Kupulumuka “Tsiku la Yehova”
“Tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?”—YOWELI 2:11.
1. Kodi nchifukwa ninji ‘tsiku la Yehova loopsa’ liyenera kukhala nthaŵi yachikondwerero?
“LOOPSA”! Ndimo mmene mneneri wa Mulungu Yoweli akufotokozera “tsiku la Yehova” lalikululo. Komabe, ife amene timakonda Yehova ndipo tadza kwa iye modzipatulira pamaziko a nsembe ya dipo ya Yesu sitiyenera kuzizira m’nkhongono ndi mantha pamene tsiku la Yehova liyandikira. Lidzakhaladi tsiku loopsa, komanso lidzakhala tsiku la chipulumutso chachikulu, tsiku lomasulidwa ku dongosolo loipa la zinthu limene lavutitsa anthu zaka zikwi zambiri. Poyembekezera tsikulo, Yoweli akuuza anthu a Mulungu kuti ‘akondwere, ndi kusekerera; pakuti Yehova adzachita zazikulu,’ ndipo akuwonjezera mawu otsimikiza akuti: “Kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.” Ndiyeno m’dongosolo la Ufumu wa Mulungu, “mudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.”—Yoweli 2:11, 21, 22, 32.
2. Pamene zifuno za Mulungu zikukwaniritsidwa, kodi chikuchitika nchiyani (a) mu “tsiku la Ambuye” (b) pa “tsiku la Yehova”?
2 Tisasokoneze tsiku loopsa la Yehova ndi “tsiku la Ambuye” la pa Chivumbulutso 1:10. “Tsiku la Ambuye” limaphatikizapo kukwaniritsidwa kwa masomphenya 16 ofotokozedwa m’Chivumbulutso machaputala 1 mpaka 22. Limaphatikizapo nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa zochitika zonse zimene Yesu analosera poyankha funso la ophunzira ake lakuti: “Zija zidzaoneka liti? ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” Kukhalapo kwa Yesu kumwamba kwaonekera padziko lapansi mwa zinthu zoopsa monga ‘nkhondo, njala, chidani, miliri, ndi kusayeruzika.’ Pamene zinthu zochititsa chisoni zimenezi zawonjezeka, Yesu wapereka chitonthozo kwa anthu oopa Mulungu mwa kutumiza ophunzira ake amakono kukalalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu . . . padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” Kenako, “chimaliziro” cha dongosolo la zinthu lilipoli, chimene chili tsiku loopsa la Yehova, chidzaulika monga chimake cha tsiku la Ambuye. (Mateyu 24:3-14; Luka 21:11) Limenelo lidzakhala tsiku la Yehova lopereka chiweruzo chamwadzidzidzi padziko loipa la Satana. “Thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu ake.”—Yoweli 3:16.
Yehova Achitapo Kanthu m’Masiku a Nowa
3. Kodi mikhalidwe lerolino ikufanana motani ndi ija ya m’tsiku la Nowa?
3 Zochitika m’dziko lerolino zikufanana ndi zija za mu “masiku a Nowa” zaka zoposa 4,000 zapitazo. (Luka 17:26, 27) Pa Genesis 6:5, timaŵerenga kuti: “Anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” Zangofanana ndendende ndi dziko lamakonoli! Kuipa, umbombo, ndi kupanda chikondi zili paliponse. Nthaŵi zina tingaganize kuti kuipa kwa mtundu wa anthu kwafika pachimake. Koma ulosi wa mtumwi Paulo wonena za “masiku otsiriza” ukukwaniritsidwabe: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.”—2 Timoteo 3:1, 13.
4. Kodi kulambira konyenga kunali ndi chisonkhezero chotani nthaŵi zakale?
4 Kodi chipembedzo chikanadzetsa mpumulo kwa mtundu wa anthu m’nthaŵi ya Nowa? Mosiyana ndi zimenezo, chipembedzo champatuko chimene chinaliko nthaŵiyo chiyenera kuti chinasonkhezera kwambiri mkhalidwe woipawo. Makolo athu oyamba anakopeka ndi chiphunzitso chonyenga cha “njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.” Mumbadwo wachiŵiri kuchoka pa Adamu, “anthu anayamba kutchula dzina la Yehova,” mwachionekere mwamwano. (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:3-6; 4:26) Kenako, angelo opanduka, amene anasiya kulambira kosagaŵanika kwa Mulungu, anavala matupi a anthu kuti achite chisembwere ndi ana aakazi okongola a anthu. Akazi ameneŵa anabereka zimphona zamphamvu, zotchedwa kuti Anefili [NW], zimene zinapondereza ndi kuzunza mtundu wa anthu. Mosonkhezeredwa ndi ziŵanda, “anthu onse anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi.”—Genesis 6:1-12.
5. Kodi Yesu akutipatsa chenjezo lotani mwa kutchula zochitika za m’tsiku la Nowa?
5 Komabe, banja limodzi linakhalabe lokhulupirika kwa Yehova. Chotero, Mulungu “anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.” (2 Petro 2:5) Chigumula chimenecho chinachitira chithunzi tsiku loopsa la Yehova, limene lidzakhala mapeto a dongosolo lino la zinthu ndiponso limene Yesu analosera kuti: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha. Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu. Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalaŵa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:36-39) Lerolino tili mumkhalidwe wofananawo, choncho Yesu akutilimbikitsa kuti ‘tidziyang’anire tokha ndi kudikira nyengo zonse ndi kupemphera, kuti tikalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika.’—Luka 21:34-36.
Chilango cha Yehova Choweruza Sodomu ndi Gomora
6, 7. (a) Kodi zochitika za m’nthaŵi ya Loti zinachitira chithunzi chiyani? (b) Kodi zimenezi zikutipatsa chenjezo liti lomveka?
6 Zaka mazana angapo Chigumula chitapita, mbadwa za Nowa zitachuluka padziko lapansi, Abrahamu wokhulupirikayo ndi Loti mphwake anaona tsiku linanso loopsa la Yehova. Loti ndi banja lake anali kukhala mumzinda wa Sodomu. Mzinda umenewu limodzi ndi mzinda woyandikana nawo wa Gomora, unadzaza ndi chisembwere chonyansa. Anthu anali okondetsanso chuma, ndipo pomalizira pake ngakhale mkazi wa Loti anakhudzidwa. Yehova anauza Abrahamu kuti: ‘Kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo kuchimwa kwawo kuli kulemera ndithu.’ (Genesis 18:20) Abrahamu anachonderera Yehova kuti asawononge mizindayo chifukwa cha olungama amene analimo, koma Yehova ananena kuti sanapezemo anthu olungama ngakhale khumi okha. Angelo a Mulungu anathandiza Loti ndi ana ake aakazi aŵiri kuti athaŵire kumzinda wapafupi wa Zoari.
7 Kenako kunachitikanji? Poyerekezera “masiku [athu] otsiriza” ndi aja a Loti, Luka 17:28-30 akuti: “Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba; koma tsiku limene Loti anatuluka m’Sodoma udavumba moto ndi sulfure zochokera kumwamba, ndipo zinawawononga onsewo; momwemo kudzakhala tsiku lakuvumbuluka Mwana wa munthu.” Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora patsiku loopsalo la Yehova kumatipatsa chenjezo lomveka m’nthaŵi ino ya kukhalapo kwa Yesu. Mbadwo wamakono wa mtundu wa anthu nawonso ‘wadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo.’ (Yuda 7) Ndiponso, khalidwe lachisembwere la m’nthaŵi zathu zino lachititsa “miliri” yambiri yoloseredwa ndi Yesu kuti idzakhalako m’nthaŵi yathu.—Luka 21:11.
Israyeli Akolola “Kavumvulu”
8. Kodi Israyeli analisunga motani pangano lake ndi Yehova?
8 M’kupita kwa nthaŵi, Yehova anasankha Israyeli kukhala ‘chuma chake chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; . . . ufumu wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.’ Koma zimenezi zinadalira kuti iwo ‘amvere mawu ake ndithu, ndi kusunga chipangano chake.’ (Eksodo 19:5, 6) Kodi analabadira mwaŵi waukulu kwambiri umenewu? Kutalitali! Zoonadi, anthu ena okhulupirika a mumtundu umenewo anamtumikira mokhulupirika—Mose, Samueli, Davide, Yehosafati, Hezekiya, Yosiya, limodzi ndi aneneri aamuna ndi aakazi odzipereka. Komabe, mtundu wonsewo sunakhulupirike. M’kupita kwa nthaŵi, ufumuwo unagaŵika paŵiri—Israyeli ndi Yuda. Ndithudi, mitundu yonse iŵiri inamwerekera ndi kulambira kwachikunja ndi miyambo ina yonyozetsa Mulungu ya maiko apafupi.—Ezekieli 23:49.
9. Kodi ndi motani mmene Yehova anaweruzira ufumu wopandukawo wa mafuko khumi?
9 Kodi Yehova anatani nayo nkhaniyo? Monga mwa nthaŵi zonse, iye anapereka chenjezo, mogwirizana ndi pulinsipulo lotchulidwa ndi Amosi lakuti: “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” Iyeyo Amosi analengeza tsoka kwa ufumu wakumpoto wa Israyeli kuti: “Mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? Ndilo mdima, si kuunika ayi.” (Amosi 3:7; 5:18) Ndiponso, mneneri mnzake wa Amosi, Hoseya, analengeza kuti: “Abzala mphepo, nadzakolola kavumvulu.” (Hoseya 8:7) Mu 740 B.C.E., Yehova anagwiritsira ntchito gulu lankhondo la Asuri powononga ufumu wakumpoto wa Israyeli kosatha.
Yehova Aŵerengera Mlandu Yuda Wampatuko
10, 11. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova sanafune kukhululukira Yuda? (b) Kodi ndi zinthu zonyansa ziti zimene zinaipitsa mtunduwo?
10 Yehova anatumizanso aneneri ake ku ufumu wakummwera wa Yuda. Komabe, mafumu a Yuda monga Manase ndi woloŵa m’malo mwake, Amoni, anapitirizabe kuchita zoipa pamaso Pake, kukhetsa ‘mwazi wambiri wosachimwa ndi kutumikira mafano ndi kuwagwadira.’ Ngakhale kuti mwana wa Amoni, Yosiya, anachita choyenera pamaso pa Yehova, mafumu amene anatsatira, limodzi ndi anthu onse, anamwerekeranso ndi zoipa, kotero kuti “Yehova sanafuna kukhululukira.”—2 Mafumu 21:16-21; 24:3, 4.
11 Kudzera mwa mneneri wake Yeremiya, Yehova anati: “Chodabwitsa ndi choopsa chaoneka m’dzikomo; aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwawo; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?” Mtundu wa Yuda unakhala ndi liwongo lalikulu la mwazi, ndipo anthu ake anali kuchita zoipa monga kuba, kupha, kuchita chigololo, kulumbira monama, kulambira milungu ina, ndi zinthu zina zonyansa. Kachisi wa Mulungu anakhala “phanga la okwatula.”—Yeremiya 2:34; 5:30, 31; 7:8-12.
12. Kodi ndi motani mmene Yehova analangira Yerusalemu wopandukayo?
12 Yehova analengeza kuti: “Ndidza ndi choipa chochokera kumpoto [kwa Akasidi] ndi kuwononga kwakukulu.” (Yeremiya 4:6) Choncho, anaitana Ulamuliro wa Dziko Lonse wa Babulo, panthaŵiyo “nyundo ya dziko lonse,” kudzawononga Yerusalemu wopandukayo ndi kachisi wake. (Yeremiya 50:23) Mu 607 B.C.E., mzindawo utavutika pozingidwa ndi asilikali, unawonongedwa ndi gulu lankhondo lamphamvu la Nebukadinezara. “Pamenepo mfumu ya ku Babulo inapha ana a [Mfumu] Zedekiya ku Ribila pamaso pake; mfumu ya ku Babulo niphanso aufulu onse a Yuda. Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, nammanga m’zigologolo, kumka naye ku Babulo. Ndipo Akasidi anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu. Ndipo Nebuzaradani kapitawo wa alonda anatenga anthu otsalira m’mudzi, ndi othaŵa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira namka nawo a m’nsinga ku Babulo.”—Yeremiya 39:6-9.
13. Kodi ndani anapulumuka patsiku la Yehova la mu 607 B.C.E., ndipo nchifukwa ninji?
13 Tsiku loopsadi! Komabe, anthu angapo amene anamvera Yehova anali pakati pa awo amene analanditsidwa pachiweruzo choopsacho. Ameneŵa anaphatikizapo Arekabu osakhala Aisrayeli, amene anasonyeza mzimu wa kudzichepetsa ndi kumvera mosiyana ndi eni Yudeya. Enanso amene anapulumuka anali Ebedi-meleki mdindo wokhulupirikayo, amene anapulumutsa Yeremiya kuti asafere m’dzenje lamatope, ndiponso mlembi wokhulupirika wa Yeremiya, Baruki. (Yeremiya 35:18, 19; 38:7-13; 39:15-18; 45:1-5) Yehova anali kulankhula kwa ameneŵa pamene anati: “Ndidziŵa malingiriro amene ndilingiririra inu, . . . malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.” Lonjezo limenelo linakwaniritsidwa pamlingo waung’ono mu 539 B.C.E. pamene Ayuda oopa Mulungu anamasulidwa ndi munthu amene anagonjetsa Babulo, Mfumu Koresi, nabwerera kukamanga mzinda wa Yerusalemu ndi kachisi wake. Lerolino awo amene amatuluka m’chipembedzo chachibabulo ndi kuyamba kulambira koyera kwa Yehova nawonso angayembekezere mtsogolo mwaulemerero ndiponso mwamtendere wosatha m’Paradaiso wobwezeretsedwa wa Yehova.—Yeremiya 29:11; Salmo 37:34; Chivumbulutso 18:2, 4.
“Chisautso Chachikulu” cha m’Zaka za Zana Loyamba
14. Kodi nchifukwa ninji Yehova anakana Israyeli kosatha?
14 Tifike m’zaka za zana loyamba C.E. Podzafika nthaŵiyo Ayuda amene anabwerera kwawo anakhalanso ampatuko. Yehova anatumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi kuti adzakhale Wodzozedwa wake, kapena kuti Mesiya. Pazakazo 29 mpaka 33 C.E., Yesu analalikira m’dziko lonse la Israyeli, nati: “Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:17) Ndiponso, anasonkhanitsa ophunzira ndi kuwaphunzitsa kulengeza naye uthenga wabwino wa Ufumu. Kodi olamulira a Ayuda anatani? Iwo anamnyoza Yesu ndipo pomalizira pake anachita upandu wonyansa wa kumupha momzunza pamtengo wozunzirapo. Yehova anawasiya Ayuda ndipo sanakhalenso anthu ake. Kukanidwa kumeneko tsopano kunali kwachikhalire.
15. Kodi Ayuda olapa anali ndi mwaŵi wakuchita chiyani?
15 Patsiku la Pentekoste 33 C.E., Yesu woukitsidwayo anatsanula mzimu woyera, ndipo zimenezi zinachititsa ophunzira ake kukhala ndi mphamvu yolankhula m’malirime kwa Ayuda ndi otembenukira kuchiyuda amene anasonkhana mwamsanga. Polankhula ndi khamulo, mtumwi Petro analengeza kuti: “Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse. . . . Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampachika.” Kodi Ayuda oona mtima anatani? “Analaswa mtima,” kulapa machimo awo, nabatizidwa. (Machitidwe 2:32-41) Kulalikira za Ufumu kunawonjezereka, ndipo pazaka 30 kunali kutafikira “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”—Akolose 1:23.
16. Kodi Yehova anaziyendetsa motani zinthu kuti apereke chiweruzo pa Israyeli wakuthupi?
16 Tsopano inali nthaŵi yoti Yehova apereke chiweruzo pa anthu ake amene anawakana, Aisrayeli akuthupi. Anthu zikwi zambiri, a m’mitundu ya m’dziko lonse panthaŵiyo, anali ataloŵa mumpingo wachikristu ndipo anali atadzozedwa monga “Israyeli [wauzimu] wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) Komabe, Chiyuda cha panthaŵiyo chinali chitawonongeka kukhala chachidani ndi chiwawa champatuko. Mosiyana ndi zimene Paulo analemba ponena za ‘kumvera maulamuliro aakulu,’ iwo mwachindunji anapandukira ulamuliro wachiroma umene unali kuwalamulira. (Aroma 13:1) Mwachionekere Yehova anayendetsa zochitika zimene zinatsatira. M’chaka cha 66 C.E., magulu ankhondo achiroma otsogozedwa ndi Kazembe Gallus anafika ndi kuzinga Yerusalemu. Aroma oukirawo analoŵa mumzindawo mpaka kukakumba khoma la kachisi. Malinga nkunena kwa mbiri yolembedwa ndi Josephus, mzindawo ndi anthu ake anasautsidwadi.a Koma mwadzidzidzi asilikali oukirawo anathaŵa. Zimenezi zinapereka mpata wakuti ophunzira a Yesu “athaŵire kumapiri,” monga momwe iye anawachenjezera mu ulosi wake wolembedwa pa Mateyu 24:15, 16.
17, 18. (a) Kodi Yehova anagwiritsira ntchito chisautso chotani kuti apereke chiweruzo pa Chiyuda? (b) Kodi ndi anthu ati amene ‘anapulumuka,’ ndipo kodi zimenezi zinachitira chithunzi chiyani?
17 Komabe, Yehova anali kudzaperekabe chiweruzo chonse pachimake cha chisautso mtsogolo. Mu 70 C.E., asilikali achiroma, tsopano otsogozedwa ndi Kazembe Titus anabweranso kudzaukira. Ulendo uno nkhondo inali kudzachitikadi! Ayuda, amenenso anali kuthirana nkhondo okhaokha, sanali kanthu powalinganiza ndi Aroma. Mzindawo ndi kachisi wake zinasakazidwa kotheratu. Ayuda owonda oposa miliyoni imodzi anavutika ndi kufa, mitembo ngati 600,000 inaponyedwa kunja kwa zipata za mzinda. Mzindawo utawonongedwa, Ayuda 97,000 anatengeredwa kuukapolo, ndipo ambiri anafera m’mabwalo a maseŵero ophana. Ndithudi, anthu okha amene anapulumuka m’zaka za chisautso chimenecho anali Akristu omvera amene anathaŵira kumapiri tsidya lina la Yordano.—Mateyu 24:21, 22; Luka 21:20-22.
18 Chotero, ulosi waukulu wa Yesu wonena za “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano” unakwaniritsidwa nthaŵi yoyamba, ndipo kukwaniritsidwako kunafika pachimake patsiku la Yehova lopereka chiweruzo pa mtundu wopanduka wachiyuda mu 66-70 C.E. (Mateyu 24:3-22) Komabe, chimenecho chinali chabe chithunzi cha ‘tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa likudzalo,’ chisautso chomaliza chimene chili pafupi kukuta dziko lonse lapansi. (Yoweli 2:31) Kodi ‘mungapulumuke’ motani? Nkhani yotsatira idzafotokoza.
[Mawu a M’munsi]
a Josephus akusimba kuti Aroma oukirawo anazinga mzindawo, kukumba mbali ina ya khomalo, ndipo anali pafupi kuyatsa moto chipata cha kukachisi wa Yehova. Ayuda otsekeredwa mkati anachita mantha kwambiri ndi zimenezi, popeza kuti anaona imfa ikuyandikira.—Wars of the Jews, Book II, mutu 19.
Mafunso Openda
◻ Kodi “tsiku la Ambuye” likugwirizana motani ndi “tsiku la Yehova”?
◻ Popenda tsiku la Nowa, kodi tiyenera kulabadira chenjezo lotani?
◻ Kodi Sodomu ndi Gomora akupereka motani phunziro lamphamvu?
◻ Kodi ndani anapulumuka “chisautso chachikulu” cha m’zaka za zana loyamba?
[Zithunzi patsamba 15]
Yehova anapereka chipulumutso ku banja la Nowa ndi la Loti, ngakhalenso mu 607 B.C.E. ndi 70 C.E.