Yehova Samapeputsa Mtima Wosweka
“Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.”—SALMO 51:17.
1. Kodi Yehova amawona motani olambira ake amene amachita tchimo lalikulu koma amene ali olapa?
YEHOVA angathe ‘kutsekereza kumyandikira monga ngati ndi mtambo wokhuthala, kuti pemphero lisapyole.’ (Maliro 3:44) Koma iye amafuna kuti anthu ake azimfikira. Ngakhale ngati mmodzi wa olambira ake angachimwe kwambiri koma ali wolapa, Atate wathu wakumwamba amakumbukira zabwino zochitidwa ndi munthuyo. Chifukwa chake, mtumwi Paulo anakhoza kuuza Akristu anzake kuti: ‘Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachiwonetsera ku dzina lake.’—Ahebri 6:10.
2, 3. Kodi akulu Achikristu ayenera kupenda chiyani posamalira ndi okhululupirira anzawo olakwa?
2 Akulu Achikristu ayenera kulingaliranso zaka za utumiki wokhulupirika zimene okhulupirira anzawo anapereka kwa Mulungu. Izi zimaphatikizapo utumiki wopatulika wochitidwa ndi olapawo amene atenga njira yolakwa kapena amene achitadi tchimo lalikulu. Abusa Achikristu amafunafuna ubwino wauzimu wa onse a m’gulu lankhosa la Mulungu.—Agalatiya 6:1, 2.
3 Wochita cholakwa wolapa afunikira chifundo cha Yehova. Komabe, zowonjezereka zikufunika. Zimenezi zamveketsedwa mwa mawu a Davide pa Salmo 51:10-19.
Mtima Woyera Ngwofunika
4. Kodi nchifukwa ninji Davide anapempherera mtima wangwiro ndi mzimu watsopano?
4 Ngati Mkristu wodzipatulira ali mumkhalidwe woipa wauzimu chifukwa cha uchimo, kodi iye angafunikirenji kusiyapo chifundo cha Yehova ndi chikhululukiro? Eya, Davide anapempha kuti: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika mkati mwanga.” (Salmo 51:10) Mwachiwonekere, Davide anapereka pempho limeneli chifukwa cha kuzindikira kuti chikhoterero cha tchimo lalikulu chinali chikhalirebe mu mtima mwake. Kungakhale kwakuti ife sitinaphatikizidwe m’mitundu ya uchimo imene inakola Davide m’chochitika chokhudza Bateseba ndi Uriya, koma tifunikira chithandizo cha Yehova kuti tipeŵe kugonjera chiyeso cha kuphatikizidwa mumkhalidwe uliwonse wa tchimo lalikulu. Chifukwa chake, aliyense wa ife angafunikire chithandizo chaumulungu chakuchotsa mumtima mwathu mikhalidwe yauchimo yotero monga ngati kusirira ndi chidani—maupandu ophatikizapo kuba ndi kuchita mbanda.—Akolose 3:5, 6; 1 Yohane 3:15.
5. (a) Kodi kumatanthauzanji kukhala ndi mtima wangwiro? (b) Kodi Davide anakhumba chiyani pamene anapempha mzimu watsopano?
5 Yehova amafuna kuti atumiki ake akhale ndi “mtima woyera,” ndiko kuti, chiyero m’cholinga kapena m’chifuno. Pozindikira kuti sanasonyeze chiyero chotero, Davide anapemphera kuti Mulungu ayeretse mtima wake ndi kuuchititsa kukhala wogwirizana ndi miyezo ya Mulungu. Wamasalmoyo anafunanso mzimu watsopano, wolungama, kapena chikhoterero cha maganizo. Iye anafunikira mzimu umene ukanamthandiza kukaniza chiyeso ndi kumamatira zolimba ku malamulo a Yehova ndi malamulo amakhalidwe abwino.
Mzimu Woyera Ngwofunika
6. Kodi nchifukwa ninji Davide anapempha Yehova kusachotsa mzimu woyera pa iye?
6 Pamene tiri ogwiritsidwa mwala chifukwa cha zophophonya zathu kapena cholakwa, tikakhoza kumva kuti Mulungu ali pafupi kutinyanyala ndi kutichotsera mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito. Davide anamva mwanjirayo, pakuti anapempha Yehova kuti: ‘Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere mzimu wanu woyera.’ (Salmo 51:11) Davide wolapa ndi wodzichepetsa anamva kuti machimo ake anampangitsa kukhala wosayenerera kutumikira Yehova. Kutayidwa pamaso pa Mulungu kukatanthauza kutaya chiyanjo chake, chitonthozo, ndi dalitso. Ngati Davide anali kudzabwezeretsedwa mwauzimu, iye anafunikira mzimu woyera wa Yehova. Pokhala nawo pa iye, mfumuyo ikafunafuna mwapemphero chitsogozo chaumulungu kotero kuti akondweretse Yehova, akakhoze kupeŵa tchimo, ndipo akakhoza kulamulira mwanzeru. Pozindikira machimo ake motsutsana ndi Mpatsi wa mzimu woyera, Davide moyenerera anachonderera kuti Yehova asauchotse kwa iye.
7. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupempherera mzimu woyera ndi kusamala kusauchititsa chisoni?
7 Bwanji za ife? Tiyenera kupempherera mzimu woyera ndipo tiyenera kukhala maso motsutsana ndi kuumvetsa chisoni mwakulephera kulondola chitsogozo chake. (Luka 11:13; Aefeso 4:30) Apo phuluzi, tikatayikiridwa ndi mzimu ndipo tikakhala osakhoza kusonyeza zipatso zake zoperekedwa ndi Mulungu za chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, ubwino, chikhulupiriro, chifatso, ndi kudziletsa. Kwakukulukulu Yehova Mulungu akachotsa mzimu wake woyera kwa ife ngati mosalapa tinapitirizabe kumchimwira.
Chimwemwe cha Chipulumutso
8. Ngati tichimwa koma tifuna kukhala ndi chisangalalo chachipulumutso, kodi tifunikira kukhala ndi chiyani?
8 Wochimwa wolapa amene amabwezeretsedwa mwauzimu angakondwerenso ndi kakonzedwe ka Yehova ka chipulumutso. Akumalakalaka kakonzedweka, Davide anapempha Mulungu kuti: ‘Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize.’ (Salmo 51:12) Kunali kokondweretsa chotani nanga kukondwera m’chiyembekezo chowona cha chipulumutso chochitidwa ndi Yehova Mulungu! (Salmo 3:8) Pambuyo pakuchimwira Mulungu, Davide anafunafuna kubwezeretsedwera chisangalalo cha chipulumutso chochitidwa ndi Iye. M’nthaŵi za pambuyo pake, Yehova anapereka chipulumutsocho kupyolera mwa nsembe ya dipo ya Mwana wake, Yesu Kristu. Ngati ife monga atumiki odzipatulira a Mulungu tichita tchimo lalikulu koma tifuna kupeza chisangalalo cha chipulumutso kuti chibwezeretsedwe kwa ife, tifunikira kukhala ndi mkhalidwe wakulapa kotero kuti tipeŵe kuchimwira mzimu woyera.—Mateyu 12:31, 32; Ahebri 6:4-6.
9. Kodi Davide anali kupempha chiyani pamene anapempha Mulungu kumchirikiza “ngakhale ndi mzimu wofunitsitsa”?
9 Davide anapempha kuti Yehova amchirikize “ngakhale ndi mzimu wofunitsitsa.” Mwachiwonekere, izi sizikusonya kukufunitsitsa kwa Mulungu kukhala wothandiza kapena ku mzimu wake woyera, koma kumkhalidwe wa maganizo wosonkhezera wa Davide. Davide anafuna Mulungu kumchirikiza mwakumpatsa mzimu wakufunitsitsa kuchita cholungama ndipo osati kugwera mu uchimo kachiŵirinso. Yehova Mulungu amachirikiza mosalekeza atumiki ake nawawongola pokowamitsidwa ndi mayeso osiyanasiyana. (Salmo 145:14) Nkotonthoza chotani nanga kuzindikira chimenechi, makamaka ngati tachimwa koma tiri olapa ndipo tifuna kutumikirabe Yehova mokhulupirika!
Kuphunzitsa Ochimwa Chiyani?
10, 11. (a) Kodi Davide akanaphunzitsa chiyani ochimwa Achiisrayeli? (b) Kodi Davide akanaphunzitsa ochimwa kokha pambuyo pakuchita chiyani iyemwini?
10 Ngati Mulungu akalola, Davide mopanda dyera anafuna kuchita kanthu kena kamene kakasonyeza kuyamikira kwake chifundo cha Yehova ndi kamene kakathandiza ena. Mwamalingaliro opemphera olunjikitsidwa kwa Yehova, mfumu yolapayo kenako inati: ‘Ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa inu.’ (Salmo 51:13) Kodi ndimotani mmene Davide wochimwayo akaphunzitsira ochimwa Chilamulo cha Mulungu? Kodi iye akawauza chiyani? Ndipo kodi chimenechi chikakwaniritsa chabwino chotani?
11 Pamene anali kusonyeza ochimwa Achiisrayeli njira za Yehova ali ndi chiyembekezo chakuwatembenuza kuchoka pamabande oipa, Davide akasonyeza mmene tchimo liliri mphulupulu, chimene kulapa kumatanthauza, ndi mmene akanalandirira chifundo cha Mulungu. Pokhala atamva ululu wamkwiyo wa Yehova ndi chikumbumtima cha liwongo, mosakaikira Davide akakhala mlangizi wokoma mtima wa ochimwa olapa, osweka mtima. Ndithudi, iye akagwiritsira ntchito chitsanzo chake kuphunzitsa ena kokha pambuyo poti iye mwini wavomereza miyezo ya Yehova ndipo walandira chikhululukiro Chake, chifukwa chakuti okana kugonjera malamulo a Mulungu alibe kuyenera kwa ‘kuwerengera malemba a Mulungu.’—Salmo 50:16, 17.
12. Kodi ndimotani mmene Davide anapindulira ndi chidziŵitso chakuti Mulungu anamlanditsa ku liwongo la mwazi?
12 Akumabwereza zolinga zake mumpangidwe wina, Davide anati: ‘Mundilanditse ku mlandu wamwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.’ (Salmo 51:14) Liwongo lamwazi linabweretsa chiweruzo cha mfa. (Genesis 9:5, 6) Chotero kuzindikira kuti Mulungu wa chipulumutso chake anamlanditsa kuliwongo la mwazi lokhudza Uriya kukapatsa Davide mtendere wa mtima ndi maganizo. Pamenepo lilime lake likaimba mwachisangalalo za chilungamo cha Mulungu, osati cha iyemwini. (Mlaliki 7:20; Aroma 3:10) Davide sakanafafaniza chisembwere chake kapena kuukitsa Uriya kumanda, monga momwedi munthu wamakono sangathe kubwezeretsa chiyero cha munthu amene wadetsa kapena kuukitsa munthu amene wamupha. Kodi sitiyenera kulingalira za zimenezo pamene tiyesedwa? Ndipo tiyenera kuyamikira kwambiri chotani nanga chifundo cha Yehova chosonyezedwa kwa ife m’chilungamo! Mchenicheni, chiyamikiro chiyenera kutisonkhezera kutsogolera ena ku Magwero aakulu amenewa achilungamo ndi chikhululukiro.
13. Kodi ndim’mikhalidwe yokha iti mu imene wochimwa angatsegule milomo yake moyenerera kutamanda Yehova?
13 Palibe wochimwa amene moyenerera angatsegule milomo yake kutamanda Yehova kusiyapo ngati Mulungu mokoma mtima aitsegula, kunena kwake titero, kulankhula chowonadi Chake. Chifukwa chake Davide anaimba kuti: “Ambuye, tsegulani pa milomo yanga; ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.” (Salmo 51:15) Pokhala chikumbumtima chake chitatonthozedwa chifukwa cha chikhululukiro cha Mulungu, Davide akasonkhezeredwa kuphunzitsa ochimwa njira za Yehova, ndipo akakhoza Kumtamanda mwaufulu. Onse amene akhululukidwa machimo awo monga momwe Davide anachitira ayenera kuyamikira chisomo cha Yehova kwa iwo, ndipo iwo ayenera kugwiritsira ntchito mpata uliwonse kulengeza chowonadi cha Mulungu ndi ‘kusimba zitamando zake.’—Salmo 43:3.
Nsembe Zovomerezedwa kwa Mulungu
14. (a) Kodi ndinsembe zotani zimene zinafunika mogwirizana ndi pangano Lachilamulo? (b) Kodi nchifukwa ninji kukakhala kulakwa kuganiza kuti tingathe kulipirira zolakwa zopitirizabe mwakuchita zinthu zabwino?
14 Davide anali atapeza chidziŵitso chozama chimene chinampangitsa kunena kuti: “Pakuti [Yehova] simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda.” (Salmo 51:16) Pangano Lachilamulo linafunikiritsa kuti nsembe za nyama ziperekedwe kwa Mulungu. Koma machimo a Davide akuchita chigololo ndi kupha, amene chilango chake chinali imfa, sakanatetezeredwa ndi nsembe zotero. Ngati zinali zotheka, iye akanalipirira mtengo uliwonse kuti apereke nsembe za nyama kwa Yehova. Popanda kulapa kowona mtima, nsembe ziri zopanda pake. Chifukwa chake kukakhala kulakwa kuganiza kuti tikakhoza kulipirira kuchita cholakwa kopitirizabe mwakuchita zinthu zina zabwino.
15. Kodi kaimidwe kamaganizo ka munthu wodzipatulira wokhala ndi mzimu wosweka nkotani?
15 Davide anawonjezera kuti: “Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.” (Salmo 51:17) Kwa wochimwa wolapa, ‘nsembe zovomerezeka kwa Mulungu ndizo mzimu wosweka.’ Munthu wotero samakhala ndi kaimidwe kamaganizo ka ndewu. Mtima wa munthu wodzipatulira wokhala ndi mzimu wosweka ngwachisoni kwambiri pa tchimo lake, ngwamanyazi chifukwa cha kuzindikira mkwiyo wa Mulungu, ndipo ngwofunitsitsa kuchita chiri chonse kupezanso chiyanjo cha Mulungu. Sitingapereke kwa Mulungu chinthu chiri chonse choyenerera kufikira titalapa machimo athu ndi kumpatsa mitima yathu m’kudzipereka kotheratu.—Nahumu 1:2.
16. Kodi ndimotani mmene Mulungu amawonera munthu wosweka mtima chifukwa cha uchimo wake?
16 Mulungu samakana nsembe monga ngati mtima wosweka ndi wopsinjika. Chifukwa chake, mosasamala kanthu za vuto lirilonse limene tikumana nalo monga anthu ake, tisagonjeretu ku kutaya mtima. Ngati takhumudwa panjira yamoyo mwanjira iriyonse imene ipangitsa mtima wathu kufuula kuti tipeze chifundo cha Mulungu, mkhalidwewo suuli wopanda chiyembekezo. Ngakhale ngati tachimwa kwadzawoneni koma ngati tiri olapa, Yehova sadzanyozera mtima wathu wosweka. Iye adzatikhululukira pa maziko ansembe ya dipo la Kristu ndipo adzatibwezeretsera ku chiyanjo Chake. (Yesaya 57:15; Ahebri 4:16; 1 Yohane 2:1) Komabe, mofanana ndi Davide, mapemphero athu ayenera kukhala opempha kubwezeretsedwa kwa chiyanjo cha Mulungu ndipo osati kuzemba chidzudzulo chofunika kapena chiwongolero. Mulungu anakhululukira Davide, komanso anamlanga.—2 Samueli 12:11-14.
Kudera Nkhaŵa Kulambira Koyera
17. Kuwonjezera pa kupempha chikhululukiro cha Mulungu, kodi ochimwawo ayenera kuchitanji?
17 Ngati tapalamula tchimo lalikulu, mosakaikira lidzavutitsa maganizo athu kwambiri, ndipo mtima wolapa udzatisonkhezera kupempha chikhululukiro cha Mulungu. Komabe, tiyeni tipemphererenso ena. Ngakhale kuti Davide anayang’anira mtsogolo kukupereka kulambira kovomerezeka kwa Mulungu kachiŵirinso, salmo lake silinasiye ena mwadyera m’nkhaniyo. Limaphatikizapo pempho ili kwa Yehova: ‘Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu.’—Salmo 51:18.
18. Kodi nchifukwa ninji Davide wolapayo anapempherera Ziyoni?
18 Inde, Davide anayang’anira mtsogolo kukubwezeretsedwa kwa chiyanjo cha Mulungu. Komabe, linalinso pemphero la wamasalmo wodzichepetsayo kuti ‘mokoma mtima Mulungu akachitire ziyoni,’ mzinda wa malikulu wa Israyeli, Yerusalemu, kumene Davide anayembekezera kumangako kachisi wa Mulungu. Machimo aakulu a Davide anawopseza mtundu wathunthu, popeza kuti anthu onse akanavutika chifukwa cha cholakwa cha mfumu. (Yerekezerani ndi 2 Samueli, chaputala 24.) M’chenicheni, machimo ake anafoketsa “malinga a Yerusalemu,” kotero kuti tsopano anafunikira kumangidwanso.
19. Ngati tinachimwa koma tinakhululukidwa, kodi nchiyani chimene moyenerera tiyenera kupempherera?
19 Ngati tachimwa momvetsa chisoni koma talandira chikhululukiro cha Mulungu, kukakhala koyenerera kupemphera kuti iye mwanjira ina yake akonzetse chivulazo chiri chonse chimene khalidwe lathu lachititsa. Tingakhale titabweretsa mtonzo pa dzina lake loyera, tingakhale titatonzetsa mpingo, ndipo tingakhale titabweretsa chisoni pa banja lathu. Atate wathu wakumwamba wachikondiyo angachotse mtonzo uliwonse woikidwa pa dzina lake, angathe kulimbikitsa mpingo kudzera mwa mzimu wake woyera, ndipo angathe kutonthoza mitima ya okondedwa athuwo amene amamkonda ndi kumtumikira. Ndithudi, kaya tchimo likuphatikizidwa kapena ayi, kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi ubwino wa anthu ake nthaŵi zonse ziyenera kukhala nkhaŵa yathu.—Mateyu 6:9.
20. Kodi ndim’mikhalidwe yotani mu imene Yehova akakondwerera nsembe ndi nsembe zopsereza za Aisrayeli?
20 Ngati Yehova anamanganso malinga a Ziyoni, kodi nchiyaninso chikachitika? Davide anaimba kuti: “Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe za chilungamo, ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu: Pamenepo adzapereka ng’ombe pa guwa lanu la nsembe.” (Salmo 51:19) Davide anali ndi chikhumbo chaphamphu chakuti iye ndi mtunduwo asangalale chiyanjo cha Yehova kotero kuti akhoze kumlambira movomerezeka. Pamenepo Mulungu akakhala wokondwera ndi nsembe zawo zopsereza ndi nsembe zathunthu. Zimenezi zikakhala choncho chifukwa chakuti zimenezi zikakhala nsembe za chilungamo zoperekedwa ndi anthu odzipatulira, owona mtima, ndi olapa okhala ndi chiyanjo cha Mulungu. Moyamikira chifundo cha Yehova, akapereka ng’ombe pa guwa lake lansembe—nsembe zabwino koposa ndi zokwera mtengo koposa. Lerolino, tikulemekeza Yehova mwakumbweretsera zabwino koposa za zimene tiri nazo. Ndipo nsembe zathu zimaphatikizapo nsembe za “ng’ombe zazing’ono za milomo yathu,” zachitamando kwa Mulungu wathu wachifundo, Yehova.—Hoseya 14:2; Ahebri 13:15.
Yehova Amamva Mfuu Zathu
21, 22. Kodi Salmo 51 liri ndi maphunziro otani otipindulitsa?
21 Pemphero lamtima wonse la Davide lolembedwa mu Salmo 51 limatisonyeza kuti tikachimwa tiyenera kuchita mwa mzimu wakulapa kowona mtima. Salmo limeneli lirinso ndi mfundo zotsimikizirika zotithandiza. Mwachitsanzo, ngati tichimwa koma tiri olapa, tingathe kukhala ndi chidaliro m’chifundo cha Mulungu. Komabe, kwakukulukulu tiyeni tidere nkhaŵa mtonzo uliwonse umene tingakhale titabweretsa pa dzina la Yehova. (Vesi 1-4) Mofanana ndi Davide, tingapemphe mochonderera chifundo kwa Atate wathu wakumwamba pa mkhalidwe wathu wauchimo wobadwa nawo. (Vesi 5) Tiyenera kulankhula chowonadi, ndipo tifunikira kufunafuna nzeru kwa Mulungu. (Vesi 6) Ngati tachimwa, tifunikira kupempha Yehova kutiyeretsa, mtima wangwiro, ndi mzimu wosandenguma.—Vesi 7-10.
22 Ndiponso tingathe kuwona mu Salmo 51 kuti sitiyenera konse kudzilola kuuma khosi mu uchimo. Ngati tikati tichite motero, Yehova akatichotsera mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito. Komabe, titakhala ndi mzimu wa Mulungu, tingathe kuphunzitsa ena mwachipambano njira zake. (Vesi 11-13) Ngati tiphophonya koma tilapa, Yehova adzatilola kupitirizabe kumtamanda chifukwa chakuti samapeputsa konse mtima wosweka ndi wopsinjika. (Vesi 14-17) Salmo limeneli limasonyezanso kuti mapemphero athu sayenera kusumika pa ife chabe. Mmalo mwake, tiyenera kupempherera dalitso ndi ubwino wauzimu wa onse ophatikizidwa m’kulambiridwa koyera kwa Yehova.—Vesi 18, 19.
23. Kodi nchifukwa ninji Salmo 51 liyenera kutisonkhezera kukhala olimba mtima ndi achiyembekezo?
23 Salmo lomvetsa chisoni la Davide limeneli liyenera kutisonkhezera kukhala olimba mtima ndi otsimikiza. Limatithandiza kuzindikira kuti sitifunikira kuganiza kuti zonse zataika ngakhale ngati tikhumudwa kuloŵa mu uchimo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ngati tilapa, chifundo cha Yehova chingatipulumutse kukugwiritsidwa mwala. Ngati tiri achisoni ndi odzipereka kotheratu kwa Atate wathu wakumwamba wachikondi, iye amamva mfuu zathu zopempha chifundo. Ndipo kumapereka chitonthozo chotani nanga kuzindikira kuti Yehova samapeputsa mtima wosweka!
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu afunikira mtima wangwiro ndi mzimu woyera wa Mulungu?
◻ Kodi munthu wolapa angaphunzitse chiyani ochimwira lamulo la Yehova?
◻ Kodi Yehova amawona motani mtima wosweka ndi wopsinjika?
◻ Kodi ndimaphunziro otani amene amapezeka m’Salmo 51?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi mumapempherera mzimu woyera ndi kusamala kusauchititsa chisoni?
[Chithunzi patsamba 17]
Sonyezani chiyamikiro cha chisomo cha Yehova mwa kulengeza chowonadi chake