Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 8/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Moyo wa Anthu Akale—M’busa
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Amaŵeta Nkhosa Mwachifundo
    Nsanja ya Olonda—1993
  • “Abusa Amene Mtima Wanga Wakonda”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Kuŵeta Nkhosa Zamtengo Wake za Yehova Mokoma Mtima
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 8/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi ndiuphungu waukulu wotani umene Miyambo 27:23 ikupereka kwa abusa auzimu limodzinso ndi kwa Akristu onse mwachisawawa?

Pavesilo timaŵerenga kuti: “Udziwitsitse zoweta zako ziri bwanji, Samalira magulu ako.” (Miyambo 27:23) Lembali kaŵirikaŵiri lagwiritsiridwa ntchito kulimbikitsa abusa auzimu kusonyeza chikondwerero ndi kukhala ozoloŵerana ndi mkhalidwe ndi mavuto a Akristu mumpingo. Chilimbikitso choterocho nchoyenerera, popeza kuti Baibulo limafananitsa akulu kwa abusa ndipo mpingo kwa gulu la nkhosa. (Machitidwe 20:28, 29; 1 Petro 5:2-4) Komabe, ngakhale kuti lamulo lamakhalidwe abwino lapamwambali limagwira ntchito, vesili kwakukulukulu silikunena za abusa auzimu.

Bukhu la Miyambo liri ndi mavesi ambiri amene amaima paokha monga ndemanga zapadera za uphungu, koma Miyambo 27:23 ndimbali ya gulu la mavesi akuti: ‘Udziwitsitse zoweta zako ziri bwanji, Samalira magulu ako. Pakuti chuma sichiri chosatha; Kodi korona alipobe mpaka mibadwo mibadwo? Amatuta maudzu, msipu uoneka, Achera masamba a kumapiri. Ana a nkhosa akuveka, Atonde aombera munda; Mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; Ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.’​—Miyambo 27:23-27.

Ndime youziridwa imeneyi imathokoza kukhala ndi njira ya moyo yozindikiridwa ndi khama, kukangalika, kudekha, ndi kuzindikira kudalira kwathu pa Yehova. Imatero mwakuunikira njira ya mbusa Wachiisrayeli, mwinamwake mosiyana ndi moyo wokhupuka wozikidwa pa machitachita a bizinesi ndi chuma chopezedwa mofulumira.

‘Chuma,’ kapena katundu wopezedwa m’mabizinesi ofulumira, ndi kukhupuka kotulukapo (“korona”), zikhoza kuzimiririka mosavuta, monga momwe ambiri angachitire umboni za chimenechi. Chotero moyo wokhweka umaloŵetsamo zambiri, wonga uja wokhala ndi abusa amakedzana m’kusamalira zoweta. Njira ya moyo imeneyo sinali yokhweka m’lingaliro lakukhala wosasamala. Mbusa anafunikira kukhala watcheru ku nkhosa zake, akutsimikizira kuti nkhosazo zinali zotetezeredwa. (Salmo 23:4) Ngati, pozisamalira, anawonapo nkhosa yodwala kapena yovulala, anaidzoza mafuta otonthoza. (Salmo 23:5; Ezekieli 34:4; Zekariya 11:16) M’zochitika zambiri mbusa wakhama yemwe anaika mtima wake pa zoweta zake anaona zoyesayesa zake zikubala zipatso​—kukula kwapang’onopang’ono kwa gulu lake la nkhosa.

Mbusa wogwira ntchito zolimba ndi wosamala adali ndi magwero odalirika a chithandizo​—Yehova. Motani? Eya, Mulungu amagaŵira nyengo ndi kuzungulira kwawo zimene mwamasiku onse zimatulukapo nsipu wokwanira kudyetsa nkhosa. (Salmo 145:16) Pamene nsipu uwuma ku malo akuchidikha chifukwa cha kusintha kwa nyengo, ungakhale wochuluka ku malo akumtunda, kumene mbusa watcheru angapititseko nyama zake.

Miyambo 27:26, 27 imatchula chotulukapo chimodzi cha ntchito yoteroyo​—zakudya ndi zovala. Mosakaikira, malongosoledwewo samanena chakudya chokoma chopambanitsa kapena mitundumitundu ya zakudya ndi zakumwa zapadera, ndiponso simapatsa wogwira ntchitoyo chifukwa chakuyembekezera zovala za mafashoni atsopano koposa kapena zovala za nsalu zokongola koposa. Koma ngati anali wofunitsitsa kupanga kuyesayesa, mbusayo ndi banja lake akakhoza kupeza mkaka ku nkhosazo (ndiponso cheese), limodzinso ndi ubweya wosokera zovala zochindikala.

Choncho uphungu wakuti: “Udziwitsitse zoweta zako ziri bwanji” kwakukulukulu suli wa oyang’anira auzimu; uli wa Akristu onse. Umagogomezera phindu la kukhala kwathu okhutiritsidwa ndi chakudya ndi chofunda zopezedwa m’ntchito yakhama, yapang’onopang’ono, tikukhulupirira kuti Mulungu sadzatisiya. (Salmo 37:25; 2 Atesalonika 3:8, 12; Ahebri 13:5) Tikayerekezera Miyambo 27:23-27 ndi uphungu wa pa Luka 12:15-21 ndi 1 Timoteo 6:6-11, timawona mmene uphungu wa Mulungu uliri woyenerera pankhaniyi. Chotero aliyense wa ife angaŵerengenso Miyambo 27:23-27, ndi kudzifunsa tokha kuti, ‘Kodi ndimayamikira zimenezi ndi kuzigwiritsira ntchito m’moyo wanga wa tsiku ndi tsiku?’

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena