“Alimo Wokwanira Madola Mamiliyoni Ambiri Mmenemo”
MAMILIYONI m’chiyani? M’phiri la Crown la ku Georgia, kumene golidi adapezedwa kale. Malinga ndi mphekesera inayake, mfuu yakuti “Alimo wokwanira madola mamiliyoni ambiri mmenemo” inaperekedwa ndi Dr. Stephenson, wopima mtengo wake wa Miyala ku United States, ali pakhonde pa nyumba yamilandu ku Dahlonega ku Georgia, U.S.A., kalelo mu 1849. Kodi nchifukwa ninji ananena zimenezo? Pamene mpikisano wa golidi wa mu 1849 wa ku California unayamba, okumba golidi a ku Dahlonega ndi Auraria yapafupiyo anayamba kuchoka kupita kumadzulo kukafuna golidi wochuluka. Koma dokotalayo anakhulupirira kuti golidi analimobe m’madera a kumpoto kwa Georgia. Ndiiko komwe, monga momwe chikwangwani cha mbiri yakale chikunenera, “pakati pa 1829 ndi 1839 pafupifupi golidi wokwanira $20,000,000 anakumbidwa m’mudzi wa Cherokee ku Georgia.” Koma Kumadzulo kunali kokopa zedi; zomwe ziliko lerolino ku Auraria wakale ndi zotsala zomwazikana za tauni ya mgodi yakale.
Tsoka lofananalo linagwera mgodi wa golidi wa Empire ku Grass Valley, California. Migula ya utali wa makilomita 591 itakumbidwa, yozama m’nthaka kwa makilomita 1.6, mgodiwo unatsekedwa mu 1957. Sunalinso kubweretsa phindu. Lerolino mgodiwo wasanduka paki yaboma ya m’mbiri.
Golidi wakhala akukopa anthu kwa zaka zikwi zambiri. Komabe, phindu lake nlachiphamaso ndi losakhalitsa, limasintha ndi malonda obetcha ndi nsika wagolidi wapadziko lonse. Komabe, pali “golidi” amene phindu lake silimatha ndipo amapezedwa ndi onse omfunitsitsa. Kodi nchiyani? ‘Wodala ndi wopeza nzeru, ndi wowona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka.’ (Miyambo 3:13, 14) Inde, nzeru ndi luntha, zozikidwa pa chidziŵitso cha Mulungu wowona ndi chifuno chake kaamba ka dziko lapansi, nzaphindu lokhalitsa kuposa golidi. Ngati mungakonde kudziŵa zambiri ponena za Mulungu wa Baibulo ndi dziko latsopano limene akulonjeza anthu omvera, chonde fikirani Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakufupi ndi kwanu kapena lemberani ofalitsa magazini ano.—Onani makeyala patsamba 5.
[Chithunzi patsamba 32]
Hotela yosiidwa m’tauni yakale ya mgodi wa golidi ya Auraria