Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Ntchito Yanu Idzapulumuka Moto?
    Nsanja ya Olonda—1998 | November 1
    • 4. (a) Kodi Paulo anali ndi udindo wotani pantchito yomanga yachikristu? (b) Nchifukwa chiyani tinganene kuti Yesu ndi omvetsera ake ankadziŵa za kufunika kwa maziko abwino?

      4 Kuti nyumba ikhale yolimba ndi yokhalitsa, imafunikira maziko abwino. Nchifukwa chake Paulo analemba kuti: “Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwinimamangidwe waluso, ndinaika maziko.” (1 Akorinto 3:10) Pogwiritsa ntchito fanizo lofanana, Yesu Kristu anasimba za nyumba imene inapulumuka mphepo yamkuntho chifukwa woimanga anasankha maziko olimba. (Luka 6:47-49) Yesu ankadziŵa bwino za kufunika kwa maziko. Analipo pamene Yehova anakhazika dziko lapansi pa maziko ake.a (Miyambo 8:29-31) Anthu amene anali kumvera Yesu akulankhula ankadziŵanso kufunika kwa maziko abwino. Nyumba zokha zomwe zikanapulumuka zigumula ndi zivomezi zomwe nthaŵi zina zinkachitika ku Palestina ndi zija zomwe anazimanga pa maziko olimba. Nanga kodi Paulo anali kunena za maziko ati?

  • Kodi Ntchito Yanu Idzapulumuka Moto?
    Nsanja ya Olonda—1998 | November 1
    • a “Maziko a dziko” angatanthauze mphamvu zachilengedwe zimene zimaligwira​—ndi zakumwamba zonse​—kuti likhazikike zolimba. Ndiponso, dziko lapansi linamangidwa mwanjira yakuti “silidzagwedezeka” konse, kapena kuwonongeka.​—Salmo 104:5.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena