Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 6/8 tsamba 11
  • Kodi Akristu Ayenera Kutchova Juga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akristu Ayenera Kutchova Juga?
  • Galamukani!—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limaletsa Kutchova Juga?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?
    Galamukani!—1994
  • Peŵani Msampha wa Kutchova Njuga
    Galamukani!—2002
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 6/8 tsamba 11

Kodi Akristu Ayenera Kutchova Juga?

KODI Mkristu ayenera kutchova juga kuti apeze kanthu kena kamene sanakagwirire ntchito? Ayi, pakuti Mawu a Mulungu amamlimbikitsa kugwira ntchito kuti adzidyetse iye mwini ndi banja lake kumati: ‘Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso. . . . Agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha.’—2 Atesalonika 3:10, 12.

Katswiri wa zakakhalidwe ka anthu anatcha lotale kukhlala ‘njira imene anthu ambiri osauka amalemeretsa nayo anthu oŵerengeka,’ ndipo zimenezo zimakhaladi tero ponena za kutchova juga kwamtundu uliwonse. Kodi Mkristu angafune kudzilemeretsa mwakudyerera amene sakhoza kutero? Akristu ayenera ‘kukonda anzawo monga adzikonda okha.’ (Marko 12:31) Koma kutchova juga kumakulitsa mzimu wadyera mmalo mwa chikondi, kusadera nkhaŵa mmalo mwa chifundo.

Kaŵirikaŵiri kutchova juga kumasonkhezeredwa ndi chisiriro—umbombo—mzimu wosafunika mwa Akristu. Pa Aroma 7:7, Paulo anati: “Usasirire.” Liwu la “kusirira” limatanthauza “kulakalaka, kukhumbira.” Kodi zimenezo sizikusonyeza chikhumbo chachikulu cha wotchova juga chakupambana ndalama za anansi ake? Chikhumbo chotero chiri chosayenerana ndi mkhalidwe Wachikristu wa kugaŵana ndi kupatsa.

Baibulo limati: ‘Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, . . . anadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.’ (1 Timoteo 6:10) Zimenezo zimafotokoza bwino vuto la wotchova juga womwerekera, wokhala muukapolo ku chizoloŵezi chimene chimampyoza moŵaŵa, nthaŵi ndi nthaŵi.

Yesu anati anthu amazindikiridwa ndi “zipatso zawo.” (Mateyu 7:20) Pambali pa tsoka logwera otchova juga omwerekera ndi mabanja awo, kutchova juga kwachititsa kusawona mtima ndi upandu kwa zaka zambiri. The New Encyclopædia Britannica imanena kuti: “Kuipa kochuluka kochititsidwa ndi kutchova juga kuli kaamba ka kusawona mtima kwa okuchirikiza.” Upandu umachititsidwa ndi zonse ziŵiri kutchova juga kwalamulo ndi kosakhala kwalamulo. Kodi Mkristu angakonde kuchirikiza mchitidwe umenewu, mwachindunji kapena mwanjira zina?

Monga momwe nkhani yachiŵiri ya mpambo uno yafotokozera, kutchova juga kaŵirikaŵiri kumaphatikizapo kufunafuna manambala amwaŵi kozikidwa pamalaulo, masiku amwaŵi, kapena nyengo zamwaŵi. Mulungu Wamwaŵi walambiridwa kwa zaka mazana ambiri ndi otchova juga ofunitsitsa kupeza chiyanjo chake. Aroma ankamutcha Fortuna, ndipo mkupita kwa nthaŵi akachisi omlambirira okwanira 26 anamangidwa mumzinda wa Roma.

Mneneri Yesaya anatchula mulungu wofanana, wotchedwa gadh, wolambiridwa ndi Aisrayeli ampatuko. Analemba kuti: ‘Inu amene mwasiya Yehova, . . . okonzera mulungu [Wamwaŵi (m’Chihebri gadh), NW] gome.’ (Yesaya 65:11) Patsiku lothera la chaka, unali mwambo kukonzera mulungu Wamwaŵi gome lodzala zakudya zosiyanasiyana. Mwanjira imeneyo anthu amakedzana anayembekezera kukhala ndi mwaŵi m’chaka chotsatira.

Mulungu sanavomereze amene mwaumbuli anakhulupirira kuti gadh, kapena mulungu Wamwaŵi, akathetsa mavuto awo. Kudalira mwaŵi kunafanizidwa ndi kusiya Mulungu wowona, Yehova. Mmalo mwakudzipatulira kwa Mwaŵi wongoyerekezera, Akristu ayenera kukhulupirira mwa Mulungu wowona, Yehova, Amene amatilonjeza chuma chamtengo wapatali ndithu, Amene sadzatigwiritsa mwala.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena