Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 2/1 tsamba 4-6
  • Maziko Olimba Oyembekezerera Zinthu Zabwino Lerolino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maziko Olimba Oyembekezerera Zinthu Zabwino Lerolino
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Abrahamu Afupidwa Chifukwa Choyembekezera Zinthu Zabwino
  • Azondi Aŵiri Amene Anayembekezera Zinthu Zabwino
  • Kukayikira kwa Yona
  • Kuyembekezera Zinthu Zabwino Pakati pa Mavuto
  • Kuyembekezera Zinthu Zabwino Koona Kumalakika!
  • Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Yona Aphunzira za Chifundo cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Anaphunzira pa Zolakwa Zake
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 2/1 tsamba 4-6

Maziko Olimba Oyembekezerera Zinthu Zabwino Lerolino

WOLEMBA mbiri ndi katswiri wa chikhalidwe cha anthu H. G. Wells, yemwe anabadwa mu 1866, anasonkhezera mwamphamvu kaganizidwe ka m’zaka za zana la 20. Mwa zimene analemba, anafotokoza chikhulupiriro chake kuti kupitabe patsogolo kwa sayansi kudzabweretsa nthaŵi yosangalatsa kwambiri. Choncho, Collier’s Encyclopedia ikunena za “kuyembekezera zinthu zabwino kopanda malire” kwa Wells pamene mosalekeza anagwira ntchito kuti awanditse zikhulupiriro zake. Koma ikunenanso kuti chiyembekezo chake cha zinthu zabwino chinasweka pamene Nkhondo Yadziko II inaulika.

Pamene Wells anazindikira kuti “sayansi ingabweretse zoipa ndiponso zabwino, chikhulupiriro chake chinatha, ndipo anayamba kuyembekezera zinthu zoipa,” ikutero Chambers’s Biographical Dictionary. Kodi izi zinachitika chifukwa chiyani?

Chikhulupiriro cha Wells ndi kuyembekezera kwake zinthu zabwino zinazikidwa kotheratu pa zipambano za anthu. Pamene anazindikira kuti munthu anali wosakhoza kubweretsa mkhalidwe wosangalatsa kwambiri, analibenso kopita. Kutaya kwake chikhulupiriro mwamsanga kunakhala kuyembekezera zoipa.

Anthu ambiri lerolino zimenezi zawachitikira pa zifukwa zofananazo. Amakhala odzala ndi chiyembekezo cha zinthu zabwino pamene ali ana koma iwo atakula amakhumudwa ndi kutaya chiyembekezocho. Pali ngakhale achinyamata amene amasiya moyo umene tingati ndi wozoloŵereka ndi kuyamba kugwiritsa ntchito molakwa mankhwala osokoneza bongo, kuchita zachiwerewere, ndi mikhalidwe ina yowononga moyo. Kodi yankho lake nchiyani? Talingalirani za zitsanzo izi za m’nthaŵi za m’Baibulo ndipo onani maziko a kuyembekezera zinthu zabwino amene alipo​—kale, tsopano, ndi mtsogolo.

Abrahamu Afupidwa Chifukwa Choyembekezera Zinthu Zabwino

M’chaka cha 1943 B.C.E, Abrahamu anachoka ku Harana, nawoloka mtsinje wa Firate ndi kuloŵa m’dziko la Kanani. Abrahamu wafotokozedwa kukhala “kholo la onse akukhulupira,” ndipo ndi chitsanzo chabwino chotani nanga chimene anapereka!​—Aroma 4:11.

Abrahamu anatsagana ndi Loti, mwana wamasiye wa mbale wake, ndi banja lake la Loti. Pambuyo pake, pamene m’dzikomo munagwa njala, mabanja aŵiriwa anapita ku Aigupto ndipo panthaŵi yake anabwereranso pamodzi. Tsopano Abrahamu ndi Loti anali ndi chuma chambiri kuphatikizapo nkhosa ndi ng’ombe. Pamene mkangano unabuka pakati pa abusa awo, Abrahamu anayambirira kuchitapo kanthu anati: “Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale. Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukamka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndimka ku dzanja lamanja: ukamka iwe ku dzanja lamanja, ine ndimka ku dzanja lamanzere.”​—Genesis 13:8, 9.

Pokhala wamkulu, Abrahamu akanatha kuchita zinthu moti zimukomere iyeyo, ndipo Loti akanavomereza monyinyirika chosankhacho chifukwa chowapatsa ulemu atate akewo. M’malo mwake, “Loti anatukula maso ake nayang’ana chigwa chonse cha Yordano kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanawononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Aigupto pakumka ku Zoari. Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordano.” Ndi chosankha choterocho Loti anayeneradi kuyembekezera zinthu zabwino. Koma bwanji za Abrahamu?​—Genesis 13:10, 11.

Kodi Abrahamu anapusa akumaika ubwino wa banja lake pangozi? Ayi. Abrahamu anafupidwa kwambiri chifukwa cha maganizo ake abwino ndi mzimu wake woolowa manja. Yehova anati kwa Abrahamu: “Tukulatu maso ako, nuyang’ane kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwera, ndi kummawa, ndi kumadzulo: chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbewu yako nthaŵi yonse.”​—Genesis 13:14, 15.

Kuyembekezera zinthu zabwino kwa Abrahamu kunali ndi maziko olimba. Kunazikidwa pa lonjezo la Mulungu lakuti mwa Abrahamu adzatulutsa mtundu waukulu kotero kuti “mwa [iye] adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.” (Genesis 12:2-4, 7) Ifenso tili ndi chifukwa chokhalira ndi chidaliro, pakuti tidziŵa kuti “amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino.”​—Aroma 8:28.

Azondi Aŵiri Amene Anayembekezera Zinthu Zabwino

Zaka zoposa 400 pambuyo pake, mtundu wa Israyeli unali pafupi kuloŵa m’Kanani, “m’dziko moyenda mkaka ndi uchi.” (Eksodo 3:8; Deuteronomo 6:3) Mose anatuma akalonga 12 kuti ‘akazonde dziko ndi kubwezera mawu akunena za njira ya kukwera nayo iwo pomka komweko, ndi za midzi yoti adzafikeko.’ (Deuteronomo 1:22; Numeri 13:2) Azondi onse 12 anali ogwirizana pakalongosoledwe kawo ka ulemerero wa dzikolo, koma 10 a iwo analankhula zosalimbikitsa, zimene zinabweretsa mantha m’mitima ya anthu.​—Numeri 13:31-33.

Kumbali ina, Yoswa ndi Kalebi anapereka uthenga woyembekezeretsa zabwino ndipo anayesetsa kuti athetse mantha amene anali nawo. Kaonedwe kawo ka zinthu ndi lipoti lawo zinasonyeza chidaliro chotheratu m’mphamvu ya Yehova ya kukwaniritsa lonjezo lake la kuwabwezeretsa ku Dziko Lolonjezedwa​—koma sizinathandize. M’malo mwake “khamu lonse lidati liwaponye miyala.”​—Numeri 13:30; 14:6-10.

Mose analimbikitsa anthuwo kuti akhulupirire Yehova koma iwo sanamvere. Chifukwa chakuti anaumirira kusayembekezera zabwino, mtundu wonsewo unazungulira m’chipululu kwa zaka 40. Mwa azondi 12 onsewo, kokha Yoswa ndi Kalebi ndiwo analandira mphotho ya kuyembekezera zinthu zabwino. Kodi vuto lenileni linali chiyani? Kusoŵa chikhulupiriro, popeza anthuwo anadalira pa nzeru za iwo eni.​—Numeri 14:26-30; Ahebri 3:7-12.

Kukayikira kwa Yona

Yona anakhalapo ndi moyo m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E. Baibulo limasonyeza kuti anali mneneri wokhulupirika wa Yehova mu ufumu wa mafuko khumi a Israyeli pamene Yerobiamu II anali kulamulira. Komatu anakana kutumidwa ku Nineve kuti akachenjeze anthu. Wolemba mbiri Josephus anati Yona “anaganiza kuti ndi bwino kuthaŵa” ndi kungopita ku Yopa. Kumeneko anakwera bwato kupita ku Tarisi, mwinamwake dziko limene tsopano likutchedwa Spain. (Yona 1:1-3) Chifukwa chimene Yona analili ndi maganizo oipa pantchito imeneyi chalongosoledwa pa Yona 4:2.

Pamapeto pake Yona anavomera kugwira ntchito yakeyo, koma anakwiya pamene anthu a ku Nineve analapa. Choncho Yehova anamphunzitsa phunziro labwino la kukhala wachifundo mwa kufotetsa ndi kupha mtengo wa msatsi umene Yona anali kukhala pamthunzi wake. (Yona 4:1-8) Moyenerera chisoni cha Yona pa kufa kwa mtengo chinafunikira kukhala pa anthu 120,000 a mu Nineve amene anali “osadziŵa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.”​—Yona 4:11.

Kodi tingaphunzirenji pa zimene zinachitikira Yonazi? Utumiki wopatulika sugwirizana ndi kuyembekezera zinthu zoipa. Ngati tizindikira chitsogozo cha Yehova ndi kuchitsatira ndi chidaliro chonse, tidzapambana.​—Miyambo 3:5, 6.

Kuyembekezera Zinthu Zabwino Pakati pa Mavuto

“Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa,” anatero Mfumu Davide. “Usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.” (Salmo 37:1) Umenewutu ndi uphungu wanzeru chifukwa lerolino tazingidwa ndi chisalungamo ndi kukonda choipa.​—Mlaliki 8:11.

Ngakhale kuti sitiwasirira anthu oipa, ndi kwapafupi kukhumudwa pamene tiona anthu abwino akuvutitsidwa ndi oipa kapena pamene ife eni tichitiridwa mosalungama. Zochitika zoterozo zingathe kutikhumudwitsa kwambiri kapena zingatipangitse kuyembekezera zinthu zoipa. Kodi tiyenera kuchitanji pamene tikumva choncho? Choyamba, tiyenera kukumbukira kuti anthu oipa sangangokhala ndi kumaganiza kuti zonse zili bwino ndi kuti sadzalangidwa. Salmo 37 limapitiriza kutitsimikizira mu vesi 2 kuti: “Adzawamweta [ochita zoipa] msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauŵisi.”

Ndiponso, tingapitirizebe kuchita chabwino, kukhalabe oyembekezera zinthu zabwino ndi kuyembekezera Yehova. “Siyana nacho choipa, nuchite chokoma, nukhale nthaŵi zonse,” anapitiriza motero wamasalmo. “Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake.”​—Salmo 37:27, 28.

Kuyembekezera Zinthu Zabwino Koona Kumalakika!

Nanga bwanji za mtsogolo mwathu? Buku la Baibulo la Chivumbulutso likutiuza za “[zinthu zimene, NW] ziyenera kuchitika pasachedwapa.” Pakati pa zimenezi, wokwera pa kavalo wofiira, kusonyeza nkhondo, akuvumbulutsidwa kukhala “[a]kuchotsa mtendere padziko.”​—Chivumbulutso 1:1; 6:4.

Malingaliro ofala​—ndi oyembekezera zinthu zabwino​—amene anthu a ku Britain anali nawo panthaŵi ya Nkhondo Yadziko I anali akuti nkhondoyo inali nkhondo yaikulu yotsiriza. Mu 1916, nduna ya Britain David Lloyd George inanena zoona. Iye anati: “Nkhondo iyi, ngatinso nkhondo yotsatira, ndi nkhondo yothetsa nkhondo.” (Kanyenye ngwathu.) Analondola. Nkhondo Yadziko II inangopititsa patsogolo kapezedwe ka njira za nkhanza kwambiri zopululutsira anthu. Pambuyo pa zaka zoposa 50, kutha kwa nkhondo sikunayambebe kuoneka.

M’buku la Chivumbulutso lomwelo, timaŵerenganso za anthu enanso okwera pa akavalo​—kusonyeza njala, miliri ndi imfa. (Chivumbulutso 6:5-8) Ali mbali ina ya chizindikiro cha nthaŵi zino.​—Mateyu 24:3-8.

Kodi zimenezi ziyenera kuchititsa munthu kuyembekezera zinthu zoipa? Kutalitali, pakuti masomphenyawo akulongosolanso za “kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nawo uta; ndipo anampatsa kolona; ndipo anatulukira wolakika kuti alakike.” (Chivumbulutso 6:2) Tikuona Yesu Kristu monga Mfumu ya kumwamba akuchotsa kuipa konse, kuti akhazikitse mtendere ndi chiyanjano padziko lonse.a

Monga Mfumu Yosankhidwa, Yesu Kristu pamene anali pano padziko lapansi anaphunzitsa ophunzira ake kupempherera Ufumuwo. Mwinamwake inunso munaphunzitsidwa kunena pemphero la “Atate Wathu wa Kumwamba,” kapena kuti Pemphero la Ambuye. M’pempheroli timapempha kuti Ufumu wa Mulungu udze, kuti chifuniro chake chichitidwe pano padziko lapansi monga kumwamba.​—Mateyu 6:9-13.

M’malo moika zigamba padongosolo lino la zinthu, Yehova, kupyolera mwa Mfumu yake Yaumesiya, Kristu Yesu, adzalichotseratu. M’malo mwake, Yehova akuti, “ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.” M’boma la Ufumu lakumwamba, dziko lapansi lidzakhala mudzi wa anthu wamtendere ndi wosangalatsa, kumene moyo ndi ntchito zidzakhala zokondweretsa nthaŵi zonse. “Khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga,” akutero Yehova. “Osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.” (Yesaya 65:17-22) Ngati muzika chiyembekezo chanu chamtsogolo pa lonjezo losalephera limenelo, mudzakhala ndi chifukwa chabwino choyembekezerera zinthu zabwino​—tsopano lino ndi mtsogolo kosatha!

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze malongosoledwe atsatanetsatane a masomphenya amenewa, chonde onani chaputala 16 cha buku lakuti Revelation​—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 4]

H. G. Wells

[Mawu a Chithunzi]

Corbis-Bettmann

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena