Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 6/1 tsamba 4-7
  • Akristu Owona Amalemekeza Anthu Okalamba!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akristu Owona Amalemekeza Anthu Okalamba!
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Kugwadira’ Anthu Okalamba
  • Kuwachitira Ulemu “Mochulukira Koposa”
  • Yehova Amasamalira Mwachikondi Atumiki Ake Okalamba
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Anthu Okalamba Tiyenera Kuwachitira Zinthu Motani?
    Galamukani!—2004
  • Banja Lachikristu Limathandiza Okalamba
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Ulemerero wa Imvi
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 6/1 tsamba 4-7

Akristu Owona Amalemekeza Anthu Okalamba!

“OKALAMBA,” anatero wofufuza Suzanne Steinmetz, “ali kumapeto kwa umoyo wawo wotulutsa mwa chuma, omwe ali maziko amene mwambo wathu umawerengera munthu aliyense payekha ndikuwapatsa iwo kusiyana, malo, ulemu ndi mphatso.” Kawonedwe ka chitaganya chamakono ka okalamba chotero kali kozilala, kosayenerera. Nchosadabwitsa, mwakutero, kuti kawirikawiri timawerenga ponena za kunyalanyazidwa kwawo ndi kuyipsyidwa.

Komabe, kodi ndi kawonedwe kotani kamene Baibulo limatenga ponena za okalamba? Mawu a Mulungu moyenerera amazindikiritsa kuti ukalamba sichiri chinthu chopepuka. Anapemphera wamasalmo: “Musanditaye muukalamba wanga; musandisiye pakutha mphamvu zanga.” (Masalmo 71:9) Muukalamba wake, iye anadzimva kukhala wofuna chirikizo la Yehova kuposa ndi kale lonse. Ndipo kawonedwe ka Baibulo kali kabwino m’kusonyeza kuti ife, nafenso, tiyenera kupereka chisamaliro kuzosowa za okalamba.

Zowona, Solomo anautcha ukalamba “masiku oyipa” mu amene munthu “sakondwera nawo.” (Mlaliki 12:1-3) Koma “masiku ambiri ndi zaka zamoyo, m’Baibulo zimagwirizanitsidwanso ndi madalitso kuchokera kwa Mulungu. (Miyambo 3:1, 2) Kuchitira chitsanzo, Yehova analonjeza Abrahamu: “Ndipo iwe, . . . udzaikidwa ndi ukalamba wabwino (Genesis 15:15) Zowonadi, Mulungu sanali kumupatsa chilango chakutayidwa, “m’masiku oyipa” mu amene iye “analibe chikondwerero.” Abrahamu anapeza mtendere ndi kudekha mu zaka zake zomalizira, akumayang’ana m’mbuyo ndi chikhutiritso pa moyo wowonongedwa mu utumiki wa Yehova. Iye akanayang’ananso kutsogolo ku “mzinda wokhala ndi maziko enieni,” Ufumu wa Mulungu. (Ahebri 11:10) Chotero iye akanafa “wokalamba ndi wokhutiritsidwa.”​—Genesis 25:8.

Nchifukwa ninji, nanga, Solomo anatcha ukalamba monga “masiku oyipa”? Solomo analozera kukunyonyotsoka koyipa kwa umoyo komwe kumatulukapo mu ukalamba. Komabe, amene analephera ‘kukumbukira mlengi wake wamkulu mu masiku aunyamata Wake’ amazipeza zaka zomalizira kukhala zoyipa mwapadera. (Mlaliki 12:1) Chifukwa iye anawononga moyo wake, munthu wokalamba woteroyo ‘alibe chikondwerero’ mu masiku ake omalizira amoyo. Njira yake yamoyo yopanda umulungu ingakhale itatulukamo mavuto akuthupi omwe amakulitsa kusautsa kwa ukalamba. (Yerekezani ndi Miyambo 5:3-11) Chotero pamene akuyang’ana kutsogolo, iye sawona mtsogolo koma manda. Munthu amene anapereka moyo wake kutumikira Mulungu nayenso amawona “masiku oyipa” pamene thupi lake lifooka. Koma monga Abrahamu, iye angapeze chimwemwe ndi chikhutiritso mmoyo wowonongedwa bwino ndi kugwiritsira ntchito mphamvu yake yotsalira mu utumiki wa Mulungu. “Imvi ndiyo korona wa ulemu, idzapezedwa m’njira ya chilungamo,” likutero Baibulo.​—Miyambo 16:31.

Ndipo, ukalamba ulinso ndi mwawi wina. “Ubwana ndi unyamata ngwachabe,” akutero Solomo. Pamene anthu achichepere angasangalale ndi umoyo wabwino iwo kaŵirikaŵiri amasowa kuzolowera ndi chiweruzo. Ukalamba, ngakhale kuli tero, umabweretsa limodzi ndi iwo zokumana nazo za mmoyo. Okalamba ‘amachotsa zoyipa,’ mosiyana ndi wachichepere wokakamira amene kaŵirikaŵiri amathamangira mu izo. (Mlaliki 11:10; 2 Timoteo 2:22) Mofananamo, Solomo akunena kuti: “Kukongola kwa nkhalamba ndi imvi.”​—Miyambo 20:29.

Baibulo chotero limalemekeza okalamba. Kodi ndimotani mmene ichi chimakhudzira njira mu imene Akristu amachitira ndi iwo?

‘Kugwadira’ Anthu Okalamba

Mulungu anapanga kuchitira ulemu okalamba kukhala lamulo la mtundu mu Israyeli. Lamulo la Mose linanena: “Pali aimvi udziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba ”(Levitiko 19:32) Ayuda mu zaka zakumapeto mwachiwonekere analitenga lamuloli mutanthauzo lenileni. Akutero Dr. Samuel Burder mu bukhu lake Oriental Customs: “Alembi Achiyuda ananena kuti lamulo linali, kugwadira kwa iwo pamene anali pa utali wa mapazi anayi; ndipo mwamsanga pamene adutsa, kukhalanso pansi kachiŵriri, kuti chiwoneke kuti anayimirira kokha chifukwa cha ulemu kwa iwo.” Ulemu woterowo sunali woikidwa malire kwa amuna otchuka. “Lemekeza ngakhale okalamba omwe alibe maphunziro,” inatero Talmud. Rabbi m’modzi ananena kuti ulemu umenewo uyenera kuphatikizaponso munthu wopulukira ndi wosaphunzira. “Chenicheni chakuti iye wakalamba,”iye anapereka chifukwa, “chiyenera kukhala chifukwa cha mwawi winawake.”​—The Jewish Encyclopedia.

Akristu lerolino salinso pansi pa malamulo a Chilamulo cha Mose. (Aroma 7:6) Koma ichi sichitanthauza kuti iwo sali ndi thayo la kusonyeza ulemu wapadera kwa okalamba. Ichi chimazindikiritsidwa kuchokera kumalangizo a mtumwi Paulo operekedwa kwa woyang’anira Wachikristu Timoteo: “[Usasulize kwambiri, NW] mkulu. Mmalo mwake, umdandaulire ngati atate, . . . akazi achikulire ngati amayi.” (1 Timoteo 5:1, 2) Paulo anauza Timoteo wachichepere kuti iye anali ndi ulamuliro wa “kulamula.” (1 Timoteo 1:3) Mosasamala kanthu zachimenecho, ngati winawake wachikulire kuposa iye​—makamaka amene akutumikira monga woyang’anira—​alakwa muchiweruzo kapena apanga ganizo lolakwika, Timoteo sanayenera “kumusuliza” iye monga wochepera. Mmalo mwake, iye mwaulemu anayenera “kumdandaulira ngati atate.” Timoteo anayenera kusonyeza ulemu wofananawo kwa akazi achikulire mu mpingo. Inde, iye analidi, woyenera ‘kugwadira aimvi’.

Chotero Chikristu chiri chipembedzo chimene chimalemekeza okalamba. Kunena mosuliza, ngakhale kuli tero, kuvutitsa koChulukira kwa okalamba kumachitidwa mu mitundu yodzinenera kukhala Yachikristu. Komabe, pali, alambiri omwe akupitirizabe kumamatira ku makhalidwe a Baibulo. Mboni za Yehova, mwachitsanzo, zimasangalala ndi kukhalapo kwa zikwi zambiri za okalamba pakati pawo, iwo samawona iwo monga cholemetsa kapena chokhumudwitsa. Pamene umoyo wosakhala wabwino kwenikweni ungawaletse okalamba oterowo kukhala okangalika monga mmene iwo poyamba analiri, ambiri ali ndi zolembera zazitali zautumiki wokhulupirika Wachikristu, ndipo ichi chimalimbikitsa mboni zachichepere kutsanzira chikhulupiriro chawo.​—Yerekezani ndi Ahebri 13:7.

Okalamba, ngakhale kuli tero, samayembekezeredwa kutenga mbali yosagwira ntchito mu mpingo. Iwo akufulumizidwa kukhala zitsanzo zabwino mu kukhala “Odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m’chikhuhipiriro, . . . amakhalidwe oyenera anthu oyera,” mwaufulu kugawana nzeru yawo ndi zokumana nazo zawo ndi ena. (Tito 2:2, 3) Yoweli analosera kuti pakati pa awo ogawana m’kulengeza uthenga wa Baibulo, padzakhala “okalamba.” (Yoweli 2:28) Mosakaikira inu mwaumwini munawona kuti mboni zambiri zokalamba zimapeza chimwemwe mkugawana mokangalika mu ntchito yolalikira ya ku khomo ndi khomo.

Kuwachitira Ulemu “Mochulukira Koposa”

Mboni za Yehova zimakalamira kupereka chisamaliro chapadera kwa okalamba m’njira zambiri. Pa misonkhano ya chipembedzo ya pa chaka, mwachitsanzo, iwo kawirikawiri amakonza malo kuikidwa pambali kaamba ka okalamba. Lingaliro limasonyezedwanso kaamba ka iwo pamaziko a munthu aliyense payekha. Mu Japan Mboni imodzi inapereka malo ake mu galimoto ya banja kotero kuti mkazi wachikulire wa zaka 87 angakwere kupita ku misonkhano ya mpingo. Kodi ndimotani mmene iye amapitira ku misonkhano iyemwini? Pa njinga. Mu Brazil kuli wolengeza wa ufumu wanthawi zonse wa zaka 92. Oyang’ana anasimba kuti Mboni za kumeneko “zimamuchitira iye ulemu, kulankhula ndi iye . . . Iye ali mbali yofunika kwambiri ya mpingo.”

Ichi sichikutanthauza kuti palibe malo kaamba ka kuwongolera mkulemekeza kwathu okalamba. Paulo analemba kwa Akristu mu Tesalonika; “Koma kunena za chikondano cha pa abale . . . munawachitira ichi abale onse a m’Makedoniya lonse. Koma, tikudandaulirani abale, muchulukireko koposa.”(1 Atesalonika 4:9, 10) Uphungu wofananawo pa nthawi zina umafunidwa lerolino pamene chadza kuchisamaliro chathu kwa okalamba. Mkristu wa zaka 85, mwachitsanzo, anakhumudwitsidwa pamene iye sanalandire kope la chofalitsidwa chatsopano chozikidwa pa Baibulo. Vuto lake? Iye ali pafupi kukhala gonthi ndipo sanamve chilengezo chokumbutsa aliyense kuorda bukhulo, ndipo panalibe aliyense mu mpingo amene anaganiza za kuorda ilo kaamba ka iye. Mkhalidwewo ngakhale kuli tero, unawongoleredwa mwamsanga. Icho mosasamala kanthu chimasonyeza kuti pali kufunika kwa kukhala odera nkhawa mwapadera kaamba ka zosowa za okalamba.

Pali njira zosiyanasiyana zambiri mu zimene anthu a Mulungu lerolino angachitire ichi “mokulira koposa.” Misonkhano Yachikristu imapereka mwawi wa “kufulumiza” okalamba ku “chikondano ndi ntchito zabwino.” (Ahebri 10:24, 25) Ndipo pamene achichepere ndi achikulire amasakanizana kale mwaufulu pa Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova, mwinamwake kuyesayesa kowonjezereka kungapangidwe m’chigwirizano ndi izi. Mwachitsanzo, makolo ena amalimbikitsa ana awo mwaulemu kufikira ndi kulankhula ndi ziwalo zachikulire za mpingo.

Ulemu ungapitirizenso kusonyezedwa kwa okalamba pa maziko amwamwawi. Mchigwirizano ndi prinsipulo lokhazikitsidwa ndi Yesu pa Luka 14:12-14, kuyesayesa kokulira kungachitidwe mwakuwaitana okalamba kumapwando amayanjano. Ngakhale ngati iwo sangakhoze kupezekapo, iwo mowonadi adzayamikira kuwakumbukira kwanu. Akristu akulimbikitsidwanso “kuchereza alendo.”(Aroma 12:13) Ichi sichikafunikira kuitanira pa chinachake chosangalatsa kapena chokongola. Ikulingalira Mboni imodzi kuchokera ku Germany: “Itanani okalamba kaamba ka kapu ya tii, ndipo aloleni iwo kupereka zokumana nazo zawo zakale.”

Mtumwi Paulo anati: “Mkuchitirana ulemu wina ndi mzake mutsogolere.” (Aroma 12:10, NW) Pakati pa Mboni za Yehova, akulu a mpingo osankhidwa mwapadera amatenga chitsogozo m’kusonyeza ulemu kwa Akristu okalamba. Kaŵirikaŵiri akulu amakhala okhoza kugawira mathayo oyenerera kuchitidwa ndi okalamba, monga kuphunzitsa achatsopano monga alaliki kapena kuwathandiza kukonza malo osonkhanira Achikristu. Amuna achichepere otumikira monga akulu mu mpingo amasonyeza ulemu kwa oyang’anira okalamba mwa kuwafikira iwo modzichepetsa kaamba ka chithandizo, kugwiritsira ntchito kuzindikira kutenga nsonga zawo zauchikulire. (Miyambo 20:5) Pa misonkhano ya akulu oterowo iwo amatsatira chitsanzo cha mu Baibulo cha Elihu wachichepere ndipo mwaulemu amagonjera kwa akulu, amuna achidziwitso chochuluka, kuwapatsa mwawi wakudzilongosola iwo eni choyamba.​—Yobu 32:4.

Movomerezeka, chiri chapafupi kukhala osaleza mtima ndi okalamba chifukwa iwo sangathe kuyenda ndi kuganiza mofulumira monga mmene amachitira achichepere. Dr. Robert N. Butler amalongosola bwino ena a mavuto amene ukalamba umabweretsa: “Wina amataya mphamvu yake yakuthupi, kuthekera kwa kupitiriza, ndipo icho mwa icho chokha chingakhale chochititsa mantha koposa. Wina angataye kuthekera kwa kuzindikira monga ngati kumva kapena kupenya.” Kuyamikira chimenechi, kodi achichepere sayenera kusonyeza malingaliro omvera chisoni ndi kudera nkhawa?​—1 Petro 3:8.

Inde, Akristu lerolino ali ndi thayo lakusonyeza chikondi chenicheni, kudera nkhawa ndi ulemu kwa okalamba pakati pawo. Ndipo pakati pa Mboni za Yehova, ichi chikuchitidwa mwanjira ya chitsanzo. Nchiyani chimene chimachitika, ngakhale kuli tero, pamene Akristu okalamba​—kapena makolo Achikristu—​adwala kapena kusauka? Kodi ndi thayo landani kupereka kwa iwo chisamaliro? Nkhani zotsatirazi zidzafufuza ndimotani mmene Baibulo limayankhira mafunso amenewa.

[Chithunzi patsamba 7]

Mu mipingo ya Mboni za Yehova, okalamba amapeza ntchito yokhutiritsa kwambiri yoti aichite

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena