padziko lapansi?
3 Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, ndiye chitsanzo changwiro cha nzeru ndipo ali mphunzitsi wamkulu woposa aliyense wokhalako padziko lapansi. Zimenezi nzosadabwitsa! Popeza kuti kwa nyengo zosaneneka Yehova anali Mphunzitsi wake kumwambako. Ndi iko komwe, chiphunzitso chaumulungu chinayamba pamene Mulungu anayamba kulangiza chilengedwe chake choyamba, Mwana wake wobadwa yekha. Chifukwa chake Yesu anakhoza kunena kuti: “Monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.” (Yohane 8:28; Miyambo 8:22, 30) Mawu a Kristu mwiniyo olembedwa m’Baibulo amawonjezera zochuluka pa chidziŵitso chathu cha chiphunzitso chaumulungu. Mwa kuphunzitsa zimene Yesu anaphunzitsa, Akristu odzozedwa amamvera Mlangizi wawo Wamkulu, amene chifuniro chake chili chakuti “nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu” idziŵike kupyolera mwampingo.—Aefeso 3:10, 11; 5:1; Luka 6:40.
Kufunafuna Nzeru
4. Kodi nchiyani chimene chanenedwa ponena za kukhoza kwa ubongo?
4 Kupeza nzeru yochokera m’chiphunzitso chaumulungu kumafunikiritsa kugwiritsira ntchito mwakhama maganizo athu opatsidwa ndi Mulungu. Zimenezi nzotheka chifukwa ubongo wa munthu uli ndi kukhoza kwakukulu. Buku lakuti The Incredible Machine limati: “Ngakhale makompyuta ocholoŵana koposa amene tingaganizire atsala kutali poyerekezera ndi kucholoŵana ndi kukhoza kuchita zinthu zosiyanasiyana kwa ubongo wa munthu—mikhalidwe yotheketsedwa ndi dongosolo lolinganizika, ndi locholoŵana la kayendedwe ka mauthenga la makhemikolo ndi magetsi. . . . Mauthenga mamiliyoni ambiri oloŵa muubongo wanu panthaŵi iliyonse amakhala ndi chidziŵitso chochuluka koposa. Amabweretsa chidziŵitso chonena za mkhalidwe wa m’thupi lanu ndi wa kunja kwake: chonena za chala chochita dzanzi, kapena fungo lokoma la khofi, kapena mawu oseketsa a bwenzi lanu. Pamene mauthenga ena afufuza ndi kufotokoza chidziŵitsocho, amayambitsa mikhalidwe yakutiyakuti ya mtima, zikumbukiro, malingaliro, kapena mapulani ochititsa munthu kupanga chosankha. Mwamsanga, mauthenga ochokera muubongo wanu amauza mbali zina za thupi lanu chochita: gwedeza chala chako, imwa khofi, seka, kapena mwinamwake yankha moseka. Panthaŵi imodzimodziyo ubongo wanu ukuyang’anira kupuma kwanu, msanganizo wa mwazi, temperecha, ndi zochita zina zofunikira za m’thupi zimene simumazizindikira. Umapereka malangizo amene amachititsa thupi lanu kugwirabe ntchito bwino mosasamala kanthu za kusintha kosalekeza kwa malo amene mulimo. Ndiponso umakonzekera zofunika za mtsogolo.”—Tsamba 326.
5. M’lingaliro la Malemba, kodi nzeru nchiyani?
5 Ngakhale kuti mosakayikira ubongo wa munthu uli ndi kukhoza kodabwitsa, kodi tingagwiritsire ntchito motani maganizo athu mwa njira yabwino koposa? Osati mwa kudziloŵetsa kotheratu m’maphunziro ovuta a chinenero, mbiri yakale, sayansi, kapena mpikisano wa nzeru za chipembedzo. Tiyenera kugwiritsira ntchito maluso athu akulingalira kwakukulukulu kupezera chiphunzitso chaumulungu. Ndicho chokha chimapatsa nzeru yeniyeni. Koma kodi nzeru yeniyeni nchiyani? M’lingaliro la Malemba, nzeru imagogomezera pakuweruza kwabwino kozikidwa pa chidziŵitso cholongosoka ndi kuzindikira kwenikweni. Nzeru imatitheketsa kugwiritsira ntchito chidziŵitso ndi kuzindikira mwachipambano kuthetsa mavuto, kupeŵa kapena kuchinjiriza ngozi, kuthandiza ena, ndi kufikira zonulirapo. Mokondweretsa, Baibulo limasiyanitsa nzeru ndi kupusa ndi uchitsiru—mikhalidwe imene tifunadi kupeŵa.—Deuteronomo 32:6; Miyambo 11:29; Mlaliki 6:8.
Buku Lophunziridwa Lalikulu la Yehova
6. Ngati titi tisonyeze nzeru yeniyeni, kodi nchiyani chimene tiyenera kugwiritsira ntchito bwino?
6 Pali nzeru zadziko zochuluka zotizinga. (1 Akorinto 3:18, 19) Eya, dzikoli lili ndi sukulu zambirimbiri ndi malaibulale okhala ndi mamiliyoni a mabuku! Ambiri a ameneŵa ali mabuku ophunzitsa zinenero, masamu, sayansi, ndi mitundu ina ya nzeru. Koma Mlangizi Wamkulu wapereka buku lophunziridwa limene limapambana ena onse—Mawu ake ouziridwa, Baibulo. (2 Timoteo 3:16, 17) Ilo nlolondola osati kokha pankhani zonga mbiri yakale, malo adziko, ndi zomera komanso poneneratu za mtsogolo. Ndiponso, limatithandiza kukhala ndi moyo wachimwemwe kwambiri ndi wopindulitsa ngakhale tsopano lino. Ndithudi, monga momwe ophunzira m’sukulu zadziko amafunikira kugwiritsira ntchito mabuku awo, tiyenera kuzoloŵera bwino lomwe ndi kugwiritsira ntchito Buku Lophunziridwa lalikulu la Mulungu ngati titi tisonyeze nzeru yeniyeni monga anthu “ophunzitsidwa ndi [Yehova, NW].”—Yohane 6:45.
7. Kodi nchifukwa ninji munganene kuti kudziŵa mwaluntha zimene zili m’Baibulo sikuli kokwanira?
7 Komabe, kudziŵa mwaluntha zimene zili m’Baibulo sikufanana ndi nzeru yeniyeni ndi kulabadira chiphunzitso chaumulungu. Tamverani chitsanzo: M’zaka za zana la 17 C.E., mwamuna Wachikatolika wotchedwa Cornelius van der Steen anafuna kukhala chiŵalo cha Mjesuit koma anakanidwa chifukwa chakuti anali wamfupi kwambiri. Manfred Barthel akunena motere m’buku lake lakuti The Jesuits—History & Legend of the Society of Jesus: “Komiti imeneyi inauza van der Steen kuti inali yokonzekera kuchotsapo chiyeneretso cha msinkhucho, koma pamaziko amodzi akuti aloŵeze Baibulo lonselo pamtima. Sipakanakhala chifuno chosimbira nkhani imeneyi ngati van der Steen akanalephera kulabadira chiyeneretso chovutitsa chimenechi.” Ha, panafunikira kuyesayesa kwakukulu chotani nanga kuloŵeza pamtima Baibulo lonse lathunthu! Komatu, nkofunikadi kwambiri kumvetsetsa Mawu a Mulungu kuposa kungowaloŵeza pamtima.
8. Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupindula ndi chiphunzitso chaumulungu ndi kusonyeza nzeru yeniyeni?
8 Ngati titi tipindule mokwanira ndi chiphunzitso chaumulungu ndipo ngati titi tisonyeze nzeru yeniyeni, tifunikira kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Malemba. Tiyeneranso kutsogozedwa ndi mzimu woyera wa Yehova, kapena mphamvu yake yogwira ntchito. Zimenezi zidzatikhozetsa kuphunzira chowonadi chamaziko, “zakuya za Mulungu.” (1 Akorinto 2:10) Chifukwa chake, tiyeni tiphunzire mwakhama Buku Lophunziridwa lalikulu la Yehova ndi kupempherera chitsogozo chake mwamzimu woyera. Mogwirizana ndi Miyambo 2:1-6, tiyeni tiike chisamaliro pa nzeru, tiyedzamitse mtima wathu pa kuzindikira, ndipo tifunefune luntha. Tifunikira kuchita zimenezi monga ngati kuti tinali kufunafuna chuma chobisika, pakuti mpokhapo pamene tingathe ‘kuzindikira kuwopa Yehova ndi kupeza nzeru yeniyeni ya Mulungu.’ Kupenda zina za zilakiko ndi mapindu a chiphunzitso chaumulungu kudzakulitsa chiyamikiro chathu cha nzeru yoperekedwa ndi Mulungu.
Kumvetsetsa Komawonjezereka
9, 10. Kodi Mulungu ananenanji, monga momwe kwalembedwera pa Genesis 3:15, ndipo kodi tanthauzo loyenera la mawu amenewo nlotani?
9 Chiphunzitso chaumulungu chilakika mwa kupatsa anthu a Yehova kumvetsetsa Malemba komawonjezereka. Mwachitsanzo, taphunzira kuti anali Satana Mdyerekezi amene analankhula kudzera mwa njoka m’Edene ndi kunena monama kuti Mulungu ananama pamene Iye anati imfa ndiyo ikakhala chilango cha kudya chipatso choletsedwacho. Komabe, taona kuti kusamvera Yehova Mulungu kunadzetsadi imfa pa fuko la anthu. (Genesis 3:1-6; Aroma 5:12) Komabe, Mulungu anapatsa mtundu wa anthu chiyembekezo pamene anauza njokayo, amene ndiye Satana kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.”—Genesis 3:15.
10 Mawu amenewo anali ndi chinsinsi chomwe chavumbulidwa momawonjezereka mwa chiphunzitso chaumulungu. Yehova waphunzitsa anthu ake kuti mutu waukulu wa Baibulo ndiwo kulemekezedwa kwa uchifumu wake kupyolera mwa Mbewuyo, mbadwa ya Abrahamu ndi Davide yokhala ndi kuyenera kwalamulo kwa kulandira ulamuliro wa Ufumu. (Genesis 22:15-18; 2 Samueli 7:12, 13; Ezekieli 21:25-27) Mlangizi wathu Wamkulu watiphunzitsa kuti Yesu Kristu ndiye Mbewu yaikulu ya “mkazi,” gulu la m’chilengedwe chonse la Mulungu. (Agalatiya 3:16) Mosasamala kanthu za chiyeso chilichonse chimene Satana anabweretsa pa iye, Yesu anasunga umphumphu wake—kufikira ngakhale imfa, kulalira chitende cha Mbewuyo. Taphunziranso kuti oloŵa Ufumu anzake okwanira 144,000 ochokera mwa mtundu wa anthu adzagwirizana ndi Kristu pophwanya mutu wa Satana, “njoka yakaleyo.” (Chivumbulutso 14:1-4; 20:2; Aroma 16:20; Agalatiya 3:29; Aefeso 3:4-6) Tiyamikira chotani nanga nzeru yoteroyo ya Mawu a Mulungu!
Kuloŵa m’Kuunika Kodabwitsa kwa Mulungu
11. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti chiphunzitso chaumulungu chimalakika mwa kuloŵetsa anthu m’kuunika kwauzimu?
11 Chiphunzitso chaumulungu chimalakika mwa kuloŵetsa anthu m’kuunika kwauzimu. Zimenezo zachitika kwa Akristu odzozedwa kukwaniritsa lemba la 1 Petro 2:9 limene limati: “Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.” Lerolino, kuunika kochokera kwa Mulungu kulinso ndi “khamu lalikulu” lomwe lidzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi laparadaiso. (Chivumbulutso 7:9; Luka 23:43) Pamene Mulungu akuphunzitsa anthu ake, lemba la Miyambo 4:18 likukwaniritsidwa: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kumkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.” Kuphunzira komawonjezereka kumeneku kumayenga kumvetsetsa kwathu chiphunzitso chaumulungu, monga momwe ana asukulu amapitira patsogolo chifukwa cha chithandizo chabwino cha mphunzitsi pophunzira galamala, mbiri yakale, kapena maphunziro ena.
12, 13. Kodi chiphunzitso chaumulungu chatetezera anthu a Yehova ku ngozi zachiphunzitso ziti?
12 Chilakiko chinanso cha chiphunzitso chaumulungu nchakuti chimatetezera ochilandira odzichepetsa ku ‘ziphunzitso za ziŵanda.’ (1 Timoteo 4:1) Kumbali ina, yang’anani Dziko Lachikristu! Kalelo mu 1878, mbusa wa Roma Katolika John Henry Newman analemba kuti: “Pokhala ndi chidaliro m’mphamvu ya Chikristu ya kutetezera kukuipitsidwa ndi zoipa, ndi kusanduliza zipangizo ndi machitachita enieniwo a kulambira ziŵanda kukhala zolambirira m’tchalitchi, . . . olamulira a Tchalitchi kuchokera m’nthaŵi zakale anali okonzekera, kutakhala kofunikira, kutengera, kapena kutsanzira, kapena kuvomereza madzoma ndi miyambo imene inalipo ya anthu, limodzi ndi nzeru zadziko za anthu ophunzira kwambiri.” Newman anawonjezera kuti zinthu zoterozo zonga madzi oyera, zovala zopatulika, ndi mafano “zonse zinachokera kuchikunja, ndipo zinayeretsedwa mwa kuloŵetsedwa m’Tchalitchi.” Anthu a Mulungu alidi oyamikira kuti chiphunzitso chaumulungu chimawatetezera ku mpatuko wotero. Chimalakika pa mtundu uliwonse wa uchiŵanda.—Machitidwe 19:20.
13 Chiphunzitso chaumulungu chimalakika pa zolakwa za zipembedzo m’njira iliyonse. Mwachitsanzo, monga awo ophunzitsidwa ndi Mulungu, sitimakhulupirira Utatu koma timavomereza kuti Yehova ndiye Wammwambamwamba, Yesu ali Mwana wake, ndipo mzimu woyera uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Sitimawopa moto wa helo, pakuti timadziŵa kuti helo wa m’Baibulo ndimanda wamba a munthu. Ndipo pamene azipembedzo zonama anena kuti moyo wa munthu uli wosafa, ife timadziŵa kuti akufa sadziŵa kanthu mpang’ono ponse. Mpambo ukupitirizabe wa chowonadi chopezedwa mwa chiphunzitso chaumulungu. Ndidalitso lotani nanga kukhala omasuka ku ukapolo wauzimu kwa Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonama!—Yohane 8:31, 32; Chivumbulutso 18:2, 4, 5.
14. Kodi nchifukwa ninji atumiki a Mulungu amapitiriza kuyenda m’kuunika kwauzimu?
14 Chifukwa chakuti chiphunzitso chaumulungu chilakika pa zolakwa za zipembedzo, chimatheketsa anthu a Mulungu kupitiriza kuyenda m’kuunika kwauzimu. Kwenikweni, iwo amamva mawu kumbuyo kwawo akuti: “Njira ndiiyi. Yendani mmenemo, anthu inu.” (Yesaya 30:21) Chiphunzitso cha Mulungu chimatetezeranso atumiki ake ku malingaliro onama. Pamene “atumwi onyenga” anali kuchititsa mavuto mumpingo wa Korinto, mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga; ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziŵitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu.” (2 Akorinto 10:4, 5; 11:13-15) Malingaliro osiyana ndi chiphunzitso chaumulungu amagwetsedwa ndi malangizo amene amapatsidwa modekha mumpingo ndi mwa kulalikira kwathu mbiri yabwino kwa akunjawo.—2 Timoteo 2:24-26.
Kulambira Mumzimu ndi m’Chowonadi
15, 16. Kodi kulambira Yehova mumzimu ndi m’chowonadi kumatanthauzanji?
15 Pamene ntchito yolengeza Ufumu ikupita patsogolo, chiphunzitso chaumulungu chimalakika mwa kusonyeza odzichepetsawo mmene ayenera kulambirira Mulungu “mumzimu ndi m’chowonadi.” Patchitsime cha Yakobo pafupi ndi mzinda wa Sukari, Yesu anauza mkazi Wachisamariya kuti anali wokhoza kupereka madzi opatsa moyo wosatha. Akumanena za Asamariya, iye anawonjezera kuti: “Inu mulambira chimene simuchidziŵa; . . . Ikudza nthaŵi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi, pakuti Atate afuna otero akhale olambira ake.” (Yohane 4:7-15, 21-23) Ndiyeno Yesu anadziulula kukhala Mesiya.
16 Koma kodi ndimotani mmene tingalambirire Mulungu mumzimu? Mwa kumlambira koyenera kosonkhezeredwa ndi mitima yoyamikira yodzazidwa ndi chikondi cha pa Mulungu chozikidwa pa chidziŵitso cholongosoka cha Mawu ake. Tingamlambire m’chowonadi mwa kukana zinyengo zachipembedzo ndi mwa kuchita chifuniro cha Mulungu, monga momwe chasonyezedwera m’Buku Lophunziridwa lalikulu la Yehova.
Chimalakika pa Ziyeso ndi Dziko
17. Kodi mungasonyeze motani kuti chiphunzitso chaumulungu chathandiza atumiki a Yehova kuyang’anizana ndi ziyeso?
17 Pamene anthu a Mulungu ayang’anizana ndi ziyeso, chiphunzitso chaumulungu chimalakika nthaŵi zonse. Talingalirani izi: Kuchiyambi kwa Nkhondo Yadziko II, m’September 1939, atumiki a Yehova anafunikira chidziŵitso chapadera cha Buku lake Lophunziridwa lalikululo. Chithandizo chachikulu chinali nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1939, imene inapereka momvekera bwino chiphunzitso chaumulungu pankhani ya uchete Wachikristu. (Yohane 17:16) Mofananamo, kuchiyambi kwa ma 1960, nkhani za mu Nsanja ya Olonda zonena za kugonjera kokhala ndi polekezera ku “maulamuliro aakulu” a maboma zinathandiza anthu a Mulungu kulabadira chiphunzitso chaumulungu poyang’anizana ndi chipwirikiti cha m’chitaganya.—Aroma 13:1-7; Machitidwe 5:29.
18. Kodi ndimotani mmene odzinenera kukhala Akristu a m’zaka za zana lachiŵiri ndi lachitatu C.E. anaonera zosangulutsa zoluluzika, ndipo kodi nchithandizo chotani chimene chiphunzitso chaumulungu chimapereka pankhaniyo lerolino?
18 Chiphunzitso chaumulungu chimatithandiza kulaka ziyeso, zonga zonyengerera za kufuna zosangulutsa zoluluzika. Tamverani zimene zinanenedwa ndi odzinenera kukhala Akristu a m’zaka za zana lachiŵiri ndi lachitatu la Nyengo Yathu. Tertullian analemba kuti: “Tilibe chochita, m’mawu, m’kuona kapena m’kumva, ndi kufuntha kwa zionetsero zosangulutsa, zochititsa manyazi za m’bwalo la maseŵero, uchiŵanda wa m’bwalo la maseŵera.” Wolemba nkhani wina wapanthaŵiyo anafunsa kuti: “Kodi Mkristu wokhulupirika amakhala akuchitanji pazochita zimenezi, popeza kuti sayenera konse ngakhale kuganizira chabe zoipa? Kodi iye amapeza bwanji chisangalalo m’zinthu zosonyeza zilakolako zonyansa?” Ngakhale kuti olemba nkhani ameneŵa anakhalako patapita zaka zambiri pambuyo pa Akristu a m’zaka za zana loyamba, iwo anatsutsa zosangulutsa zoluluzika. Lerolino, chiphunzitso chaumulungu chimatipatsa nzeru yokanira zosangulutsa zaumaliseche, zamakhalidwe oipa ndi zachiwawa.
19. Kodi ndimotani mmene chiphunzitso chaumulungu chimatithandizira kulaka dziko?
19 Kumvera chiphunzitso chaumulungu kumatikhozetsa kulilaka dziko lenilenilo. Inde, kugwiritsira ntchito chiphunzitso cha Mlangizi wathu Wamkulu kumatikhozetsa kulaka zisonkhezero zoipa za dziko lino limene ligona m’mphamvu ya Satana. (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) Lemba la Aefeso 2:1-3 limanena kuti Mulungu watikhalitsa amoyo ngakhale kuti tinali akufa m’zolakwa zathu ndi m’machimo pamene tinayenda mogwirizana ndi wolamulira wa mlengalenga. Timayamikira Yehova kuti chiphunzitso chaumulungu chimatithandiza kulaka zikhumbo zadziko ndi mzimu wochokera kwa mdani wake ndi wathu—wonyenga wamkuluyo, Satana Mdyerekezi!
20. Kodi ndimafunso ati amene afunikira kupenda kowonjezereka?
20 Pamenepa, chiphunzitso chaumulungu mosakayikira chimalakikadi m’njira zambiri. Kwenikweni, kungaoneke kukhala kosatheka kutchula zilakiko zake zonse. Chimayambukira anthu kuzungulira dziko lonse. Koma kodi chikukuchitirani chiyani? Kodi chiphunzitso chaumulungu chikuyambukira motani moyo wanu?
Kodi Mwaphunziranji?
◻ Kodi nzeru yeniyeni ingafotokozedwe motani?
◻ Kodi nchiyani chimene Mulungu wavumbula momawonjezereka ponena za Genesis 3:15?
◻ Kodi ndimotani mmene chiphunzitso chaumulungu chalakikira m’zinthu zauzimu?
◻ Kodi kulambira Mulungu mumzimu ndi m’chowonadi kumatanthauzanji?
◻ Kodi ndimotani mmene chiphunzitso chaumulungu chathandizira atumiki a Yehova kulaka ziyeso ndi dziko?
[Zithunzi patsamba 10]
Yesu anasunga umphumphu kufikira imfa—kulalira Mbewu kuchitende