Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g21 No. 1 tsamba 14
  • Tikamudziwa Bwino Mlengi Wathu Timafuna Kukhala Anzake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tikamudziwa Bwino Mlengi Wathu Timafuna Kukhala Anzake
  • Galamukani!—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mlengi Wathu Ali ndi Dzina
  • Yehova Ndi Mulungu Wachikondi
  • Yehova Ndi Mulungu Amene Amakhululuka
  • Yehova Amamva Mapemphero Athu
  • ‘Pitirizani Kukhululukirana Eni Okha’
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Yehova Amakhululuka Kwambiri Kuposa Aliyense
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Mukudziwa Zotani Zokhudza Mulungu?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Galamukani!—2021
g21 No. 1 tsamba 14

Tikamudziwa Bwino Mlengi Wathu Timafuna Kukhala Anzake

Mlengi wathu si mphamvu chabe. Koma ali ndi makhalidwe ochititsa chidwi. Ndipo iye amafuna kuti tiphunzire za iyeyo komanso tikhale anzake. (Yohane 17:3; Yakobo 4:8) N’chifukwa chake amatiuza zambiri zokhudza iyeyo.

Mlengi Wathu Ali ndi Dzina

“Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”​—SALIMO 83:18.

Baibulo limaphunzitsa kuti Yehova ndi Mulungu woona. Iye ndi amene analenga chilengedwe chonse komanso zamoyo zonse. Choncho iye yekha ndi amene tiyenera kumulambira.​—Chivumbulutso 4:11.

Yehova Ndi Mulungu Wachikondi

Dzina la mlengi lakuti Yehova lalembedwa mu Chihindi, Chipunjabi, Chigujarati, Chitelugu, Chitamiwu komanso Chingelezi.

“Mulungu ndiye chikondi.”​—1 YOHANE 4:8.

Yehova amagwiritsa ntchito Baibulo komanso zinthu zimene analenga potiphunzitsa za makhalidwe ake. Khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. Zonse zimene amachita amazichita chifukwa chachikondi. Tikamaphunzira zambiri zokhudza Yehova m’pamenenso timayamba kumukonda kwambiri.

Yehova Ndi Mulungu Amene Amakhululuka

“Inu ndinu Mulungu wokhululuka.”​—NEHEMIYA 9:17.

Yehova amadziwa kuti si ife angwiro. Choncho amakhala wokonzeka ‘kutikhululukira.’ Tikavomereza kuti talakwitsa komanso n’kuyesetsa kusiya zoipa zimene tachitazo, iye amatikhululukira ndipo samatipatsa chilango chifukwa cha zimene talakwitsazo.​—Salimo 103:12, 13.

Yehova Amamva Mapemphero Athu

“Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”​—SALIMO 145:18, 19.

Yehova safuna kuti tizichita miyambo inayake kapena kugwiritsa ntchito zithunzi ndi zifaniziro pomulambira. Iye amamvetsera mapemphero athu mofanana ndi mmene makolo amamvetserera ana awo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena