Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ws mutu 16 tsamba 129-135
  • “Khamu Lalikulu” Tsopano Likuyenda pa “Khwalala” Lomka ku Gulu la Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Khamu Lalikulu” Tsopano Likuyenda pa “Khwalala” Lomka ku Gulu la Mulungu
  • Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kutulutsa Munda wa Edene Wophiphiritsira
  • “Khwalala” Lopatulika
  • Achimwemwe Tsopano ndi Kosatha
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Pitirizani Kuyenda pa “Msewu wa Chiyero”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Tili ndi Chifukwa Chofuulira ndi Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda—1996
  • “Mzimu wa Moyo Wochokera kwa Mulungu Unawalowera”
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
ws mutu 16 tsamba 129-135

Chaputala 16

“Khamu Lalikulu” Tsopano Likuyenda pa “Khwalala” Lomka ku Gulu la Mulungu

1, 2. Kodi ndiliti pamene Yesaya chaputala 35 amakhala ndi kukwaniritsidwa kwauzimu, ndipo ndimalongosoledwe otani amene mavesi aŵiri oyambirira amapereka?

MKATI mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa “Kalonga wa Mtendere,” mbali zambiri za Yesaya chaputala 35, zimene tsopano zikukwaniritsidwa chiwonongeko cha Babulo Wamkulu chisanachitike, zidzawoneka m’lingaliro lenileni kwa anthu. Chifukwa chakuti zimene zidzakhala zitakwaniritsidwa mwanjira yauzimu zidzakwaniritsidwadi mwanjira yakuthupi. Kukwaniritsidwa kwakukulu kwauzimu kwa ulosi umenewu kukuchitika tsopano lino mwa kubwezeretsedwa kwa atumiki a Mulungu kuchokera ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. Mneneri Yesaya anakulongosola mwa mawu aŵa okondweretsa:

2 “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti see lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa. Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebano, ndi ukulu wa Karimeli ndi Saroni; anthuwo adzawona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.”—Yesaya 35:1, 2.

3. Kalero m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., kodi dziko labwinja linali kuti, ndipo likanakondwera motani?

3 Kodi chipululu ndi malo opanda madzi ndi chipululu cha mchenga zinali kuti? M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., izo zinali m’gawo la ufumu wa Yuda. Podzafika 537 B.C.E., dziko limenelo linali bwinja ndi lopanda okhalamo kwa zaka 70. Koma kodi chipululu chikasangalala motani? Kukakhala kofunika kuti nzika zake zoyamba zibwereremonso. Linali kudzakwezedwa kuchokera kumkhalidwe wake wotsika ndi kupatsidwa ulemerero wa mapiri aatali a Lebano wokongolayo.

Kutulutsa Munda wa Edene Wophiphiritsira

4, 5. (a) Kodi ndiliti, m’nthaŵi zamakono, pamene masinthidwe ofananawo a dziko lonyanyalidwa motero anachitidwa, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi ntchito za kubwezeretsedwa kwa otsalira odzozedwa zinakhala n’chotulukapo chotani? (c) Kodi ndimotani mmene Yesaya 35:5-7 amalongosolera mkhalidwe wawo wauzimu wobwezeretsedwa?

4 Kufanana kwamakono, m’lingaliro lauzimu, ku kusandulika kumeneku kwa dziko kuchokera kumawonekedwe onyanyalidwa ndi Mulungu kufikira kumkhalidwe wosonyeza chiyanjo chobwezeretsedwa cha Yehova kunayamba kuchitika mu 1919. Anthu obwezeretsedwa a Yehova anali otsimikiza kupindula mokwanira ndi nyengo ya mtendere imene panthaŵiyo inaŵatsegukira. Koresi Wamkulu, Yesu Kristu, ndi Atate wake, Yehova Mulungu, anagaŵira otsalira Aisrayeli auzimu omasulidwawo kuchita ntchito yaulemerero imene inali yofanana ndi kumangidwa kwa kachisi wa Yehova ndi otsalira a Israyeli wakale obwerera kwawo pambuyo pa 537 B.C.E. Ntchito ya kuyambiranso pambuyo pa 1919 inachititsa kutulutsidwa kwa munda wa Edene wophiphiritsira.

5 Zimenezi zidanenedweratu m’mawu aŵa a Yesaya 35: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzaimba; pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti see. Ndipo mchenga wong’azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m’malo a ankhandwe mmene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.”—Yesaya 35:5-7.

6. Kodi nchiyani chimene kupitirizabe kukhalapo kwa Edomu wamakono wophiphiritsiridwa sikunalepheretse, ndipo kodi ndani lerolino amene amafuula mokondwera limodzi ndi otsalira obwezeretsedwa?

6 Kukhalako kwa Edomu wophiphiritsiridwa, wamakono sikunalepheretse kubwezeretsedwa kwa Israyeli wauzimu kumkhalidwe wa paradaiso m’kukwaniritsidwa kwa Yesaya chaputala 35. Motero Aedomu amakono alibe chifukwa cha kusangalalira monga momwe amachitira otsalira a Israyeli wauzimu, limodzi ndi “khamu lalikulu” lowonjezerekawonjezereka. “Khamu lalikulu” liri ndi mbali yaikulu m’kusungitsa paradaiso wauzimu wa Mboni zamakono za Yehova.

7. Kodi nchiyani chimene maso a kuzindikira a otsalira sanawone 1914 isanakhale, koma kodi maso awo “akhungu” anatsegudwa?

7 Ndi kalelonse Nthaŵi za Akunja zisanathe maso a kuzindikira a Israyeli auzimu sanatseguke motere kuwona kuti vuto la dziko limene linali loyenera kuulika mu 1914 likatha otsalira a iwo ali chikhalirebe pano padziko lapansi. Ndiponso iwo sanawone kuti iwo ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” akayanjidwa ndi mwaŵi wa kupereka umboni wa padziko lonse lapansi wa kukhazikitsidwa kwa Ufumu Waumesiya wa Mulungu. Chotero zinachitika kuti mu 1919 maso akhungu a otsalira anatsegudwa, ndipo ha ndimasomphenya aakulu chotani nanga a mtsogolo pafupi amene maso otsegudwawo anawona!

8. Kodi nchiyambukiro chotani chimene misonkhano iŵiri pa Cedar Point, Ohio, inakhala nacho pamakutu ndi malirime auzimu a otsalira obwezeretsedwa?

8 Pamisonkhano yawo pa Cedar Point, Ohio, mu 1919 ndi 1922, iwo analandira chidziŵitso cha ntchito imene inali patsogolo. Iwo analumphira pantchito imene inali pamaso pawo. Makutu awo auzimu anatsegudwa kuti amve uthenga wochititsa chidwi wa Ufumu wa Mulungu ndi kufunika kwa kuulengeza. Mofanana ndi nswala, iwo analumpha kutumikira monga onyamula umboni wa Ufumu wopemphereredwa kwanthaŵi yaitali. Malirime awo amene kufikira panthaŵiyo anali osalankhula, anafuula ndi chimwemwe ponena za Ufumu Waumesiya wolamulira m’miyamba.—Chivumbulutso 14:1-6.

9. Mwauzimu, kodi ndimotani mmene madzi anatumphukira m’chipululu?

9 Inde, kunali ngati kuti madzi anatumphuka m’malo auzimu amene poyamba anali gwaa ndi apululu, kotero kuti tsopano kanthu kalikonse kanawonekera kukhala kobiriŵira ndi kophukira bwino—kokonzekera kukhala kobalitsa koposa. Mposadabwitsa kuti anthu obwezeretsedwa a Yehova anasangalala kwambiri namva ali olimbikitsidwa mofanana ndi nswala imene imakwera mwamphamvu ndi kutumphatumpha m’mapiri! Ndithudi, madzi a chowonadi a Ufumu wa Mulungu, wokhazikitsidwa m’manja a Yesu Kristu mu 1914, anayenda mosefukira kwambiri, akumachititsa kutsitsimulidwa kwakukulu.—Yesaya 44:1-4.

“Khwalala” Lopatulika

10, 11. (a) Kodi masinthidwe otsitsimula amenewa anatanthauzanji? (b) Kodi ndikudzera njira iti imene otsalira amayenda popita ku paradaiso wawo wauzimu, ndipo kodi ndimotani mmene Yesaya 35:8, 9 amailongosolera?

10 Kodi zapamwambapazi zikusonyezanji? Ichi: Choyamba otsalira ndipo pambuyo pake “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” atuluka m’Babulo Wamkulu ndipo apangidwa kukhala Mboni za Ufumu wa Mulungu. Koma kodi iwo adzabwerera ndi njira iti kuchiyanjo cha Mulungu ndi kuloŵetsedwa m’paradaiso wauzimu ameneyo? Kunali kudzakhala ngati kuti njira yaikulu, yotakata inaŵatsegukira kulola makamu a Aisrayeli odzala ndi mzimu waupainiya kuyenda mogwirizana pamodzi kumka kudziko lawo lopatsidwa ndi Mulungu. Ulosi wothutsa mtima wa Yesaya umasonyeza zimenezi:

11 “Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; audyo sadzapita mmenemo; koma iye adzakhala nawo oyenda m’njira, ngakhale opusa, sadzasokera mmenemo. Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale chirombo cholusa sichidzapondapo.”—Yesaya 35:8, 9.

12. Kodi kutha kwa Nkhondo Yadziko I mwa iko kokha kunatsegula “khwalala” la otsalira, ndipo nchiyani chimene chinachitika patsiku lachinayi la chaka cha 1919?

12 Kutha kwa Nkhondo Yadziko I sikunatsegule mwa maiko kokha “khwalala” lamakono. Asanu ndi atatu a ogwira ntchito pamalikulu a Watch Tower Society anali chikhalirebe m’ndende ndipo ntchito yaumboni inatsika mwapadera. Pa January 4, 1919, pamsonkhano wa chaka ndi chaka wa Watch Tower Society mu Pittsburgh, Pennsylvania, J. F. Rutherford, prezidenti wa Sosaite, anavoteredwanso pamalo ake antchito, mosasamala kanthu za kumangidwa kwake, kwenikweni iye anali mtumiki wopanda liwongo wa Mulungu Wam’mwambamwamba.

13, 14. Kodi ndizochitika zotani mu 1919 zimene zinasonyeza kuti khwalala lophiphiritsira linali litatsegukira otsalira, ndipo ndani amene anayenda pa “khwalala” limenelo?

13 Pa March 25, 1919, iye ndi andende anzake asanu ndi aŵiri anamasulidwa ndipo pambuyo pake anapezedwa opanda mlandu kotheratu. Nsanja ya Olonda Yachingelezi ya September 15, 1919, tsamba 283, inali ndi uthenga wolimbikitsa kuyambira pa October 1, 1919, maofesi a Sosaite akasamutsidwa kuchokera ku Pittsburgh kubwerera ku Beteli ya Brooklyn pa 124 Columbia Heights. Pamenepo, kuyambira kope la December 15, 1919, Nsanja ya Olonda, magazine otulutsidwa kaŵiri pamwezi ameneŵa analengezedwa kuti kachiŵirinso akufalitsidwira ku Brooklyn, New York.

14 Chotero kunachitika kuti mu 1919 khwalala lophiphiritsira linatsegukira atumiki osangalala a Mulungu. Awo amene anafuna kukhala opatulika m’maso mwa Yehova ndiwo amene anayenda pa “khwalala,” “Njira Yopatulika.” Aliyense amene analibe cholinga chabwino, chisonkhezero choyenera, sanapatukire pa “Khwalala Lopatulika” lophiphiritsira limenelo ndi kufikira kubwezeretsedwera ku chiyanjo chaumulungu.

15. Kodi nchiyani chimene chimapereka umboni wowoneka wakuti “khamu lalikulu” laloŵa pakhwalala lophiphiritsira?

15 Pa June 1, 1935, pamsonkhano m’Washington, D.C., 840 a “khamu lalikulu” anabatizidwa m’madzi, akumapereka umboni wowoneka wakuti iwo anali atayamba kuloŵa pa “khwalala.” Tsopano, mamiliyoni owonjezereka awo aloŵa pakhwalala limenelo, akumagwirizana ndi chiŵerengero chomachepachepa cha otsalira odzozedwa. Mwamtendere ndi mu unansi wosangalatsa, iwo tsopano akuyendera limodzi pa “khwalala,” ali otsimikiza kuti, mwachithandizo cha Mulungu Wamphamvuyonse wakumwamba, palibe chimene chidzaswa chigwirizano chawo.

16. M’kulankhula kophiphiritsira, kodi ndimotani mmene kuliri kuti m’khwalala limeneli mulibe mkango kapena chirombo china cholusa?

16 M’kulankhula kophiphiritsira, palibe mkango kapena chirombo china chirichonse cholusa chimene chinali kudzapezeka m’khwalala limeneli. Ndiko kuti, panalibe chirichonse chimene chikakhala choletsa kapena chothupsa otsalira odzozedwa ndi “khamu lalikulu.” Molimba mtima iwo anatenga njira yopita ku Ziyoni imene Mpulumutsi wawo, Koresi Wamkulu, tsopano anawatsegulira.

17. (a) Ngakhale kuli kwakuti tiri mkati mwenimweni mwa “mapeto a dongosolo la zinthu,” kodi “khwalala” likali chitsegukirebe? (b) Kodi ndani amene akuloŵa pa “Njira Yopatulika,” ndipo kodi iwo atero motani?

17 Lerolino, ngakhale kuli kwakuti taloŵa kwambiri mu “mapeto a dongosolo la zinthu,” “khwalala” loperekedwa ndi Mulungu likali chitsegukirebe. Makamu a anthu oyamikira akuchitapo kanthu pa chidziŵitso chakuti Babulo Wamkulu wagwa Koresi Wamkulu, Yesu Kristu asanamuukire. Ndipo akuthaŵamo, kuloŵa panjira yomka ku paradaiso wauzimu, “Njira ya Opatulika.”—Yeremiya 50:8.

18. Kodi ndimotani mmene vesi lomalizira la Yesaya 35 limalongosolera mkhalidwe wamakono wa mboni zokhulupirika za Yehova, ndipo kodi zithokozo za kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu zimapita kwayani?

18 Iwo akupeza chisangalalo ndi chikondwerero chosaneneka monga momwe vesi lomalizira la Yesaya chaputala 35 likunenera kuti: “Ndipo owomboledwa a Yehova adzabwera nadzafika ku Ziyoni ali kuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pamitu yawo; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.” Chisoni chawo ndi kubuula zochititsidwa ndi kusakhala kwawo ogiwirizana ndi Yehova Mulungu zinachoka chiyambire 1919. Ndipo chisoni ndi kubuula sizinabwerere kwa mboni zokhulupirika ndi zosangalala za Yehova. Ayamikike Mulungu amene amalankhula chowonadi, Yehova, amene wakwaniritsa ulosi umenewo wa ulemerero wa Yesaya chaputala 35 mwanjira yoyamikirika motere!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena