Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ba tsamba 14-17
  • Kodi Buku Limeneli Tingalikhulupirire?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Buku Limeneli Tingalikhulupirire?
  • Buku la Anthu Onse
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukumba Umboniwo
  • Limafotokoza Nkhani Zake Mosabisa
  • Analondola Popereka Tsatanetsatane Wake
  • “Nyumba ya Davide” Yeniyeni Kapena Yopeka?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Ufumu Wotayika Umene Unachititsa Manyazi Osuliza Baibulo
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Zimene Asayansi Afukula Zikutsimikizira Kuti Mfumu Davide Analikodi
    Nkhani Zina
  • Asuri Wankhalwe—Mphamvu Yaikulu ya Dziko Yachiŵiri
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Buku la Anthu Onse
ba tsamba 14-17

Kodi Buku Limeneli Tingalikhulupirire?

“M’Baibulo ndimapezamo umboni wotsimikizirika kwambiri wakuti nloona kuposa m’mbiri ina iliyonse yakudziko kaya ikhale yotani.” —Bwana Isaac Newton, wasayansi wotchuka wa ku England.1

KODI buku limeneli​—Baibulo—​tingalikhulupirire? Kodi limatchula anthu omwe anakhalakodi, malo omwe analikodi, ndi zinthu zimene zinachitikadi? Ngati limatero, ndiye kuti payenera kukhala umboni wakuti linalembedwa ndi alembi osamala ndi oona mtima. Umboniwo ulipo. Wambiri wapezeka wokwirira m’nthaka, ndipo ngakhale bukulo lili nawo wina wambiri.

Kukumba Umboniwo

Zinthu zakale zokwirira zopezeka m’maiko a m’Baibulo zatsimikiza kuti mbiri ya Baibulo ndi malo otchulidwamo nzolondola. Tiyeni tingopenda umboni wina umene akatswiri ofukula m’mabwinja akumba.

Davide, mbusa wachinyamata wolimba mtima amene anadzakhala mfumu ya Israyeli, ngwodziŵika kwambiri kwa oŵerenga Baibulo. Dzina lake limapezeka m’Baibulo nthaŵi 1,138, ndipo mawu akutiwo “Nyumba ya Davide”​—amene nthaŵi zambiri amanena za mzera wake wachifumu—​limapezeka nthaŵi 25. (1 Samueli 16:13; 20:16) Komabe, kale kunalibe umboni wina kusiyapo wa m’Baibulo wotsimikiza kuti Davide analikodi. Kodi Davide anali chabe munthu wongopeka?

M’chaka cha 1993 kagulu ka akatswiri ofukula m’mabwinja, kotsogozedwa ndi Profesa Avraham Biran, kanapeza zinthu zodabwitsa, zimene zinasimbidwa m’magazini ya Israel Exploration Journal. Pamalo omwe kale panali chiunda chotchedwa Tel Dan, kumpoto kwa Israyeli, iwo anakumbapo mwala wakuda. Pamwalawo panali mawu ozokota akuti “Nyumba ya Davide” ndi “Mfumu ya Israyeli.”2 Iwo akuti mwala wozokotawo, wa m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E., ndi chibenthu cha chipilala chimene Aaramu​—adani a Israyeli amene amakhala kummaŵa—​anaimika. Kodi nchifukwa ninji mwala wakale wozokota umenewo uli wofunika kwambiri?

Malinga ndi lipoti la Profesa Biran ndi mnzake, Profesa Joseph Naveh, nkhani ya m’magazini ya Biblical Archaeology Review inati: “Imeneyi ndi nthaŵi yoyamba kupeza dzina la Davide pamwala wozokota wakale kunja kwa Baibulo.”3a Palinso china chofunika kuchidziŵa ponena za mwalawo. Mawuwo “Nyumba ya Davide” alembedwa monga liwu limodzi. Katswiri wa chinenero Profesa Anson Rainey akufotokoza kuti: “Nthaŵi zambiri . . . liwu saligaŵa, makamaka ngati liwulo lili dzina lenileni lodziŵika bwino. Ndithudi mawu akuti ‘Nyumba ya Davide’ anali dzina lenileni landale ndi la malo chapakati pa zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E.”5 Chotero malinga ndi umboni Mfumu Davide ndi mzera wake wachifumu anali kudziŵika kwambiri m’dziko lakale.

Kodi Nineve​—mzinda waukulu wa Asuri umene Baibulo limatchula—​unalikodi? Posachedwapa chakumayambiriro kwa zaka za zana la 19, ofufuza Baibulo ena anakana kukhulupirira zimenezo. Koma m’chaka cha 1849, Bwana Austen Henry Layard anafukula mabwinja a nyumba yachifumu ya Mfumu Sanakeribu ku Kuyunjik, malo omwe anapezeka kuti anali dera la Nineve wakale. Motero pankhani imeneyo ofufuzawo anakhala chete. Koma mabwinja amenewo anali nzambiri. Makoma a chipinda china chosungika bwino anali ndi chithunzi chosonyeza mzinda wamalinga olimba ataulanda, ndipo andende akuwayendetsa pamaso pa mfumu yolanda mzindawo. Pamwamba pa mfumuyo pali mawu awa: “Sanakeribu, mfumu ya dziko, mfumu ya Asuri, anakhala pa mpando wachifumu wa nîmedu ndipo anayendera zofunkha (zotengedwa) ku Lakisi (La-ki-su).”6

Chithunzi chimenechi ndi mawu akewo, zimene munthu angaone ku British Museum, zikugwirizana ndi nkhani ya m’Baibulo yakuti Sanakeribu analanda mzinda wa Yuda wa Lakisi, yolembedwa pa 2 Mafumu 18:​13, 14. Pokambapo za tanthauzo la zimene anapezazo, Layard akulemba kuti: “Kodi ndani akanakhulupirira kuti zinali zotheka, tisanapeze zimenezi, kuti pansi pa nthaka ndi mabwinja pamene panali Nineve, pangapezeke mbiri ya nkhondo za Hezekiya [mfumu ya Yuda] ndi Sanakeribu, yolembedwa ndi Sanakeribu mwiniyo panthaŵi yomwe anali kumenyana, ndi kutsimikiza kotheratu kuti mbiri ya Baibulo njoona?”7

Akatswiri ofukula m’mabwinja akumba zinthu zina zambiri​—ziŵiya zadothi, mabwinja, mapale, makobiri, zikalata, zipilala, ndi miyala yozokota—​zimene zimatsimikiza kuti Baibulo nlolondola. Okumba zokumbakumba afukula mzinda wa Akaldayo wa Uri, malo a malonda ndi chipembedzo kumene Abrahamu anali kukhala.8 (Genesis 11:​27-​31) Mbiri ya Nabonidus, mwala womwe anaufukula m’zaka za zana la 19, umasimba kuti Koresi Wamkulu anagwetsa Babulo mu 539 B.C.E., chochitika chomwe Danieli chaputala 5 amasimba.9 Mwala wina wozokota (zidutswa zake zikusungidwa mu British Museum) umene unapezeka pakhoma la pakhomo ku Tesalonika wakale uli ndi maina a akulu a mzindawo otchedwa “politarchs,” liwu losadziŵika m’mabuku a akatswiri achigiriki koma limene mlembi wa Baibulo, Luka, analigwiritsira ntchito.10 (Machitidwe 17:​6, NW, mawu amtsinde) Motero zinatsimikizidwa kuti Luka analondola​—muja zinakhaliranso ndi mfundo zake zina.​—Yerekezerani ndi Luka 1:3.

Komabe, si nthaŵi zonse pamene akatswiri ofukula m’mabwinja amagwirizana iwo okha, ndipo si nthaŵi zonse pamene amagwirizana ndi Baibulo. Ngakhale zili choncho, Baibulo lili nawo umboni wamphamvu mkati mwake wakuti ndi buku lomwe tingalikhulupirire.

Limafotokoza Nkhani Zake Mosabisa

Olemba mbiri oona mtima anali kulemba osati chabe za kulakika (monga mawu ozokota osimba kuti Sanakeribu analanda Lakisi) komanso za kugonja, osati chabe za kukhoza komanso kulephera, osati chabe za kulimba komanso za kufooka. Pa mbiri zakudziko, ndi zoŵerengeka zokha zimene zili zoona mtima choncho.

Za olemba mbiri achisuri, Daniel D. Luckenbill akufotokoza kuti: “Nthaŵi zambiri nzachionekere kuti chifukwa cha kunyada kwa mafumu, amafunika kusintha mwamachenjera choonadi cha mbiri yawo.”11 Monga chitsanzo cha “kunyada kwa mafumu” kumeneko, Mfumu Ashurnasirpal ya Asuri analemba mawu awa podzitama: “Ndine wamkulukulu, ndine wotamandika, ndi wokwezeka, ndine wolimba, ndine wolemekezeka, ndine waulemerero, ndine womveka, ndine wamphamvu, ndine chilombo, ndine mkango, ndine ngwazi!”12 Kodi mungavomereze kuti zonse zomwe mukuŵerenga m’zolemba ngati zimenezo ndi mbiri yolondola?

Komabe, olemba Baibulo sanabise kanthu, ndipo zimenezi zimapatsa munthu chidaliro. Mose, mtsogoleri wa Israyeli, anasimba mosabisa zolakwa za mbale wake, Aroni, za mlongo wake Miriamu, za Nadabu ndi Abihu ana a mbale wake, za anthu ake, ndi zolakwa zake zomwe. (Eksodo 14:​11, 12; 32:​1-6; Levitiko 10:​1, 2; Numeri 12:​1-3; 20:​9-12; 27:​12-14) Zolakwa zazikulu za Mfumu Davide sizinabisidwe koma zinalembedwa​—ndipotu pamene Davide anali kulamulira monga mfumu. (2 Samueli machaputala 11 ndi 24) Mateyu, wolemba buku lotchedwa ndi dzina lake, akusimba mmene atumwi (nayenso anali mmodzi wa iwo) anakanganirana ponena zakuti wamkulu ndani ndi mmene anasiyira Yesu usiku womwe iye anagwidwa. (Mateyu 20:​20-24; 26:56) Olemba makalata a m’Malemba Achigiriki Achikristu anatchula mosabisa mavuto, kuphatikizapo chisembwere ndi magaŵano, zimene zinali m’mipingo ina yoyambirira yachikristu. Ndipo sanapite m’mbali polankhula za mavutowo.​—1 Akorinto 1:​10-13; 5:​1-13.

Kufotokoza zinthu mosabisa ndi momasuka choncho kumasonyeza kuti cholinga chawo chinali kunena choonadi. Popeza kuti olemba Baibulo anali okonzeka kusimba zinthu zosakondweretsa ponena za okondedwa awo, anthu awo, ngakhale iwo eniwo, kodi sitili ndi chifukwa chabwino chokhulupirira zolemba zawo?

Analondola Popereka Tsatanetsatane Wake

Pamlandu wa m’khoti kudalirika kwa zokamba za mboni nthaŵi zambiri kungadziŵike mwa kuyang’ana pa mfundo zazing’ono. Ngati maumboni aang’onong’onowo akugwirizana amatsimikiza kuti zokambazo nzolondola ndipo nzoona, pamene ngati sakutsatirika konse angasonyeze kuti nzopeka. Komanso, mafotokozedwe opambanitsa kutsatirika kwake​—amene maumboni ake onse alinganizidwa bwinobwino—​angavumbulenso kuti zokambazo nzabodza.

Kodi “zokamba” za olemba Baibulo zikuchita bwanji pamenepa? Olemba Baibulo anali ogwirizana kwambiri. Kugwirizanako kumaoneka ngakhale patinthu tating’onong’ono. Komabe, kugwirizanako sikochita kulinganiza bwinobwino, zimene zikanatikayikitsa kuti mwina anayamba amvana. Nzachionekere kuti kufanana kwa zokamba zawo nkosakhalira pansi kupangana, poti olembawo nthaŵi zambiri agwirizana pachinthu chimodzi mosadziŵa. Tiyeni tipende zitsanzo zingapo.

Mateyu, wolemba Baibulo, analemba kuti: ‘Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo.’ (Mateyu 8:​14) Panopa Mateyu akupereka mfundo yabwino koma yosafunika kwenikweni: Yakuti Petro anali wokwatira. Mfundo yaing’ono imeneyi anaichirikiza Paulo, yemwe analemba kuti: “Kodi sindiyenera ine kumtenga mkazi wachikristu ndi kuyendayenda naye, monganso atumwi ena ndi . . . Kefa?”b (1 Akorinto 9:​5, The New English Bible) Nkhani yake ikusonyeza kuti Paulo anali kupereka chodzikanira ponenezedwa kosayenera. (1 Akorinto 9:​1-4) Mwachionekere, mfundo yaing’ono imeneyi​—yakuti Petro anali wokwatira​—Paulo sakuitchula kuti achirikize nkhani ya Mateyu kuti njolondola koma wangoitchula ngati mfundo wamba.

Onse anayi olemba Mauthenga Abwino​—Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane—​akutchula kuti usiku womwe Yesu anagwidwa, mmodzi wa ophunzira ake anasolola lupanga nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, kumdula khutu. Uthenga Wabwino wa Yohane ndiwo wokha umene umatchula mfundo yooneka ngati yosafunika kwenikweni: “Dzina lake la kapoloyo ndiye Malko.” (Yohane 18:​10, 26) Nanga nchifukwa ninji Yohane yekha ndiye akutchula dzina la mwamunayo? Mavesi angapo pambuyo pake, nkhaniyo ikutchula mfundo yaing’ono yosatchulidwa kwina kulikonse: Yohane “anadziŵika kwa mkulu wa ansembe.” Anadziŵikanso kwa banja la mkulu wa ansembe; akapolonso anali kumdziŵa, ndipo iye anali kuwadziŵa. (Yohane 18:​15, 16) Pamenepa, nzachibadwa kuti Yohane anatchula dzina la mwamuna wovulalayo, pamene ena olemba Mauthenga Abwino, amene sanamdziŵe mwamunayo, sanalitchule.

Nthaŵi zina, nkhani ina imalumpha mafotokozedwe atsatanetsatane koma iwo amadzatchulidwa kwina m’ndemanga zokambidwa ngati zosafunika kwenikweni. Mwachitsanzo, nkhani ya Mateyu ya mlandu wa Yesu pamaso pa Sanhedrin yachiyuda imatero kuti anthu omwe analipo ‘anampanda kofu, nati, Utilote ife, Kristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?’ (Mateyu 26:​67, 68) Kodi nchifukwa ninji iwo anauza Yesu ‘kulota’ amene anammenya, pamene wommenyayo anaimirira patsogolo pake? Mateyu sakufotokoza. Koma ena aŵiri olemba Mauthenga Abwino akutchula mfundo imene iye analumpha: Omzunza Yesu anaphimba nkhope yake asanammenye. (Marko 14:65; Luka 22:64) Mateyu akufotokoza nkhani yakeyo osasamala kuti kaya mfundo iliyonse waitchula.

Uthenga Wabwino wa Yohane umasimba za nthaŵi ina imene khamu lalikulu linasonkhana kudzamva Yesu akuphunzitsa. Malinga ndi nkhaniyo, pamene Yesu anayang’ana khamulo, ‘ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?’ (Yohane 6:5) Pa ophunzira onse omwe analipo, nchifukwa ninji Yesu anafunsa Filipo kumene akanagula mkate? Wolembayo sakunena. Komabe, m’nkhani imodzimodzi, Luka akutchula kuti zimenezo zinachitikira pafupi ndi Betsaida, mzinda wakugombe la kumpoto kwa Nyanja ya Galileya, ndipo poyamba Uthenga Wabwino wa Yohane umati “Filipo anali wa ku Betsaida.” (Yohane 1:​44; Luka 9:​10) Choncho Yesu moyenerera anafunsa munthu amene mudzi wake unali pafupi. Kugwirizana kwa mfundozo nkodabwitsa, koma nzachionekere kuti iwo sanadziŵe.

Nthaŵi zina kusatchula mfundo zina kumangowonjeza kudalirika kwake kwa wolemba Baibulo. Mwachitsanzo, wolemba 1 Mafumu akusimba za chirala choopsa m’Israyeli. Chinali choopsadi koti mfumu sinathe kupeza madzi ndi msipu zokwanira kuti akavalo ake ndi nyulu zikhale moyo. (1 Mafumu 17:7; 18:5) Komabe, nkhani imodzimodziyo ikusimba kuti mneneri Eliya analamula kuti ambweretsere madzi ambiri pa Phiri la Karimeli (ogwiritsira ntchito popereka nsembe) kuti adzaze nawo mchera wozungulira malo aakulu ngati masikweya mita 1,000. (1 Mafumu 18:​33-35) Mkati mwa chirala, kodi madzi onsewo anawachotsa kuti? Wolemba 1 Mafumu sanadzivute nkuyesa kufotokoza. Komabe, aliyense wokhala m’Israyeli anadziŵa kuti Karimeli anali kugombe la Mediterranean Sea, monga momwe mawu ongotchulidwa pambuyo pake m’nkhaniyo akusonyezera. (1 Mafumu 18:43) Chotero, madzi a m’nyanja ayenera kuti sanavute kupeza. Ngati buku limeneli limene m’mbali zina limafotokoza zinthu mwatsatanetsatane linali longopeka koma nkumanamizira kukhala loona, nchifukwa ninji wolilemba, amene akanakhala wonyenga wochenjera, anasiya mbali imeneyo yooneka ngati yovuta m’nkhaniyo?

Choncho kodi tingalikhulupirire Baibulo? Akatswiri ofukula m’mabwinja akumba zinthu zokwirira zokwanira kutsimikiza kuti Baibulo limatchula anthu enieni, malo enieni, ndi zochitika zenizeni. Komabe, umboni wamphamvu kwambiri koposa umenewo ndi uja wopezeka m’Baibulo. Olemba ake oona mtima sanasiye aliyense​—ngakhale iwo eniwo—​polemba zimene zinachitikadi. Kugwirizana kwa zimene analembamo, kuphatikizapo kunena chimodzimodzi kosapangana, kumatsimikiza kuti “zokamba” zawo nzoonadi. Pokhala ndi ‘umboni wotsimikizirika wakuti nloona’ ngati umenewu, Baibulo lilidi buku limene mungalikhulupirire.

[Mawu a M’munsi]

a Atapeza zimenezo, Profesa André Lemaire anatero kuti mzera wokonzedwanso pambuyo powonongeka wa pamwala wa Mesha (wodziŵikanso kuti Mwala wa Moabu), umene unapezeka m’chaka cha 1868, umasonyeza kuti mwalawo umatchulanso “Nyumba ya Davide.”4

b “Kefa” ndi dzina lachihebri lofanana ndi “Petro.”​—Yohane 1:​42.

[Chithunzi patsamba 15]

Chibenthu cha ku Tel Dan

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Chithunzi cha Asuri pakhoma chosonyeza kugwa kwa Lakisi, kotchulidwa pa 2 Mafumu 18:​13, 14

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena