-
“Mudzalakalaka Ntchito ya Manja Anu”Nsanja ya Olonda—2011 | March 1
-
-
Taganizirani zimene zinachititsa kuti Yobu alankhule mawu amenewa. Iye ankakhulupirira kwambiri Mulungu koma anakumana ndi mayesero aakulu. Chuma chake chinatha, ana ake onse anafa ndiponso iyeyo anadwala matenda owawa kwambiri. Atathedwa nzeru, iye anapemphera kwa Mulungu kuti: “Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda.” (Vesi 13) Yobu ankaona kuti munthu akapita ku Manda ndiye kuti wasiyana ndi mavuto. Ankaona kuti ku Mandako akakhala ngati chuma chimene Mulungu wachibisa ndipo sakakhalanso ndi mavuto komanso sadzikamvanso ululu.a
Kodi ndiye kuti Yobu akanakhalabe ku Mandako mpaka kalekale? Yobu sanaganize choncho. Iye anapitiriza kupemphera kuti: “Zikanakhala bwino . . . mukanati mundiikire nthawi n’kudzandikumbukira.” Yobu ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti sadzakhala ku Mandako mpaka kalekale chifukwa Yehova adzamukumbukira. Iye anayerekezera nthawi imene adzakhale m’Manda ndi “ntchito yokakamiza,” kutanthauza kuti adzakakamizika kudikirira mpaka adzaukitsidwe. Koma kodi anafunika kudikira kwa nthawi yaitali bwanji? Iye anati: “Mpaka mpumulo wanga utafika.” (Vesi 14) Mpumulo umenewu ukutanthauza kuukitsidwa ku Manda.
-
-
“Mudzalakalaka Ntchito ya Manja Anu”Nsanja ya Olonda—2011 | March 1
-
-
a Buku lina limanena kuti mawu a Yobu akuti “mukanandibisa,” ayenera kuti ankatanthauza kuti “munditeteze ngati chuma chamtengo wapatali.” Komanso buku lina limanena kuti pamenepa Yobu ankatanthauza kuti “mundibise ngati chuma chamtengo wapatali.”
-