Kodi Mungakondwere ndi Zochita Zambiri?
AMBIRI a ife timakhala ndi moyo wotanganitsidwa, kaŵirikaŵiri wopanikizika. Zitsenderezo zosalekeza za kakhalidwe kamakono zimafuna kuti tipange kuyesayesa kosalekeza kokha kuti tichite nazo. Amuna okwatira ndi atate ayenera kukwaniritsa mathayo opanikiza a mabanja awo, oŵalemba ntchito, ndi ena. Akazi okwatiwa ndi anakubala ayenera kusamalira zosoŵa za panyumba za mabanja awo ndipo kaŵirikaŵiri afunikira kugwira ntchito yakuthupi. Achichepere nawonso ali pansi pa chitsenderezo chochita ndi mathayo akutiakuti abanja pamene akupeza maphunziro amene adzaŵakonzekeretsa kaamba ka mbali yopindulitsa m’chitaganya.
Koma bwanji ponena za ife amene tapereka miyoyo yathu kwa Yehova Mulungu ndipo ndife Mboni zake zobatizidwa? Kuwonjezera pa zofunidwa zonse, tiri ndi chenjezo ili la mtumwi Paulo lakuti: ‘Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.’ (1 Akorinto 15:58) Inde, mathayo ambiri owonjezereka ali mbali ya ziyeneretso za kulambira kowona. Kodi tingakwaniritse motani mathayo onse ameneŵa ndikukhala ndi mtendere wa maganizo ndi malingaliro achimwemwe?
Kukwaniritsa Kumadzetsa Chimwemwe
Chimwemwe—lingaliro la kudzimva bwino kapena chikhutiro—nchogwirizana kwambiri ndi chipambano m’kusamalira mathayo a moyo. Ngati ndife okhoza kukwaniritsa mathayo athu atsiku ndi tsiku mokwanira, kuchita zinthu panthaŵi yake ndipo mwadongosolo, timakhala ndi lingaliro lakukwaniritsa ndi chikhutiro. Umo ndimmene ziyenera kukhalira, ndipo zotulukapo zake zimawonjezera chimwemwe chathu.
Yehova Mulungu sanafune konse kuti kusamalira mathayo kwathu kukhale goli lotsendereza. Mmalomwake, chakhala chikhumbo chake nthaŵi zonse kuti ‘tikondwe ndi kuwona zabwino m’ntchito zathu zonse.’ (Mlaliki 3:12, 13) Pamene tiri okondwera ndi ntchito yathu, timakhala obala zipatso nthaŵi zambiri. Timalandira malangizo mosavuta ndi kuchita mwamtendere ndi ena. Kumbali ina, ngati ndife osakondwera, ntchito yathu imakhoterera kukhala yothodwetsa—yogwetsa ulesi, yosungulumwitsa, ngakhale yovutitsa malingaliro. Izi zimatsogolera ku zizoloŵezi za ntchito yosabala zipatso ndi mkhalidwe wamaganizo wosayenera. Moyo umakhala kulimbana kwatsiku ndi tsiku pamene tiyesayesa kukwaniritsa zonse zofunidwa kwa ife. Komabe, ngati tingapeze njira yokhalira wokondwera ndi zimene timachita, tidzakhala othekera kwambiri kusangalala ndi njira ya moyo yopereka mphotho ndi yokhutiritsa.
Khalani Olinganizika
Ngati titi tikhale okondwera chinkana kuti tiri ndi zochita zambiri, tifunikira kukhala olinganizika. Ndipo kodi kulinganizika nchiyani? Ndiko “kukhazikika kwamaganizo ndi malingaliro.” Munthu wolinganizika amayesayesa kukhala wadongosolo m’zochita zake. Iye amapanga makonzedwe pasadakhale, amapeŵa kuchedwetsa zinthu, ndipo ngwachikatikati m’zizoloŵezi. Iye amasonyeza kudziletsa m’kadyedwe, zakumwa, zosangulutsa, zochita zapamtima, ndi zosangalatsa. Kwenikweni, iye amasonyeza “chiletso m’zinthu zonse”!—1 Akorinto 9:24-27, NW; yerekezerani ndi Tito 2:2.
Pemphero limachita mbali yaikulu m’kusunga kulinganizika Kwachikristu. Mtumiki wa Yehova angapempherere mzimu woyera wa Mulungu ndi chithandizo cha Atate wake wakumwamba m’kukulitsa zipatso zake, kuphatikizapo kudziletsa. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23) Mkristu makamaka ayenera kuyang’ana kwa Mulungu m’pemphero pamene avutitsidwa ndi ziyeso zimene zimawopseza kudodometsa kulinganizika kwake. Wamasalmo Davide anati: ‘Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso iye, adzachichita.’ (Salmo 37:5) Nthaŵi zina tingafunikire kupemphera monga momwe Davide anachitira pamene anachonderera kuti: ‘Mundifulumirire, Mulungu: inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga; musachedwe, Yehova.’ (Salmo 70:5) Osaiŵala konse kuti mwa pemphero nkotheka kusunga kulinganizika ndi kusangalala ndi ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, ndipo udzasunga mitima yathu ndi maganizo.’—Afilipi 4:6, 7.
Chifukwa chakuti iye amadalira pa Yehova ndipo amasangalala ndi mtendere wa Mulungu, Mkristu wolinganizika ngwolama maganizo. (Tito 2:11, 12) Izi zimadza mwakukhala ndi kumvetsetsa kwabwino kwa malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo ndi mwakuwagwiritsira ntchito m’moyo wake. Munthu wotero sali wachinyengo, kapena wansontho m’kupereka chiweruzo. Kulingalira kwabwino kumamupeŵetsa kukhala wodalira pamalingaliro ake kapena wouma khosi. Amasunga lingaliro lodzichepetsa la iyemwini ndi maluso ake, ndipo zimenezi zimamtheketsa kugwirizana ndi ena. (Mika 6:8) Chokondweretsa nchakuti, mikhalidwe imene imathandiza munthu kukhala wolinganizika irinso pakati pa mikhalidwe yofunidwa kwa awo oikidwa kutumikira monga oyang’anira mumpingo Wachikristu.—1 Timoteo 3:2, 3.
Tingawonjezere chimwemwe chathu mokulira mwakukalamira kukhala olinganizika mowonjezereka m’zochita zathu zatsiku ndi tsiku. Mwakusonyeza mikhalidwe yogwirizana ndi kulinganizika kwabwino, tingachite zinthu zofunikira popanda kuvutika kwakukulu kwakuthupi kapena kwamaganizo. Njira yathu yamoyo idzasonyeza kukhazikika kokulirapo, ndipo tidzakwaniritsa zambiri. Anthu ena adzapeza chisangalalo chowonjezereka m’mayanjano athu, ndipo tidzasangalala ndi chikhutiro chokulirapo, ndi chimwemwe. Koma kodi nziti zomwe ziri njira zina zothandiza kusunga kulinganizika?
Njira Zothandiza Kusunga Kulinganizika
Kuti tisunge kulinganizika, tiyenera kuyesayesa kukhala achangu ndi adongosolo posamalira zochita zathu. Tifunikira kukonzekera pasadakhale, kusamalira zinthu m’mkhalidwe wolingalira ndi wadongosolo. Awo osoŵa kulinganiza kwabwino ndipo ngokhoterera kuchedwetsa zinthu amacholoŵanitsa miyoyo yawo ndi kupanikizika kowonjezereka ndi nkhaŵa. Chipambano m’mbali iyi yamoyo chidzatithandiza kudzimva kuti tikulamulira mikhalidwe mmalo modzimva kukhala minkhole yake yosakhoza kudzithandiza.
Sitiyenera kuyesa kuchita tokha zinthu zonse. Awo osafuna kulandira chithandizo cha ena kaŵirikaŵiri amalipira mtengo waukulu wa kutopa ndi kukhumudwa. Pali ntchito zosiyanasiyana zimene zingasamalidwe ndi ena. Chotero, nkwanzeru kulandira mwaŵi wa awo okhoza omwe afunitsitsa kuthandiza. Kuwonjezera pa kupeputsa ntchito yathu, izi zingalimbikitse awo ofuna kuyandikana nafe mwathithithi.
Nkupanda nzeru kudziyerekezera ife eni ndi awo amene angakhoze kuchita zochuluka. Kuyesayesa kukhala monga awo amene mwachiwonekere amakwaniritsa zambiri kutiposa nkolefulitsa, kumatipangitsa kudzimva ochepa ndi osayenerera. Kulingalira koteroko nkowononga, kododometsa kutsimikiza mtima kwathu ndi chidaliro chaumwini. Paulo analemba kuti: ‘Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, sichifukwa cha wina.’ (Agalatiya 6:4) Kumbukirani kuti wantchito woŵerengeredwa koposa njemwe amatsatira malangizo, wokhazikika ndi wodalirika, ndipo amachita ntchito yabwino koposa. Ngati tiri otero, mautumiki athu adzayamikiridwa ndi kufunidwa.—Miyambo 22:29.
Tifunikira kulisamalira bwino thanzi lathu. Ilo liri chimodzi cha zinthu zamtengo wapatali zomwe tiri nazo, popeza kuti popanda ilo tingakhoze kuchita zochepa kwambiri. Chifukwa chake, tiyenera kuyesayesa kusunga kadyedwe kabwino mwakudya zakudya zopatsa thanzi. Tifunikira kupeza mpumulo umene timaufunikira, mwakupita kukagona panthaŵi yoyenerera usiku. Pamene tikhala otopa mopambanitsa kapena kumva kuti tidzadwala, sitiyenera kudzikakamiza; tingalipire mtengo waukulu.
Nkofunika kupeŵa kukulitsa mzimu wodandaula. Ngati tilekerera malingaliro oipidwa, tingapeze kanthu kena kolakwika pafupifupi kwa chirichonse kapena aliyense. Iyi ndi njira yotsimikizirika yolanda enife ndi ena chimwemwe. Mmalo mochita miseche kapena kudandaula ponena za chimene tikulingalira kukhala cholakwika, tiyenera kudziŵitsa awo okhala ndi thayo la kusamalira nkhaniyo ndi kuŵasiira kuti awongolere zinthu. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 1:10-12.) Tidzakhala anzeru kusunga lingaliro labwino, nthaŵi zonse kufunafuna ndi kuyembekezera kupeza zabwino mwa ena ndi m’zochitika zimene zimaumba moyo wathu.—Yerekezerani ndi Yuda 3, 4, 16.
Pokonzekera zochita zathu, tiyenera kukumbukira kuti liŵiro lalikulu lingapange dzina labwino, koma silingasungidwe konse kwanthaŵi yaitali. Kuyesayesa kopambanitsa kopitirizabe sikumangotopetsa koma kungagwiritsenso mwala zimene zingadodometse kutsimikiza mtima kwathu kwa kupitiriza. Chifukwa chake, tatiyeni tikhazikitse liŵiro limene tingalisunge kunthaŵi yosadziŵika. Mwachitsanzo, nkwabwino kukhazikitsa ndandanda yothandiza yakutengamo mbali mokhazikika m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba ndi mbali zina za uminisitala Wachikristu. Timafunikira kupeza nthaŵi yakupuma ndi kusanguluka komangirira. Ndipo tidzakupeza kukhala kopindulitsa kulankhula ndi anthu achikulire amene ali ndi zaka makumi ambiri zakuzoloŵera, popeza kuti iwo angakhale anaphunzira kuchita zinthu zofunikira popanda kudzitopetsa okha mwakuthupi ndi mwamaganizo.
Gwiritsirani Ntchito Kulingalira Kwabwino
Nkoyenera kukhala ndi lingaliro lathayo ndi chikhumbo chakukwaniritsa mathayo athu onse ogaŵiridwa, kuphatikizapo aja a mumpingo wa anthu a Yehova. Mulungu amakondwera ndi antchito akhama, ndi odalirika. (Yerekezerani ndi Mateyu 25:21; Tito 2:11-14.) Koma Malemba amalimbikitsa kuti: “Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira.” (Miyambo 3:21) Kugwiritsira ntchito nzeru ya Baibulo kudzatipindulitsa, ndipo tifunikira kugwiritsira ntchito nzeru yeniyeni ndi kulingalira kwabwino, kupanga makonzedwe mosamala ndipo nthaŵi zonse kusachita mopambana pa nyonga yathu.
Chilimbikitso cha kuchuluka m’ntchito ya Ambuye chiyenera kulingana ndi chenjezo loperekedwa pa Mlaliki 9:4. Pamenepo timaŵerenga kuti: ‘Pakuti galu wamoyo aposa mkango wakufa.’ Inde, galu wamoyo, chinkana kuti amanyozedwa ndi ena, ngwabwinopo kuposa mkango wakufa, nyama imene ambiri amaiyesa yowopsa. Ngati tichita molinganizika ndi kusamalira thanzi lathu moyenera, tidzakhala ndi moyo ndi kupitirizabe kuchita zinthu. Akufa alibe phande lirilonse m’ntchito iriyonse. Kulingalira kwabwino kungatithandize kupeza kulinganizika koyenera kumene kumatilola kukwaniritsa zinthu zofunika popanda kutaya chimwemwe chathu.
Chotero pamenepa, kukhala ndi zambiri zochita sikumatanthauza kuti sitingakhale okondwera. Anthu otanganitsidwa koposa angakhale pakati pa anthu achimwemwe koposa ngati ali olingalira, amasunga lingaliro labwino, ndi kugwiritsira ntchito kulingalira kwabwino kotero kuti akhalebe olinganizika bwino. Tingasangalale ndi chimwemwe chachikulu koposa chothekera ngati tisonyeza nzeru, kuchita ntchito zokoma, ndi kuika chiyembekezo chathu mwa Yehova Mulungu.—1 Timoteo 6:17-19.