Kodi Nkupeŵeranji Kulambira Mafano?
“Tiana, dzisungireni nokha kupeŵa mafano.”—1 YOHANE 5:21.
1. Kodi nchifukwa ninji kulambira Yehova sikumaphatikizapo kulambira mafano?
YEHOVA sali fano lachitsulo, lachikuni, kapena lamwala. Iye sangakhale m’kachisi wapadziko lapansi. Popeza kuti iye ndiye Mzimu wamphamvuyonse, wosakhoza kuwoneka kwa anthu, nkosatheka kupanga chifaniziro chake. Chifukwa chake, kulambira koyera kwa Yehova kuyenera kukhala kopandiratu kulambira mafano.—Eksodo 33:20; Machitidwe 17:24; 2 Akorinto 3:17.
2. Kodi ndimafunso otani amene tiyenera kuwalingalira?
2 Ngati ndinu wolambira wa Yehova, pamenepo, mungafunse kuti, ‘Kodi kulambira mafano nchiyani? Kodi ndimotani mmene atumiki a Yehova anakupeŵera m’nthaŵi zakale? Ndipo kodi nkupeŵeranji kulambira mafano lerolino?’
Chimene Kulambira Mafano Kuli
3, 4. Kodi kulambira mafano kungalongosoledwe motani?
3 Kaŵirikaŵiri, kulambira mafano kumaloŵetsamo mwambo kapena dzoma. Kulambira mafano ndiko kupembedza, kukonda, kulemekeza, kapena kugwadira fano. Ndipo kodi fano nchiyani? Ndilo chifaniziro, choimira cha chinthu china, kapena chizindikiro, chimene munthu amadziperekako. Kaŵirikaŵiri, kulambira mafano kumachitidwa kulinga kwa mphamvu yapamwamba yeniyeni kapena yoyerekezeredwa yokhulupiriridwa kukhalapo yamoyo (munthu, nyama, kapena gulu). Koma kulambira mafano kungachitidwenso kulinga kwa zinthu zopanda moyo (mphamvu kapena zinthu za m’chilengedwe.)
4 M’Malemba, mawu Achihebri onena za mafano kaŵirikaŵiri amasonyeza kupanda pake, kapena ali mawu oluluza. Pakati pa mawuwo pali omasuliridwa monga “fano losema kapena lozokota” (kwenikweni, chinthu chosemedwa); “fano, chifaniziro, kapena fano lofulidwa” (chinthu chofulidwa kapena chosungunulidwa); “fano lonyansa”, “fano lopanda pake” (kwenikweni, lachabechabe); ndi “fano loipa.” Liwu Lachigiriki eiʹdo·lon limamasuliridwa “fano.”
5. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti sizifaniziro zonse zimene ziri mafano?
5 Sikuti zifaniziro zonse ziri mafano. Mulungu iye mwiniyo anauza Aisrayeli kupanga akerubi agolidi aŵiri oikidwa palikasa lachipangano ndi kusokera zithunzithunzi za zolengedwa zauzimu zoterozo pansalu zabafuta khumi zophimbira mkati mwa chihema chokumanira ndi pansalu yotchinga yolekanitsa Malo Opatulika ndi Opatulikitsa. (Eksodo 25:1, 18; 26:1, 31-33) Ansembe otumikira pakachisi, ndiwo okha anawona zithunzithunzi zimenezi zimene kwakukulukulu zinaimira akerubi akumwamba. (Yerekezerani ndi Ahebri 9:24, 25.) Nkowonekeratu kuti zithunzithunzi za pachihema za akerubi sizinapembedzedwe, popeza kuti angelo olungama enieniwo sanalole kulambiridwa.—Akolose 2:18; Chivumbulutso 19:10; 22:8, 9.
Lingaliro la Yehova la Kulambira Mafano
6. Kodi Yehova amakulingalira motani kulambira mafano?
6 Atumiki a Yehova amapeŵa kulambira mafano chifukwa chakuti iye amatsutsa machitachita alionse akulambira mafano. Mulungu analamula Aisrayeli kusapanga zifaniziro zakuzipembedza ndi kuzilambira. Pa Malamulo Khumi pali mawuŵa: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chirichonse cha zinthu za m’thambo lakumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate awo, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene akudana ndi ine; ndi kuwachitira chifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi ine, nasunga malamulo anga.”—Eksodo 20:4-6.
7. Kodi nchifukwa ninji Yehova amatsutsa kulambira mafano kulikonse?
7 Kodi nchifukwa ninji Yehova amatsutsa kulambira mafano kulikonse? Kwakukulukulu nchifukwa chakuti iye amafuna kudzipereka kotheratu, monga momwe lamulo lachiŵiri la Malamulo Khumi lasonyezera pamwambapo. Ndiponso, iye anati kupyolera mwa mneneri wake Yesaya: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.” (Yesaya 42:8) Panthaŵi ina, kulambira mafano kunatchera Aisrayeli msampha kufikira pamlingo “wakupereka ana awo aamuna ndi aakazi nsembe kwa ziŵanda.” (Salmo 106:36, 37) Olambira mafano samangokana kuti Yehova ali Mulungu wowona koma amatumikiranso zifuno za Mdani wake wamkulu, Satana, limodzi ndi ziŵanda.
Kukhulupirika Pachiyeso
8. Kodi nchiyeso chotani chimene Ahebri atatuwo Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anayang’anizana nacho?
8 Kukhulupirika kwathu kwa Yehova kumatithandizanso kupeŵa kulambira mafano. Izi zikusonyezedwa ndi chochitika cholembedwa pa Danieli chaputala 3. Kuti atsegulire mwalamulo kulambiridwa kwa fano lalikulu la golidi limene iye analiimika, Nebukadinezara mfumu ya Babulo anasonkhanitsa nduna za muufumu wake. Chiitano chake chinaphatikizapo Sadrake, Mesake, ndi Abedinego—nduna Zachihebri zitatu zoyang’anira kayendetsedwe kazinthu m’chigawocho cha m’Babulo. Onse opezekapo analamulidwa kugwadira fanolo pakuwombedwa kwa zipangizo zoimbira. Kumeneku kunali kuyesa kwa mulungu weniweni wa Babulo, Satana, kuti achititse Ahebri atatuwo kugwadira fanolo loimira Ufumu wa Babulo. Tayerekezerani kukhala mulipo pachochitikacho.
9, 10. (a) Kodi Ahebri atatuwo anatenga kaimidwe kotani, ndipo anafupidwa motani? (b) Kodi nchilimbikitso chotani chimene Mboni za Yehova zingapeze m’kachitidwe ka Ahebri atatuwo?
9 Tawonani! Ahebri atatuwo ali chiriri. Iwo akukumbukira lamulo la Mulungu loletsa kutumikira mafano kapena zifaniziro zosema. Nebukadinezara akuwaikira chosankha—kugwada kapena kufa! Koma mokhulupirika kwa Yehova, iwo akuti: “Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m’ng’anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m’dzanja lanu, mfumu. Koma akapanda kutero, dziŵani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.”—Danieli 3:16-18.
10 Atumiki a Mulungu okhulupirika ameneŵa akuponyedwa m’ng’anjo yamotoyo yosonkhezedwa moŵirikiza. Atazizwa powona anthu anayi akuyendayenda m’ng’anjomo, Nebukadinezara akuitana Ahebri atatuwo kuti atulukemo, ndipo anatuluka opanda kuvulala. Itawona zimenezo, mfumuyo ikufuula niti: “Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mawu a ine mfumu, napereka matupi awo kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu wawowawo. . . . Palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.” (Danieli 3:28, 29) Kusunga umphumphu kwa Ahebri atatuwo kumapereka chilimbikitso kwa Mboni za Yehova zamakono kukhala zokhulupirika kwa Mulungu, kusunga uchete kulinga ku dziko, ndi kupeŵa kulambira mafano.—Yohane 17:16.
Mafano Atsutsidwa m’Bwalo Lamilandu
11, 12. (a) Kodi ndinkhani yotani yoloŵetsamo Yehova ndi milungu yamafano imene Yesaya analemba? (b) Kodi milungu ya mitundu inachita motani pamene inatokosedwa ndi Yehova?
11 Chifukwa china chopeŵera kulambira mafano nchakuti kupembedza mafano nkopanda pake. Ngakhale kuti mafano ena opangidwa ndi anthu angawonekere kukhala ngati amoyo—kaŵirikaŵiri okhala ndi kamwa, maso, ndi makutu—iwo samalankhula, kuwona, kapena kumva ndipo satha kuchitira owalambira kalikonse. (Salmo 135:15-18) Izi zinasonyezedwa m’zaka za zana la chisanu ndi chitatu B.C.E., pamene mneneri wa Mulungu analemba pa Yesaya 43:8-28 nkhani imene iri, kwenikweni, mlandu wachiweruzo wapabwalo lamilandu pakati pa Yehova ndi milungu yamafano. Mumlanduwo, anthu a Mulungu Aisrayeli anali kumbali ina, ndipo mitundu yadziko kumbali inayo. Yehova anatokosa milungu yonama ya mitunduyo kunena “zidapitazo,” kulosera molondola. Palibe ndi mmodzi yemwe anakhoza kutero. Potembenukira kwa anthu ake, Yehova anati: “Inu ndinu Mboni zanga. . . . ndipo ine ndine Mulungu.” Mitunduyo sinathe kupereka umboni wotsimikizira kuti milungu yawo inakhalako Yehova asanatero kapena kuti iyo inakhoza kulosera. Koma Yehova ananeneratu za kuwonongedwa kwa Babulo ndi kumasulidwa kwa anthu ake okhala muukapolowo.
12 Ndiponso, atumiki a Yehova omasulidwawo akanena, monga momwe kwalembedwera pa Yesaya 44:1-8 kuti, iwo ‘ali a Yehova.’ Iye mwiniyo anati: “Ine ndiri woyamba ndi womaliza, ndi popanda ine palibenso Mulungu.” Palibe mawu otsutsa alionse ochokera kwa milungu yamafano. “Inu ndinu Mboni zanga,” Yehova anateronso kwa anthu ake, nawonjezera kuti: “Kodi popanda ine aliponso Mulungu? Iyayi, palibe thanthwe.’
13. Kodi kulambira mafano kumavumbulanji ponena za munthu woilambira?
13 Timapeŵanso kulambira mafano chifukwa kudziloŵetsamo kumasonyeza kupanda nzeru. Ndi mbali ya mtengo umene ausankha, wolambira mafano amapanga mulungu womlambira, ndipo ndi mbali inayo akolezera moto wophikira chakudya chake. (Yesaya 44:9-17) Nkupusa chotani nanga! Munthu amene amapanga milungu yamafano ndi kuilambira amadzichititsanso manyazi chifukwa chakuti amalephera kupereka umboni wokhutiritsa wotsimikizira umulungu wa mafanowo. Koma Umulungu wa Yehova ngwosakaikirika, pakuti iye sananene chabe za kumasulidwa kwa anthu ake ku Babulo komanso anakukwaniritsa. Yerusalemu anakhalidwanso ndi anthu, mizinda ya Yuda inamangidwanso, ndipo “nyanja yakuya” ya Babulo—Mtsinje wa Firate—inaphwa ndi kusakhalanso magwero a chitetezero. (Yesaya 44:18-27) Monga momwe ananeneranso Mulungu, Koresi Mperesiyayo anagonjetsa Babulo.—Yesaya 44:28–45:6.
14. M’Bwalo Lamilandu Lachilengedwechonse, kodi nchiyani chimene chidzatsimikiziridwa kwanthaŵi yonse?
14 Milungu yamafanoyo inatsutsidwa pamlandu wachiweruzo umenewo wonena za umulungu. Ndipo zomwe zinagwera Babulo nzotsimikizirika kugweranso mnzake wamakono, Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Iye ndi milungu yake yonse, chuma chake chachipembedzo chamtengo wapatali, ndi mafano ake posachedwapa zidzawonongedwa kotheratu. (Chivumbulutso 17:12–18:8) Panthaŵiyo, m’Bwalo Lamilandu Lachilengedwechonse, kudzatsimikiziridwa kwanthaŵi yonse kuti Yehova yekha ndiye Mulungu wamoyo ndi wowona ndi kuti amakwaniritsa Mawu ake aulosi.
Nsembe kwa Ziŵanda
15. Kodi nchiyani chimene chinasonyezedwa ndi mzimu woyera ndi bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba ponena za anthu a Yehova ndi kulambira mafano?
15 Anthu a Yehova amapeŵanso kulambira mafano chifukwa chakuti amatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu ndi gulu lake. Bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba la atumiki a Yehova linauza Akristu anzawo kuti: “Chinakomera mzimu woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa china chachikulu choposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe zamafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungira pazimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.”—Machitidwe 15:28, 29.
16. M’mawu anu, kodi mungafotokoze motani zimene Paulo ananena pa zinthu zoperekedwa nsembe ku mafano?
16 Chifukwa china chopeŵera kulambira mafano ndicho kupeŵa kukhulupirira ziŵanda. Ponena za Mgonero wa Ambuye, mtumwi Paulo anauza Akristu anzake aku Korinto kuti: “Thaŵani kupembedza mafano. . . . Chikho chadalitso chimene tidalitsa, sichiri chiyanjo cha mwazi wa Kristu kodi? Mkate umene tinyema, suli chiyanjano cha thupi la Kristu kodi? Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako ku mkate umodzi. Tapenyani Israyeli monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe? Ndinena chiyani tsono? kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chiri kanthu? Kapena kuti fano liri kanthu kodi? Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziŵanda; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziŵanda. Simungathe kumwera chikho cha [Yehova, NW], ndi chikho cha ziŵanda; Simungathe kulandirako ku gome la [Yehova, NW], ndi ku gome la ziŵanda. Kapena kodi tichititsa nsanje [Yehova, NW]? Kodi mphamvu zathu ziposa iye?”
17. M’zaka za zana loyamba C.E., kodi ndi m’mikhalidwe yotani imene Mkristu anakhoza kudya nyama yoperekedwa nsembe ku mafano, ndipo chifukwa ninji?
17 Mbali ya nyamayo inaperekedwa nsembe kwa fano, mbali ina inapita kwa ansembe, ndipo wolambira fanoyo anatenga mbali ina yokachitira phwando. Komabe, mbali ya nyamayo ikagulitsidwa pamsika. Sikunali bwino kwa Mkristu kupita ku kachisi wa fano kukadya nyama ngakhale kuti sakaidya monga mbali ya dzoma, pakuti zimenezi zikakhumudwitsa ena kapena kumloŵetsa m’kulambira konyenga. (1 Akorinto 8:1-13; Chivumbulutso 2:12, 14, 18, 20) Kupereka nsembe nyama kwa mafano sikunasinthe nyamayo, chotero Mkristu akakhoza kuigula pamsika. Ndipo iye sanafunikire kufunsa za kumene kunachokera nyama yodyedwa panyumba. Koma ngati wina ananena kuti “inaperekedwa nsembe,” iye sakaidya, kupeŵa kukhumudwitsa aliyense.—1 Akorinto 10:25-29.
18. Kodi ndimotani mmene awo odya chinthu choperekedwa nsembe kumafano akayanjanira ndi ziŵanda?
18 Kaŵirikaŵiri kunalingaliridwa kuti pambuyo pa dzoma lakupereka nsembe, mulunguyo anali kukhala m’nyamayo ndipo analoŵa m’thupi la oidyawo paphwando la olambira. Monga momwe anthu odyera pamodzi anapalana chibwenzi pakati pawo, odya nyama zoperekedwa nsembe analinso ogwirizana paguŵa lansembe ndipo anayanjana ndi mulungu wachiŵanda woimiridwa ndi fanolo. Kupyolera m’kulambira mafano koteroko, ziŵanda zinatsekereza anthu kulambira Mulungu yekha wowona. (Yeremiya 10:1-15) Mposadabwitsa kuti anthu a Yehova anafunikira kusala zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano! Kukhulupirika kwa Mulungu, kulandira chitsogozo cha mzimu wake woyera ndi gulu lake, ndi kutsimikiza mtima kupeŵa kudziloŵetsa kulikonse m’kukhulupirira ziŵanda kumakhalanso chisonkhezero champhamvu chopeŵera kulambira mafano lerolino.
Nchifukwa Ninji Pali Kufunika Kwakupeŵa?
19. Kodi ndimtundu wotani wakulambira mafano umene unali m’Efeso wakale?
19 Akristu amapeŵa mwakhama kulambira mafano chifukwa chakuti kuli m’mipangidwe yambiri, ndipo ngakhale mchitidwe umodzi wokha wakulambira mafano ukhoza kugonjetsa chikhulupiriro chawo. Mtumwi Yohane anauza okhulupirira anzake kuti: “Dzisungireni nokha kupeŵa mafano.” (1 Yohane 5:21) Uphungu umenewu unafunikira chifukwa chakuti anazingidwa ndi mipangidwe yambiri ya kulambira mafano. Yohane analemba ali ku Efeso, mzinda womwerekera m’machitachita amatsenga ndi nthano za milungu yonama. Efeso anali ndi chimodzi cha zozizwitsa zisanu ndi ziŵiri za dziko—kachisi wa Artemi, malo othaŵirako apandu ndi phata la madzoma achisembwere. Wanthanthi Heracleitus wa ku Efeso anafanizira njira yamdima yofikira ku guwa lansembe la kachisiyo ndi mdima wa kululuzika, ndipo analingalira makhalidwe apakachisi kukhala oipirapo kuposa azinyama. Chifukwa chake, Akristu a ku Efeso anafunikira kuchirimika motsutsana ndi kukhulupirira ziŵanda, chisembwere, ndi kulambira mafano.
20. Kodi nchifukwa ninji kunali kofunika kupeŵa ngakhale kulambira mafano kochepetsetsa?
20 Akristu amafunikira kukhala otsimikiza mtima mwamphamvu kuti apeŵe ngakhale kulambira mafano kochepetsetsa chifukwa chakuti mchitidwe umodzi wokha wakulambira Mdyerekezi ukachirikiza chitokoso chake chakuti anthu sakakhalabe okhulupirika kwa Mulungu pachiyeso. (Yobu 1:8-12) Posonyeza Yesu “maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo,” Satana anati: “Zonse ndikupatsani inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.” Kukana kwa Kristu kunachirikiza mbali ya Yehova pankhani ya uchifumu wa chilengedwe chonse ndipo kunatsimikizira Mdyerekeziyo kukhala wabodza.—Mateyu 4:8-11; Miyambo 27:11.
21. Ponena za wolamulira wa Roma, kodi Akristu okhulupirika anakana kuchitanji?
21 Ngakhale otsatira oyambirira a Yesu sakachita mchitidwe wakulambira wochirikiza mbali ya Satana m’nkhaniyo. Ngakhale kuti anasonyeza ulemu woyenerera kwa “maulamuliro aakulu,” iwo sakapsereza zonunkhira kulemekeza wolamulira wa Roma, ngakhale ngati kutero kukawataitsa miyoyo yawo. (Aroma 13:1-7) Ponena za zimenezi, Daniel P. Mannix analemba kuti: “Ndi ochepa kwambiri a Akristu amene anagonja, ngakhale kuti kaŵirikaŵiri, guwa lansembe lokhala ndi moto woyaka linalipo m’bwalomo loti aligwiritsire ntchito. Zokha zimene mkaidi anafunikira kuchita zinali kumwaza mbali yaing’ono ya zonunkhirazo pa motowo ndipo anapatsidwa Chikalata cha Nsembe namasulidwa. Anamfotokozeranso bwino lomwe kuti iye sanali kulambira wolamulirayo; anali kungovomereza mkhalidwe waumulungu wa wolamulirayo monga mutu wa boma la Roma. Chikhalirechobe, pafupifupi palibe Akristu amene anayesa kufunafuna mpata wakuwonjoka.” (Those About to Die, tsamba 137) Ngati inuyo muyesedwa mofananamo, kodi mukatsutsa kotheratu kulambira mafano kulikonse?
Kodi Mudzapeŵa Kulambira Mafano?
22, 23. Kodi nchifukwa ninji muyenera kupeŵa kulambira mafano?
22 Momveka bwino, Akristu ayenera kupeŵa mipangidwe iriyonse yakulambira mafano. Yehova amafuna kudzipereka kotheratu. Ahebri okhulupirika atatuwo anapereka chitsanzo chabwino mwakukana kulambira fano lalikululo loimikidwa ndi mfumu Nebukadinezara. M’nkhani ya pabwalo lamilandu lachilengedwe chonse yolembedwa ndi mneneri Yesaya, Yehova yekha ndiye anasonyezedwa kukhala Mulungu wowona ndi wamoyo. Mboni zake Zachikristu zakalezo zinafunikira kupeŵa zinthu zoperekedwa nsembe ku mafano. Okhulupirika ambiri pakati pawo sanagonje ku chitsenderezo chakuchita ngakhale mchitidwe umodzi wokha wakulambira mafano umene ukatanthauza kukana Yehova.
23 Pamenepo, kodi inuyo panokha mukupeŵa kulambira mafano? Kodi mumampatsa Mulungu kudzipereka kotheratu? Kodi mumachirikiza uchifumu wa Yehova ndi kumkweza monga Mulungu wowona ndi wamoyo? Ngati nditero, muyenera kukhala wotsimikiza mtima kupitiriza kuima nji motsutsana ndi machitachita akulambira mafano. Koma kodi ndimfundo Zamalemba zina ziti zimene zingakuthandizeni kupeŵa kulambira mafano kwa mtundu uliwonse?
Kodi Malingaliro Anu Ngotani?
◻ Kodi kulambira mafano nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova amatsutsa kulambira mafano kulikonse?
◻ Kodi ndikaimidwe kotani kamene Ahebri atatuwo anakatenga ponena za kulambira mafano?
◻ Kodi amene anali kudya zinthu zoperekedwa nsembe ku mafano anayanjana motani ndi ziŵanda?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kulambira mafano?
[Chithunzi patsamba 23]
Ngakhale kuti miyoyo yawo inawopsezedwa, Ahebri atatuwo sanadziloŵetse m’kulambira mafano