Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 10/15 tsamba 3-4
  • Chimwemwe Chovuta Kwambiri Kuchipeza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chimwemwe Chovuta Kwambiri Kuchipeza
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mfungulo ya Kusoŵa Chimwemwe
  • Cholinga Chovuta Kukwaniritsa
  • Kufunafuna Moyo Wachimwemwe
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Chuma Chingakupatseni Chimwemwe?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Thanzi Ndi Chimwemwe—kodi Mungazipeze Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Chimwemwe Chenicheni Chingapezeke Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 10/15 tsamba 3-4

Chimwemwe Chovuta Kwambiri Kuchipeza

ASAYANSI kwa nthaŵi yaitali afufuza za mkwiyo, kuda nkhaŵa, ndi kuchita tondovi. Komabe, m’zaka zaposachedwapa asayansi opambana akhala akufufuza kwambiri za mkhalidwe wolimbikitsa ndi wokhumbika wa anthu​—chimwemwe.

Kodi chimene chingapangitse anthu kukhala achimwemwe kwambiri nchiyani? Kodi ndi kukhala achinyamata, olemera, aatali, kapena oonda? Kodi mfungulo ya chimwemwe chenicheni nchiyani? Anthu ambiri amavutika kwambiri kuyankha funsolo, ndipo mwina amalephereratu. Poganizira za kulephera kwa anthu ambirimbiri kuti apeze chimwemwe, mwinamwake ena angayankhe msanga za chimene sichili mfungulo ya chimwemwe.

Kwa nthaŵi yaitali, akatswiri opambana a zamaganizo ankanena kuti mfungulo ya chimwemwe ndiyo kukhala wongosamala zako zokha basi. Iwo analimbikitsa anthu osoŵa chimwemwe kuti azingoganiza zokhutiritsa zofunika zawo zokha basi. Mawu ochititsa chidwi onga “uzingosamala zako basi,” “zindikira zamumtima mwako,” ndi “dzidziŵe umunthu wako” awagwiritsira ntchito kwambiri m’machiritso a matenda amaganizo. Komabe, ena mwa akatswiri omwewo ochirikiza maganizowa tsopano amavomereza kuti mzimu wongosamala zako zokha umenewu sumadzetsa chimwemwe chokhalitsa. Kuganizira zako zokha basi kudzangodzetsa zoŵaŵa ndi kusoŵa chimwemwe. Kudzikonda sindiko mfungulo ya chimwemwe.

Mfungulo ya Kusoŵa Chimwemwe

Awo amene amafunafuna chimwemwe mwa kulondola zosangulutsa akusemphana nacho. Lingalirani za Mfumu Solomo yanzeruyo ya Israyeli wakale. M’buku la m’Baibulo la Mlaliki, iye akufotokoza kuti: “Chilichonse maso anga anachifuna sindinawamana; sindinakaniza mtima wanga chimwemwe chilichonse pakuti mtima wanga unakondwera ndi ntchito zanga zonse; gawo langa la m’ntchito zanga zonse ndi limeneli.” (Mlaliki 2:10) Solomo anadzimangira nyumba, kuoka mipesa, ndi kupanga minda ya maluŵa, mapaki ndi matamanda a madzi. (Mlaliki 2:4-6) Nthaŵi ina anafunsa kuti: “Ndani angadye ndi kufulumirako, koposa ine.” (Mlaliki 2:25) Anali ndi oimba abwino koposa omsangulutsa, ndipo anasangalala ndi ubwenzi wa akazi okongola koposa m’dzikolo.​—Mlaliki 2:8.

Mfundo ndiyo yakuti, Solomo sananyalanyaze zinthu zosangalatsa. Kodi anafika palingaliro lotani atakhala ndi zosangalatsa zambirimbiri m’moyo? Anati: “Ndinayang’ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.”​—Mlaliki 2:11.

Zomwe mfumu yanzeruyo inapeza zikali zolondola kwambiri mpaka lero. Mwachitsanzo tiyeni titenge dziko lolemera monga United States. Pazaka 30 zapitazi, Aamereka aŵirikiza unyinji wa katundu wawo wakuthupi, monga magalimoto ndi mawailesi akanema. Komabe, malinga ndi kunena kwa akatswiri a thanzi lamaganizo, Aamereka sanawonjezere chimwemwe chawo. Malinga ndi magazini ina, “m’nyengo imodzimodziyo, anthu ochita tondovi awonjezeka. Chiŵerengero cha achinyamata odzipha okha chawonjezeka katatu. Chiŵerengero cha zisudzulo chaŵirikiza.” Ofufuza apeza zofananazo posachedwapa atapenda mmene ndalama zimakhudzira chimwemwe pakati pa anthu a m’maiko pafupifupi 50 osiyanasiyana. Kunena mwachidule, simungagule chimwemwe.

Mosiyana ndi zimenezo, kufunafuna chuma kungatchedwe molondola kuti mfungulo ya kusoŵa chimwemwe. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”​—1 Timoteo 6:9, 10.

Chuma, thanzi labwino, unyamata, kukongola, mphamvu zaulamuliro, kapena kukhala nazo zingapo mwa zinthu zimenezi sikungadzetse chimwemwe chokhalitsa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tilibe mphamvu yoletsa zinthu zoipa kuti zisachitike. Mfumu Solomo ananena momveka kuti: “Munthu sadziŵatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa m’ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthaŵi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.”​—Mlaliki 9:12.

Cholinga Chovuta Kukwaniritsa

Palibe kufufuza kwa sayansi kwaukulu uliwonse kumene kungatulukire njira yopangidwa ndi anthu yopezera chimwemwe. Solomo ananenanso kuti: “Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m’liŵiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziŵitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m’nthaŵi mwake.”​—Mlaliki 9:11.

Ambiri amene amavomereza mawu apamwambawa afika palingaliro lakuti kuyembekeza kukhala ndi moyo wachimwemwe chenicheni nkulota. Mphunzitsi wina wotchuka ananena kuti “chimwemwe chili mkhalidwe wongoyerekezera m’maganizo.” Ena amakhulupirira kuti mfungulo ya chimwemwe nchinsinsi chosafotokozeka, kuti ndi okhoza kumvetsa zinsinsi zazikulu angapo okha anzerudi amene angavumbule chinsinsi chimenechi.

Komabe, pakufunafuna kwawo chimwemwe, anthu akuyesabe njira zosiyanasiyana za moyo. Mosasamala kanthu kuti ena analepherapo kale kumbuyoku, ambiri lerolino akufunafunabe chuma, mphamvu zaulamuliro, thanzi labwino, kapena zosangulutsa monga zothetsera kusoŵa kwawo chimwemwe. Anthu ochuluka akufunafunabe chimwemwe chifukwa chakuti mumtima, amadziŵa kuti chimwemwe chokhalitsa simkhalidwe wongoyerekezera m’maganizo. Amakhulupirira kuti chimwemwe siloto wamba lopanda tanthauzo. Ndiyeno mungafunse kuti, ‘Kodi ndingachipeze motani?’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena