Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 159
  • Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi zinyama zili ndi mzimu?
  • Kodi moyo umafa?
  • Kodi zinyama zimachimwa?
  • Kodi n’zoyenera kuchitira nkhanza zinyama?
  • Nyama
    Galamukani!—2015
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kuzunza Nyama—Kodi Nkulakwa?
    Galamukani!—1998
  • Kodi Mulungu Amasamalira Nyama?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 159
Galu

Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo limaphunzitsa kuti pa zolengedwa zonse zomwe zili padziko lapansi, ndi anthu ochepa okha omwe adzapite kumwamba. (Chivumbulutso 14:1, 3) Anthuwo adzapita kumwamba kuti akalamulire limodzi ndi Yesu monga mafumu komanso ansembe. (Luka 22:28-30; Chivumbulutso 5:9, 10) Koma anthu ambiri adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi.—Salimo 37:11, 29.

Baibulo silimanena kuti ziweto kapena agalu zidzapita kumwamba. Tikutero chifukwa choti zinyama sizingakwanitse kutsatira mfundo za m’Baibulo zozithandiza kuyenerera ‘kuitanidwa kumwamba.’ (Aheberi 3:1) Mfundozi zikuphatikizapo kuphunzira, kukhala ndi chikhulupiriro komanso kumvera malamulo a Mulungu. (Mateyu 19:17; Yohane 3:16; 17:3) Choncho anthu okha ndi amene anapatsidwa chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha.—Genesis 2:16, 17; 3:22, 23.

Kuti zolengedwa zapadziko zipite kumwamba, zimafunika ziukitsidwe kaye. (1 Akorinto 15:42) M’Baibulo muli nkhani za anthu angapo omwe anaukitsidwa kwa akufa. (1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Luka 7:11-15; 8:41, 42, 49-56; Yohane 11:38-44; Machitidwe 9:36-42; 20:7-12) Koma onsewa anali anthu, osati zinyama.

  • Kodi zinyama zili ndi mzimu?

  • Kodi moyo umafa?

  • Kodi zinyama zimachimwa?

  • Kodi n’zoyenera kuchitira nkhanza zinyama?

Kodi zinyama zili ndi mzimu?

Ayi. Baibulo limanena kuti nyama komanso anthu ndi zamoyo. (Numeri 31:28) Munthu woyamba Adamu atalengedwa, sanapatsidwe mzimu koma ‘anakhala wamoyo.’ (Genesis 2:7) Moyo unapangidwa ndi zinthu ziwiri, “fumbi lapansi” komanso “mpweya wa moyo.”

Kodi moyo umafa?

Inde. Baibulo limaphunzitsa kuti moyo umafa. (Levitiko 21:11; Ezekieli 18:20) Anthu komanso zinyama zikafa, zimabwerera kufumbi. (Mlaliki 3:19, 20) M’mawu ena tinganene kuti sizikhalaponso.a

Kodi zinyama zimachimwa?

Ayi. Kuti munthu achimwe amafunika kuganiza, kukhudzidwa ndi zinthu kapena kuchita zinazake zosemphana ndi mfundo za Mulungu. Amafunikanso kukhala woti amatha kudziwa zoyenera kusankha pa nkhani ya makhalidwe. Komatu zinyama sizingathe kuchita zimenezi. Pa nthawi yonse imene zimakhala ndi moyo, zimangochita zinthu mwachibadwa. (2 Petulo 2:12) Kenako zimafa, ngakhale kuti sizinachimwe.

Kodi n’zoyenera kuchitira nkhanza zinyama?

Ayi. Mulungu anapatsa mphamvu anthu zoti aziyang’anira zinyama, koma sanawapatse ufulu woti azizichitira nkhanza. (Genesis 1:28; Salimo 8:6-8) Ndipotu Mulungu amasamalira nyama ina iliyonse ngakhale mbalame zing’onozing’ono. (Yona 4:11; Mateyu 10:29) Iye analamula olambira ake kuti asamachitire nkhanza nyama.—Ekisodo 23:12; Deuteronomo 25:4; Miyambo 12:10.

Mavesi a m’Baibulo onena za zinyama

Genesis 1:28: “Mulungu anawadalitsa n’kuwauza kuti: ‘Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire. Muyang’anirenso nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.’”

Mfundo yake: Mulungu anapatsa mphamvu anthu zoti aziyang’anira zinyama.

Numeri 31:28: “Monga msonkho kwa Yehova, pa gawo loperekedwa kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 500 zilizonse, pa anthu, ng’ombe, abulu, ndi nkhosa.”

Mfundo yake: Anthu komanso zinyama ndi zamoyo.

Miyambo 12:10: “Wolungama amasamalira moyo wa chiweto chake.”

Mfundo yake: Anthu abwino amasamalira zinyama, kuphatikizapo zomwe amaweta.

Mateyu 10:29: “Kodi mpheta ziwiri si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu? Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa.”

Mfundo yake: Mulungu amasamalira nyama ina iliyonse ngakhale mbalame zing’onozing’ono.

a Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 6 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena