Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 12/15 tsamba 8-10
  • ‘Anagula Choonadi’!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Anagula Choonadi’!
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Anakopeka ndi Ziphunzitso za Baibulo
  • Kudzipezera Choonadi
  • Kugwiritsidwa Mwala ndi Chipembedzo Chonyenga
Nsanja ya Olonda—1997
w97 12/15 tsamba 8-10

‘Anagula Choonadi’!

“GULA choonadi chenichenicho ndipo usachigulitse.” (Miyambo 23:23, NW) Analangiza motero mwamuna wanzeru Solomo. Ngakhale kuti mwachisawawa zimenezi zingatanthauze choonadi chilichonse, zimatanthauza makamaka choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Choonadi chimenecho chingatsogolere ku moyo wosatha! (Yohane 17:3, 17) Komabe, zindikirani kuti kupeza choonadi chimenecho sikwapafupi. Munthu amafunikira kukhala wofunitsitsa ‘kuchigula,’ ndiko kuti, kudzimana kapena kusiya chinachake kuti apeze choonadicho. (Yerekezerani ndi Mateyu 13:45, 46.) Kwenikweni, anthu ambiri sali ofunitsitsa kutero. Koma m’maiko ambiri, chiŵerengero chomakulirakulirabe cha anthu olimba mtima akugula choonadi cha Baibulo​—nthaŵi zambiri movutikira.

Mwachitsanzo, tiyeni tilingalirepo za Mboni za Yehova za m’dziko la Ghana ku West Africa. Pomafika m’June 1989, panali anthu oposa 34,000 a m’dzikolo amene analandira choonadi cha Baibulo ndipo anali kugaŵana ndi ena mokangalika. Kenaka ntchito yolalikira inaletsedwa. Komabe, anthu oona mtima anapitirizabe ‘kugula choonadi’​—mosasamala kanthu za chiletso cha bomacho. Chiletsocho chinachotsedwa pa October 31, 1991, ndipo chapakatikati pa 1995, patangopita zaka zitatu zokha ndi theka chichotsere cha chiletsocho, chiŵerengero cha Mboni za Yehova zokangalika ku Ghana chinafika 46,104! Ndipo chaka chino chiŵerengerocho chapitirira 52,800.

Kodi nchiyani chimene chakokera anthu ku choonadi cha Mawu a Mulungu? Kodi ndi kudzimana kotani kumene ena achita kuti ‘agule choonadi’? Poyankha, tiyeni tilingalirepo za zokumana nazo za Akristu atatu a ku Ghana.

Anakopeka ndi Ziphunzitso za Baibulo

Choyamba tiyeni tilingalirepo za mkazi wina wa m’zaka zake zoyambirira za m’ma 20. Atate ake anali apasitala, komabe iye anaganiza zosiya chipembedzo cha atate ake. Chifukwa chake? Kukonda kwake choonadi.

Iye nthaŵi ina anafotokoza kuti: “Mboni zinkakonda kubwera kunyumba kwathu pamaulendo awo a kunyumba ndi nyumba. Nditakambitsirana kangapo ndi iwo, ndinazindikira kuti zimene iwo anali kuphunzitsa zinali zochokeradi m’Baibulo. Ndinafunsa mafunso onena za Utatu, moto wa helo, kusafa kwa sou, ndipo makamakanso kuchiritsa mwachikhulupiriro. Ndinali kukhulupirira kwambiri kuti zikhulupiriro zimenezi zinali zochokera m’Baibulo. Koma Mboni zinandithandiza kuzindikira kuti sizinali choncho.”​—Ngati mufuna kudziŵa zimene Baibulo limanena pankhani zimenezi, chonde onani Marko 13:32; Aroma 6:23; Machitidwe 10:40; ndi 1 Akorinto 13:8-10.

Mtsikanayu anawonjezera kuti: “Komatu apabanja anga, makamaka atate anga sanagwirizane nazo mpang’ono pomwe. Iwo anaganiza kuti ndinali kusokeretsedwa. Komabe, ndinadziŵa kuti zimene ndinali kuphunzira kwa Mboni za Yehova zinali zoonadi. Ndinayesetsa kuuzako atate anga zinthu zimenezi za m’Baibulo, koma sanandimvere. Ndithudi chitsutsocho chinakuliratu.

“Komabe ine sindinabwerere mmbuyo. Ndinazindikira kuti choonadi chenicheni chokha ndicho chimatsogolera ku moyo wosatha m’Paradaiso, ndipo ndinatsimikiza mtima kuchigwiritsitsabe. Pamene Mboni za kuno zinamva za mavuto amene ndinali kukumana nawo, iwo anandithandiza mwachikondi, kundilimbikitsa ndi kundipatsa zosoŵa zina. Zimenezi zinandipangitsa kuzindikira mawu a Yesu opezeka pa Yohane 13:35 akuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” Chikhulupiriro changa chakuti Mboni za Yehova zimatsatira chipembedzo choona chinakula. Pambuyo pake, pamene makolo anga anaona kuti ndinayamba kusonyeza makhalidwe abwino, anasangalala kwambiri ndi zimenezo, ndipo anasiya kunditsutsa​—kotero kuti atate anga anapempha Mboni kuti ziziphunzira Baibulo ndi mlongo wanga wamkulu!”

Kudzipezera Choonadi

‘Kugula choonadi’ kumakhalanso kovuta kwa achinyamata ena amene aleredwa ndi makolo a Mboni. Achinyamata ena amatenga choonadi cha Baibulo mopepuka. Ngati alephera kudzipezera choonadi chimenecho, chikhulupiriro chawo chimafooka, ndiponso chimakhala chochepa. (Yerekezerani ndi Mateyu 13:20, 21.) Nathaniel, mwamuna wa ku Ghana wa m’zaka zake za m’ma 30, anafotokoza za mmene ‘anagulira choonadi’ akali wamng’ono.

“Makolo anga anandiphunzitsa Baibulo kuyambira paukhanda wanga,” iye anakumbukira motero. “Pamene ndinali kukula, ndinali kutsagana nawo pantchito yolalikira, koma ndinali ndisanalingalirebe zokhala Mboni. M’kupita kwa nthaŵi, ndinazindikira kuti ndinayenera kuphunzira pandekha.

“Choyamba, ndinafunikira kukhulupirira kuti Baibulo ndilodi Mawu a Mulungu, osati buku lina lililonse lopatulika lachipembedzo. Mwa kuchita phunziro laumwini, ndinazindikira kuti ndi buku lokhali lopatulika limene lili ndi maulosi ambiri odziŵika bwino amene anakwaniritsidwa ndendende. Ndinaphunziranso kuti m’Baibulo mumapezekanso zimene asayansi amaphunzitsa​—mwachitsanzo, zakuti dziko lapansi ‘linalenjekeka pachabe.’ (Yobu 26:7) Mawu ameneŵa analembedwa zaka zikwi zambiri asayansi asanazindikire za solar system yathu. Ndi Mulungu yekha amene anauzira amuna kuti alembe zinthu zimenezo!a

“Kenaka, ndinafuna kupeza gulu lachipembedzo limene limaphunzitsa ndi kutsatira choonadi chopezeka m’Baibulo. Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa za moto wa helo, Utatu, ndiponso za sou yosafa imene imapulumuka pa imfa. Koma ziphunzitso zimenezi zinali zopanda pake kwa ine. Ndinadzifunsa kuti: Kodi si tate woipa amene angagwiririre dzanja la mwana wake m’mbiya ya madzi otentha pomlanga? Nanga Mulungu wachikondi angaike bwanji ana ake m’moto wa helo kuti iwo azunzike? Komabe, Mboni za Yehova zimaphunzitsa mogwirizana ndi malemba a m’Baibulo monga Aroma 6:23, limene limati: ‘Mphotho yake ya uchimo ndi imfa’​—osati moto wa helo ayi. Zimenezi zinandigwira mtima.

“Ndinazindikiranso kuti Mboni za Yehova zimafuna kuti otsatira ake onse azikhala mogwirizana ndi malamulo a m’Baibulo ndiponso kuti iwo amachotsa mumpingo onse amene amachita machimo mosafuna kulapa. Nditazindikira zonsezi, ndinadziŵa kuti Mboni za Yehova ndizo zili ndi choonadi, ndipo ndinaganiza zokhala mmodzi wa iwo. Ndinayesetsa zolimba kuti ndikhale Mboni yobatizidwa.”​—1 Akorinto 5:11-13.

Chokumana nacho cha Nathaniel chikusonyeza bwino kuti ngakhale achinyamata amene aleredwa ndi makolo achikristu ayenerabe ‘kugula choonadi.’ Iwo sayenera kumangopezeka pamisonkhano mwamwambo chabe. Monga Abereya akale, iwo ayenera ‘kusanthula m’Malembo masiku onse, ngati zinthu zili zotero.’ (Machitidwe 17:11) Zimenezi zimatenga nthaŵi yaitali ndiponso pamafunika kuyesetsa, koma zingalimbitse chikhulupiriro chawo ndiponso angakhale otsimikiza mtima kwambiri.​—Yerekezerani ndi Aefeso 3:17-19.

Kugwiritsidwa Mwala ndi Chipembedzo Chonyenga

Mwamuna wina wa ku Ghana wotchedwa Godwin anali ndi zaka pafupifupi 70 pamene anasiya Tchalitchi cha Presbyterian ndi Gulu la Amasoni linalake. “Panali zinthu zina zimene zinali kuchitika m’tchalitchimo zimene ndinaona kuti zinali zokayikitsa,” anatero Godwin. “Mwachitsanzo, anali kumangokangana, ndipo mpaka pano akukanganabe. Nthaŵi zina kunkachita kubwera apolisi kuti adzakhazikitse mtendere ndi bata! Ndinaganiza kuti zimenezo sizinali zoyenera kwa otsatira Kristu. Kenaka panabuka vuto lina pakati pa ineyo ndi wa Presbyterian mnzanga. Nkhaniyo inapita kukhoti ndipo anaweruza kuti mnzangayo ndiye anali wolakwa. Komabe, mtumiki wa mpingowo anathandizira munthu ameneyu mokondera ndipo anafuna kundidzudzula pakati pa mpingo wonse! Ndinamfotokozera malingaliro anga ndipo ndinatuluka m’tchalitchimo​—osabwereranso.

“Patapita kanthaŵi, Mboni za Yehova zinafika panyumba panga. Poyamba, ndinamvetsera chabe chifukwa chakuti sindinafune kukana anthu amene anali kunena za Mulungu. Koma ndinayamba kuzindikira kuti ngakhale kuti ndinakhala wa Presbyterian kwa zaka makumi ambiri, panali zinthu zambiri zokhudzana ndi Baibulo zimene sindinazidziŵe. Mwachitsanzo, sindinali kudziŵa kuti Baibulo limanena za chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi.b Ndipo pamene ndinayamba kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova, makhalidwe, ndiponso kavalidwe ndi udongo wa achinyamata pakati pawo, zinandisangalatsa kwambiri. Awa ndi anthu amene amatsatiradi mapulinsipulo a Baibulo!”

Komabe, kuti ‘agule choonadi’ iye anafunikira kulimbikira kuti asinthe moyo wake. Godwin anakumbukira kuti: “Ndinali membala wa Gulu la Amasoni. Ndipo ngakhale kuti limadziŵika monga gulu logwirizana limene limathandiza mamembala ake, ndinaona kuti pamiyambo ina anali kugwiritsira ntchito zibade ndi mafupa ndiponso kufunsira mizimu. Iwo anali kunena kuti mizimu imeneyi imathandiza amene amalankhulana nayo kuti akule mwauzimu.

“Maphunziro anga anandithandiza kuzindikira kuti Yehova Mulungu amadana ndi kuchita zamizimu kulikonse chifukwa chakuti kungapangitse kuti munthu azilamuliridwa ndi Satana ndi mizimu yake yoipa.c Kodi ndikanapitirizabe kukhala membala wa Gulu la Amasoni nditazindikira kuti panali zinsinsi zotere, kapena kodi ndinayenera kuzisiya ndi kusangalatsa Yehova? Ndinasankha chachiŵirichi. Ndinasakaza ziŵiya zonse za Freemason zimene ndinali nazo, ngakhale chovala chimene ndinkavala pamisonkhano ya Gululo. Ndinazindikira kuona kwa lonjezo la Yesu pamene anati, ‘Choonadi chidzakumasulani’! (Yohane 8:32) Tsopano ndikugaŵana ndi ena mosangalala zinthu zimene ndinaphunzira. Ndipo palibe chimene ndikudandaula nacho.”

Anthu oona mtima zikwi zambiri adzimana mofananamo pofuna ‘kugula choonadi.’ Monga Akristu atatu amene afotokozedwa m’nkhani ino, iwo sakudandaula chifukwa cha kusintha kwawo. Choonadi cha Baibulo chawapatsa “maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.” (1 Timoteo 6:19) ‘Moyo weniweni’ umenewo ndi madalitso ake onse zingakhalenso zanu kosatha ngati ‘mugula choonadi.’

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mukufuna kudziŵa zowonjezereka, onani buku lakuti Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Mwachitsanzo, onani Salmo 37:9-11, 29.

c Onani Deuteronomo 18:10-12 ndi Agalatiya 5:19-21.

[Chithunzi patsamba 9]

Nathaniel

[Chithunzi patsamba 9]

Godwin

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena