-
“Uzikwaniritsa Zinthu Zimene Walonjeza”Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2017 | April
-
-
7. (a) Kodi Hana analonjeza Yehova chiyani, nanga zotsatira zake zinali zotani? (b) Kodi Samueli ankayenera kudzakhala wotani mogwirizana ndi lonjezo la Hana? (Onani mawu a m’munsi.)
7 Nayenso Hana anakwaniritsa zimene analonjeza kwa Yehova. Iye ananena lonjezo lake pamene anali wokhumudwa kwambiri chifukwa cha vuto lake la kusabereka komanso chipongwe chimene mkazi mnzake ankamuchitira. (1 Sam. 1:4-7, 10, 16) Iye anauza Yehova zakukhosi kwake komanso anamulonjeza kuti: “Inu Yehova wa makamu, mukaona nsautso yanga, ine kapolo wanu wamkazi, ndi kundikumbukira, ndiponso ngati simudzaiwala kapolo wanu wamkazi ndi kum’patsa mwana wamwamuna, ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo lezala silidzadutsa m’mutu mwake.”a (1 Sam. 1:11) Yehova anayankha pemphero la Hanali ndipo anamupatsadi mwana wamwamuna. Hana ayenera kuti anasangalala kwambiri. Komabe iye sanaiwale lonjezo lake komanso sanaiwale kuti Yehova ndi amene anamuthandiza kuti abereke mwanayu. Moti mwanayu atangobadwa iye anati: “Ndinam’pempha kwa Yehova.”—1 Sam. 1:20.
-