Tanthauzo la Mwambiwo
Kodi Nkuchondereranji Kupsompsona kwa Mdani?
MUNTHU wanzeru wouziridwa mwaumulungu anapanga ndemanga iyi: “Mabala opangitsidwa ndi bwenzi ngokhulupirika, koma kupsompsona kwa mdani kuyenera kuchondereredwa.” (Miyambo 27:6, NW) Kodi mawu ameneŵa ayenera kumvedwa motani?
Munthu amene amakukondani angapangitse mabala ophiphiritsira m’njira yokhulupirika. Iye angakupatseni uphungu ali ndi chikondi mumtima mwake ndikuyembekeza kukuchitirani zabwino. Simufunikira kuchonderera bwenzi lenileni kaamba ka thandizo kapena chidzudzulo ngati chikufunikira. Ndipo mumakhala wanzeru chotani nanga ngati mulandira mwachisomo uphungu, kusuliza komangirira, kapena chidzudzulo chofunikira!
Komabe, ngati mukufuna kuti munthu amene amakudani akuchitireni chabwino, muyenera kumchonderera. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chidani chake sichikamsintha mwachibadwa kukupsompsonani. M’malo mwake, iye akakhala wokhoterera kukuchitirani m’njira yankhalwe. Chabwino chirichonse chimene mungachilandire kuchokera kwa iye chidzachitika kokha ndi mavuto akutiakuti ndi kuchonderera kwenikweni ku mbali yanu.
Chosangalatsa mogwirizana ndi ichi ndi limodzi la mafanizo amene Yesu Kristu anapereka. Iye panthaŵi ina analankhula za mkazi wamasiye amene anapeza chilungamo kwa woweruza wosaopa Mulungu ndiwosalemekeza munthu. Kodi mkaziyo anapambana motani? Woweruzayo anatsimikizira kuti mkaziyo anapeza mpumulo umene anaufunikira kokha chifukwa chakuti anapitiriza kumchonderera. Yesu anagwiritsira ntchito fanizo limeneli kugogomezera kwa ophunzira ake kuti “ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafoka mtima.”—Luka 18:1-8.
Kodi Olungama Amachuluka Motani Pamene Oipa Afa?
Miyambo 28:28 ikulongosola kuti: ‘Pouka oipa anthu amabisala; koma pakufa amenewo olungama achuluka.’ Kodi ichi chimatsimikiza kukhala chowona motani?
Oipa ‘angauke’ m’ulamuliro, mwinamwake monga olamulira ankhanza. Panthaŵi yoteroyo, munthu wolungama amabisala. Iye angachite tero chifukwa chowopa kutsendereza kwawo. Ndipo nkulekeranji kutero? Nzowona kuti ‘wina apweteka mnzake pomlamulira.’—Mlaliki 8:9.
Komabe, pamene oipa afa, anthu olungama ‘amachuluka.’ Motani? Mwachiwonekere chifukwa chakuti olungama amatuluka pobisalira pawo ndikuyamba kuwonekera poyera. Mwakutero amachuluka ndi kuwoneka ngati akuchuluka m’chiŵerengero chifukwa chakuti palibe chifukwa chodzibisira. Pamenepo ngati olungama angalamulire, iwo akalanga ochita zoipa ndikuchilikiza mkhalidwe wolungama. Chimenechonso chikakhala ndi chotulukapo chochepetsa chiŵerengero cha anthu osalungama ndi kuchulukitsa olungama.—Yerekezerani ndi Miyambo 28:12; 29:2.
Anthu amene ngolungama posachedwapa adzawona oipa akufa padziko lapansi “m’tsiku la mkwiyo wa Yehova” lomwe likuyandikira mofulumira. Chotero, funani chilungamo ndi chifatso mogwirizana ndi miyezo yaumulungu, ndipo mungasungidwe kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu, kumene olungama adzachulukadi.—Zefaniya 2:2, 3; 2 Petro 3:11-13.