Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 4/8 tsamba 24-27
  • Nyalugwe—Mphaka Wochita Zinthu Mwakachetechete

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyalugwe—Mphaka Wochita Zinthu Mwakachetechete
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mphaka Woyenda Yekha
  • Anakubala a Anyalugwe
  • Nyalugwe—Kodi Potsirizira Adzakhala pa Mtendere?
  • Kodi Munthu ndi Chilombo Angakhale Pamtendere?
    Galamukani!—1991
  • Kukumana kwa Usiku ku Tanzania
    Galamukani!—1995
  • Zopinga Mtendere Pakati pa Munthu ndi Chilombo
    Galamukani!—1991
  • Maulendo Anga Owona Zinyama mu Africa—Analipo kaamba ka Ine—Kodi Adzakhalapo kaamba ka Ana Anga?
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 4/8 tsamba 24-27

Nyalugwe—Mphaka Wochita Zinthu Mwakachetechete

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU KENYA

DZUŴA linali kuloŵa. Tsiku lonselo tinali kuona ndi kujambula nyama zakuthengo zochititsa chidwi mu Masai Mara Game Reserve ya Kenya. Tisanayambe kupuma usikuwo pakampu, tinali kuyembekezera kuona chinthu chinanso chokondweretsa kwambiri. Zimenezi zinayambika pamene wogwira ntchito wina wa pamalopo anayenda modzikwakwaza kudutsa Talek River pa mlatho wazingwe, atapachika papheŵa lake nyama ya thako la mbuzi. Iye anamangirira nyamayo pamphanda ina m’mwamba mu mtengo wa nsangu.

Pamene maonekedwe achizimezime a malo otentha anali kuzimiririka mumdima, nyalugwe wina wamkulu anakwera mofulumira mu mtengowo mwakachetechete nayamba kumwetula nyamayo. Anaunikiridwa ndi magetsi a pansanja yoonerera. Komabe, pokomeredwa ndi chakudya chake, nyalugweyo anangotinyalanyaza pamene tinali kuonerera mozizwa. Pambuyo pake tinauzidwa kuti kufika kwake pa mtengo woikidwa nyamawo kunali chizoloŵezi chake usiku uliwonse, chimene wachita kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Chotero usikuwo tinasonyezedwanso chochitikacho!

Tinazindikiradi chifukwa chake nyalugwe wafotokozedwa kukhala “mphaka wamkulu weniweni, wokongola m’maonekedwe ndi waulemerero m’mayendedwe ake.” Pokhala wolemera makilogalamu 60 kapena kuposa pamenepo, nyalugwe ali imodzi ya nyama zokhala ndi minyewa yamphamvu kwambiri, kaŵirikaŵiri akumakhala wa masentimita oposa 60 kutalika pa mapeŵa ake ndipo masentimita 200 utali kuyambira pamphuno yake kukafika kunsonga ya mchira wake. Poyang’anitsitsa maŵanga ake apadera akudawo olinganizidwa ngati maliboni pa ubweya wake womkera kuchikasu, tinakumbutsidwa za funso limene linafunsidwa ndi mneneri Yeremiya pa nthaŵi ina: “Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe maanga ake?”—Yeremiya 13:23.

Ochititsa chidwi kwambiri ndiwo maso ake oŵala mobiriŵira. Iwo ali ndi muyalo wina wapadera wa maselo—tapetum—umene umamchititsa kuona kwambiri usiku. Nyalugwe amatha kuona pa kuunika kwa mlingo wochepa kwambiri kuposa maso a munthu. Muyalo umenewu wa maselo, umene umaŵala kuseri kwa retina, umatulutsa kunyezimira pamene maso ake aunikiridwa ndi magetsi usiku.

Mukanakhala kuti munali kuona nyalugwe akupuma masana, mukanaona kuti amaŵefemuka monga ngati kuti anali pafupi kutheredwa mpweya. Komabe, kupuma kwake kofulumirako kuli mbali ya njira yodziziziritsa yogwira bwino ntchito. Mwa kuŵefemuka kwake kufikira pafupifupi nthaŵi 150 pa mphindi, nthunzi imatuluka palilime lake, m’kamwa mwake, ndi mu mphuno zake.

Pokhala amphaka aakulu okhoza kwambiri kusinthira kumalo ena, anyalugwe angapezeke m’zipululu ndi m’nkhalango; m’mapiri ndi m’zigwa za nyanja; m’maiko osiyanasiyana onga China, India, ndi Kenya. Chinkana anthu akuloŵerera m’malo ambiri a nyalugwe, asayansi akuyerekezera kuti mu Afirika ndi mu Asia mokha muli pafupifupi miliyoni imodzi. Ngakhale kuti zili choncho, kwa zaka mazana ambiri nyalugwe wazemba kuphunziridwa mwamphamvu ndi asayansi. Mwachitsanzo, nyalugwe wa ku Sinai. Ndi posachedwapa pamene anyalugwe olingaliridwa kukhala atatha kalekalewo anaonedwanso m’chipululu cha Yudeya!

Mphaka Woyenda Yekha

Kodi nyalugwe amapeŵa motani kuonedwa ndi anthu? Amachita zimenezi makamaka chifukwa chakuti ali nyama yakuthengo yosaka usiku—ndipodi ngwochenjera kwambiri ndipo amachita zinthu mwakachetechete. M’madera kumene anthu ali owopseza, nyalugwe amachita zinthu mwakachetechete kwambiri. Kokha ngati wakwiyitsidwa mpamene amathuluma ngati mkango. Akakhala mu mkhalidwe wozoloŵereka, kulira kwake sikumakhala kowopsa: kudzuma kosasirira—kofanana kwambiri ndi kamvekedwe ka sowo yodula matabwa. Malinga nkunena kwa buku lakuti Animals of East Africa, lolembedwa ndi C. T. Astley Maberly, amati “Gruu-aa! Gruu-aa! Gruu-aa! Gruu-aa!—kaŵirikaŵiri amatha ndi mamvekedwe onga a kuusa mtima.” Pokonda kuchita kwake zinthu mwakachetechete, nyalugwe amatulutsanso mawu omvekera chapansi kwambiri, amene anthu ochuluka sangamve.

Ndiponso, mosiyana ndi mkango wokonda kuyanjana ndi ina, nyalugwe sali mphaka woyanjana ndi wina. Ngakhale kuti nthaŵi zina pamaonedwa anyalugwe aŵiri ali pamodzi, iwo amasaka nyama payekhapayekha. Kuti apeŵe adani, nyalugwe amalemba malire a dera lake limene lingakhale la makilomita kuyambira pa 25 kufikira ku 65 monsemonse. Amatulutsa madzi apadera m’ma gland kupangira malire dera lake. Fungo la madziwo lingadziŵitse anyalugwe ena ponena za kuti kaya ndi mkazi kapena mwamuna, msinkhu wake, mphamvu yake ya kugonana, ndipo mwinamwake kudziŵikitsa “mwini malo.”

Nyalugwe amaŵendera nyama posaka. M’nthaŵi za Baibulo iye anadziŵika kukhala wobisalira nyama pafupi ndi mizinda, wokonzekera kumbwandira zifuyo mofulumira kwambiri. (Yeremiya 5:6; Hoseya 13:7; Habakuku 1:8) Kuti atetezere nyama yake ku zilombo zodya zotsalira, monga ngati afisi ndi ankhandwe, amasunga nyama yake yambiri pa mphanda ya mtengo yokhala pamwamba mamita 9 kapena 12. Koma kodi amatha bwanji kukokera m’mwamba gwape yense kapena mwana wa nyamalikiti wamtali mamita 1.5 kufikira pamwamba potero? Anyalugwe samaulula wamba chinsinsi chimenechi. Koma oonerera ofatsa amanena kuti zimenezo zimachitidwa ndi nyonga yosaneneka. Anyalugwe amakonda kudya mosathamanga, atalenjekeka panthambi za mitengo, ndipo mobisika kwambiri, mozimbaitsidwa ndi nthambi ndi masamba.

Ngati saputidwa, nyalugwe amangodzichokera ndipo amapeŵa kuyang’anizana ndi munthu. Chotero pamene kuli kwakuti anyalugwe ena atha mantha ndi anthu ndipo akhala odya anthu, ambiri samaukira anthu. Komabe, ngati wavulazidwa kapena kupanikizidwa, nyalugwe samachita mantha ndi mdani wake aliyense. “Nyalugwe wokwiya,” akulemba motero Jonathan Scott mu The Leopard’s Tale, “amapenga kowopsa, . . . moti akhoza kuukira ndi mphamvu zake zonse pa liŵiro la mphezi kuchokera pafupi.”

Anakubala a Anyalugwe

Pamenepa, mposadabwitsa kuti anyalugwe amaleranso ana awo mobisa. Misona yongobadwa chatsopano imabisidwa, kaŵirikaŵiri kuphanga, pamiyezi iŵiri yoyamba. Ngakhale kuti atate samalera nawo misonayo, nakubalayo amaumba chikondi mwa kuwadyetsa ndi kuwapukuta ndi kuwafunditsa. M’kupita kwa nthaŵi, nakubalayo angasamutsire misona yake iŵiri kapena itatuyo kumalo atsopano, akumainyamula ndi kamwa lake ngati idakali yaing’ono kwambiri kapena kuiitana kuti izimtsatira ngati ili yokulirapo.

Nakubala wa nyalugwe amayesanso kubisa misona yake kwa adani, monga ngati anyani. Koma ngati anyani aukira misona yake, iye amalimbana nawo, akumadziika pangozi kuti misona yake ithaŵire kumalo otetezereka. Iye amadziloŵetsanso mu ngozi kuti adyetse misona yakeyo. Nyalugwe amene mwachibadwa amathaŵa ena amadzera pakati pa nsambi wa njovu zolira atanyamula nyama ya ana ake anjala.

Chochititsa chidwi nchakuti, anyalugwe aang’ono samakhala ndi mzimu wa kudziimira paokha kwa nthaŵi yakutiyakuti. Misonayo imaletsedwa kuyamwa patapita pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi komano siimadziphera nyama kufikira pamene ili ndi chaka chimodzi. Yaimuna yomakulayo simakhala yoyenda yokha kufikira pa usinkhu wa pafupifupi zaka ziŵiri ndi theka. Misona yaikazi yomakulayo imapitirizabe kukhala m’dera la amawo.

Nyalugwe—Kodi Potsirizira Adzakhala pa Mtendere?

Koma misona yamanyenje imeneyo imakula nikhala zilombo zakupha. Motero kungaonekere kukhala kovuta kukhulupirira kuti mawu a mneneri Yesaya adzakwaniritsidwadi: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalungwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi.”—Yesaya 11:6.

Zoyesayesa zaposachedwapa za kufuya anyalugwe zangotheka pang’ono. Sieuwke Bisleti van der Laan ndi mwamuna wake analera misona ina pa famu yawo ya mu Afirika. Misonayo inapatsidwa “ufulu wonse” ndipo inali kudyetsedwa. Komano siinali yotheka kufuyidwa kwenikweni. Sieuwke Bisleti akulemba kuti: “Pamene nyalugwe wakula, amachita zimene akufuna. Mkango nthaŵi zonse umakukondani ndi kukumverani; nyalugwe amakuzindikirani komano amadzisankhira zochita panthaŵi ina iliyonse.”

Motero kunapezeka kuti kulola misona yaikulu kupitirizabe kuyendayenda mwaufulu pa famupo nkwangozi. Anasankha kuibwezera kuthengo. Kodi kuleredwa kwa misonayo pakati pa anthu aubwenzi kunaipusitsa? Kutalitali. Mkati mwa masiku atatu itatulutsidwa, msona wamphongo unaonedwa utakhala pafupi ndi nankhodzwe amene unapha.

Komabe, kufuya anyalugwe kotheka pang’onoko sikumatsutsa ulosi wouziridwa wa Yesaya wonena za mtendere wa pakati pa nyalugwe ndi mbuzi. Chinthu chodabwitsa chimenechi chidzachitika, osati ndi zoyesayesa za munthu, koma ndi kuchitapo kanthu kwa Mulungu. Komabe, ulamuliro wa Mulungu udzachita zambiri kuposa kungobweretsa mtendere pa nyama. “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova,” ananeneratu motero Yesaya. (Yesaya 11:1-9) Motero ngakhale anthu adzaleka khalidwe longa lanyama limene labala nkhondo ndi magaŵano. Panthaŵi imodzimodziyo, mkhalidwe wamaganizo wa anthu kulinga kunyama udzasinthanso. Nyama sizidzaphedwanso mwawamba. Ndipo anthu sadzawononga malo ake okhala kapena kuzisolotsa, chifukwa chakuti Yehova adzakhala ‘atawononga iwo akuwononga dziko.’—Chivumbulutso 11:18.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena